Hos. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pakuti patapita kanthaŵi pang'ono, ndidzalanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene iye adaŵapha ku Yezireele, ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israele.

5Nthaŵi imeneyo ndidzathetsa mphamvu za Israele m'chigwa cha Yezireele.”

6Gomeri adatenganso pathupi, nabala mwana wamkazi. Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa,’ pakuti Israele sindidzamkondanso, ndipo sindidzamkhululukiranso.

7Koma ndidzaonetsa chikondi kwa banja la Yuda, ndipo ndidzaŵapulumutsa ndi mphamvu zanga, Ine Chauta, Mulungu wao. Ndidzaŵapulumutsa osati pochita kumenya nkhondo ndi mauta, malupanga, akavalo ndi anthu okwera pa akavalo ai.”

8Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna.

9Pamenepo Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Si-anthu-anga’, pakuti inu Aisraele sindinunso anthu anga, ndipo Ine sindinenso Mulungu wanu.”

Israele abwereranso

10 Aro. 9.26 Komabe Aisraele adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene sangathe kuuyesa kapena kuuŵerenga. Pamalo pamene Mulungu adaanena anthuwo kuti “Sindinu anthu anga,” pomweponso adzaŵatchula kuti, “Ana a Mulungu Wamoyo.”

11Anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzaŵasonkhanitsanso pamodzi, ndipo adzadzisankhira mtsogoleri mmodzi. Tsono adzatukuka m'dziko mwao, ndithu tsiku la Yezireele lidzakhala lalikulu kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help