1Nawu mndandanda wa maina a atsogoleri a mabanja amene adabwera nane kuchokera ku Babiloni, pa nthaŵi ya ufumu wa Arita-kisereksesi:
2Geresomo, wa fuko la Finehasi. Daniele, wa fuko la Itamara.
3Hatusi, mwana wa Sekaniya, wa fuko la Davide. Zekariya, wa fuko la Parosi. Iyeyu adalembedwa pamodzi ndi anthu ena okwanira 150.
4Eliehoenai, mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahatimowabu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 200.
5Sekaniya, mwana wa Yahaziele, wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 300.
6Ebedi, mwana wa Yonatani, wa fuko la Adini. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 50.
7Yesaya, mwana wa Ataliya, wa fuko la Elamu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 70.
8Zebadiya, mwana wa Mikaele, wa fuko la Sefatiya. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 80.
9Obadiya, mwana wa Yehiyele, wa fuko la Yowabu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 218.
10Selomiti, mwana wa Yosofiya, wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 160.
11Zekariya, mwana wa Bebai, wa fuko la Bebai. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 28.
12Yohanani, mwana wa Hakatani, wa fuko la Azigadi. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 110.
13Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene adabwera pambuyo pake, anali Elifeleti, Yeiyele ndi Semaya, ndipo pamodzi ndi iwowo panali anthu 60.
14Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri, ndipo pamodzi ndi iwowo panali anthu 70.
Ezara asankhula Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu15Anthu onsewo ndidaŵasonkhanitsa ku mtsinje umene umafika mpaka ku mudzi wa Ahava, ndipo kumeneko tidagona m'zithando masiku atatu. Pamene ndinkayang'ana anthu ndi ansembe, ndidapeza kuti ana a Levi palibe.
16Tsono ndidaitana atsogoleri aŵa, Eliyezere, Ariyele, Semaya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi aŵiri, Yoyaribu ndi Elinatani.
17Ndipo ndidaŵatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ndidaŵauza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu wathu.
18Chifukwa cha kutikomera mtima Mulungu wathu, Ido adatitumizira munthu wanzeru, mwana wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israele, dzina lake Serebiya, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi achibale ake, anthu 18 pamodzi.
19Adatitumiziranso Hasabiya ndi Yeshaiya wa fuko la Merari, kudzanso achibale ake ndiponso ana ao, anthu makumi aŵiri.
20Panalinso atumiki a ku Nyumba ya Mulungu okwanira 220, amene Davide ndi nduna zake adaaŵasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onseŵa adalembedwa potsata maina ao.
Ezara atsogolera anthu posala zakudya ndi popemphera21Ku mtsinje wa Ahavako, ndidalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kumpempha kuti atitsogolere ife ndi ana athu, ndiponso kuti ateteze katundu wathu pa ulendo wathu.
22Ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti itipatse gulu la asilikali, ena oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo, oti atiteteze kwa adani athu pa njira. Tinali titauza mfumuyo kuti, “Mulungu wathu amaŵadalitsa onse okhulupirira Iye, koma amaŵakwiyira amene salabadako za Iye.”
23Choncho tidasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze, ndipo Iye adamva kupempha kwathu.
Mphatso zopereka ku Nyumba ya Mulungu24Tsono ndidasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi aŵiri aŵa, Serebiya ndi Hasabiya, pamodzi ndi abale ao khumi.
25Ndipo ndidaŵayesera siliva ndi golide, ndiponso ziŵiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi aphungu ake ndi akalonga ake ndi Aisraele onse amene anali kumeneko, adaazipereka.
26Nditaziyesa zonse, ndidaŵapatsa m'manja mwao siliva wa matani 22, ziŵiya zasiliva za makilogaramu 70, ndiponso golide wa makilogaramu 3,400,
27mbale zagolide makumi aŵiri zolemera makilogaramu pafupi 8 ndi theka, ndiponso ziŵiya ziŵiri za mkuŵa wosalala wonyezemira bwino, zamtengowapatali wonga wa golide.
28Kenaka ndidaŵauza kuti, “Inu ndinu opatulika a Chauta, ndiponso mphatso zonsezi nzopatulika. Siliva ndi golideyu nzopereka zaufulu kwa Chauta, Mulungu wa makolo anu.
29Muzisamale ndi kuzisunga mpaka mutaziyesa pamaso pa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi akulu a mabanja a Aisraele, m'zipinda za m'Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu.”
30Motero ansembe ndi Alevi adalandira siliva, golide ndi ziŵiya zoyesedwa zija, kuti apite nazo ku Yerusalemu ku Nyumba ya Mulungu wathu.
Abwerera ku Yerusalemu31Tsono tidachoka ku mtsinje wa Ahava pa tsiku la 12, pa mwezi woyamba, kupita ku Yerusalemu. Mulungu wathu anali nafe ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, makamaka kwa anthu otibisalira pa njira.
32Tidafika ku Yerusalemu, ndipo tidatandala masiku atatu kumeneko.
33Pa tsiku lachinai lake, m'Nyumba ya Mulungu wathu momwemo, adayesa siliva ndi golide ndi ziŵiya zija, nkuzipereka m'manja mwa wansembe Meremoti, mwana wa Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eleazara mwana wa Finehasi, ndiponso Alevi aŵa: Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Biruyi.
34Zonsezo adaziŵerenga ndi kuziyesa ndipo adalemba kulemera kwa chinthu chilichonse.
35Nthaŵi imeneyo anthu amene adabwerako ku ukapolo, onse amene adaatengedwa aja, adapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, kuperekera Aisraele onse, nkhosa zamphongo 96, anaankhosa 77, ndiponso atonde 12, ngati nsembe yopepesera machimo ao. Zonsezo zinali nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta.
36Iwowo adaperekanso chidziŵitso cha mfumu chija kwa akalonga a mfumu ndi kwa akazembe a m'dera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwowo adathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.