Yud. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu okonda za mtendere atuma amithenga kwa Holofernesi

1Tsono anthu onsewo adatuma amithenga okakamba za mtendere kwa Holofernesi.

2Iwo adamuuza kuti, “Ife ndife atumiki a Nebukadinezara, Mfumu yaikulu ija. Tikudzigwetsa chafufumimba pamaso panu. Muchite nafe monga momwe mukufunira.

3Nyumba zathu, dziko lathu lonse, minda yathu yonse ya tirigu, ziŵeto zathu zonse, pamodzi ndi makola athu omwe ndiponso mahema athu, zonse ndithu zili m'manja mwanu. Muchite nazo monga momwe mukufunira.

4Mizinda yathunso ndi anthu ake omwe, onse ndi akapolo anu. Bwerani, mudzachite nawo monga momwe mukufunira.”

5Anthu a Holofernesi adakamuuza mau amenewo.

6Pamenepo iye adatsikira ku mbali ya nyanja, naika asilikali m'mizinda yonse yamalinga, nkutengamo anthu osankhidwa bwino kuti amthandize.

7Anthu akumeneko ndi a ku maiko onse ozungulira adamlandira, atavala nsangamutu zamasamba, namuvinira magule, ng'oma zili m'kati.

8Eks. 34.13; 2Mbi. 17.6Koma iyeyo adagumulabe nyumba zao zachipembedzo nagwetsa mitengo yao yopembedzerapo, chifukwa mfumu inali itamlamula kuti akaononge milungu yonse yam'dzikomo, ndi kukakamiza anthu a mitundu yonse kuti azipembedza Nebukadinezara yekha. Adafuna kuti anthu a mitundu yonse a zilankhulo zosiyanasiyana azimpembedza ngati mulungu.

9Pambuyo pake Holofernesi adapita ku Esdreloni, pafupi ndi Dotani, kuyang'anana ndi malire a Yudeya.

10Adakamanga zithando zankhondo pakati pa Geba ndi Sitopoli. Kumeneko adakhalako mwezi wathunthu akusonkhanitsa zofunika za gulu lake lankhondo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help