1Anthu amene adasindikiza chidindo chao movomereza chipanganocho ndi aŵa: Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya, Zedekiya,
2Senaya, Azariya, Yeremiya,
3Pasuri, Amariya, Malakiya,
4Hatusi, Sebaniya, Maluki,
5Harimu, Meremoti, Obadiya,
6Daniele, Ginetoni, Baruki,
7Mesulamu, Abiya, Miyamini,
8Maziya, Biligai ndi Semaya. Ameneŵa ndiwo anali ansembe.
9Alevi anali aŵa: Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi, wa fuko la Henadadi, Kadimiyele,
10ndi abale ao aŵa: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,
11Mika, Rehobu, Hasabiya,
12Zakuri, Serebiya, Sebaniya,
13Hodiya, Bani ndi Benimu.
14Atsogoleri a anthu anali aŵa: Parosi, Pahatimowabu, Elamu, Zatu, Bani,
15Buni, Azigadi, Bebai,
16Adoniya, Bigivai, Adini,
17Atere, Hezekiya, Azuri,
18Hodiya, Hasumu, Bezai,
19Harifi, Anatoti, Nebai,
20Magapiyasi, Mesulamu, Heziri,
21Mesezabele, Zadoki, Yaduwa,
22Pelatiya, Hanani, Anaiya,
23Hoseya, Hananiya, Hasubu,
24Halohesi, Piliha, Sobeki,
25Rehumu, Hasabuna, Maaseiya,
26Ahiya, Hanani, Anani,
27Maluki, Harimu ndi Baana.
Chipangano28Ife otsalafe, ansembe, Alevi, alonda a pa Nyumba ya Mulungu, oimba nyimbo, atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndi onse amene ankadzipatula kwa mitundu ina ya anthu ya m'maiko achilendo, kuti atsate Malamulo a Mulungu, tonse, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru zokwanira,
29tikuphatikana ndi abale athu olemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata Malamulo a Mulungu amene adaŵapereka Mose mtumiki wa Mulungu. Tidzamvera ndi kuchitadi zimene Malamulo a Chauta, Mulungu wathu, amanena. Tidzamveranso malangizo ndi miyambo yake yolamulidwa. Ndipo titembereredwe tikalephera kuchita zimenezi.
30Eks. 34.16; Deut. 7.3 Sitidzapereka ana athu aakazi kuti akakwatiwe ndi anthu a mitundu ina ya m'dzikomo, sitidzalolanso ana athu aamuna kuti akakwatire ana ao aakazi.
31Eks. 23.10, 11; Lev. 25.1-7; Deut. 15.1, 2 Ndipo ngati anthu a mitundu ina ya m'dzikomo abwera ndi zinthu zamalonda kapena tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la sabata, sitidzaŵagula pa tsiku limenelo, kapenanso pa tsiku loyera lina lililonse. Pa chaka chilichonse chachisanu ndi chiŵiri, tidzagoneka munda osaulima, ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
32 Eks. 30.11-16 Tikulumbiranso kuti chaka ndi chaka tizipereka magaramu anai a siliva, kuti tithandize pa ntchito za ku Nyumba ya Mulungu wathu.
33Tiziperekanso ndalama zolipirira buledi woperekedwa, chopereka cha chakudya ndiponso nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku, zopereka za pa masabata, za pokhala mwezi, za pa masiku achikondwerero osankhidwa, zoperekera zinthu zopatulika ndiponso nsembe zopepesera machimo a Aisraele, kudzanso zoperekera china chilichonse chofunika pa ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu.
34Ife ansembe, Alevi ndi anthu wamba tidzachita maele, kuti tisankhe mabanja amene adzapereke nkhuni ndi kubwera nazo ku Nyumba ya Mulungu wathu, pa nthaŵi zake zoikidwa, chaka ndi chaka, kuti azipserezera nsembe za pa guwa la Chauta, Mulungu wathu, monga mudalembedwera m'Malamulo.
35Eks. 23.19; 34.26; Deut. 26.2 Tikulonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za kuminda kwathu, ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wazipatso, chaka ndi chaka, kuti tizipereke ku Nyumba ya Chauta.
36Eks. 13.2 Tidzaperekanso kwa Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa. Ana a ng'ombe oyamba kubadwa ndiponso ana oyamba kubadwa a nkhosa ndi a mbuzi zathu, tidzapereka kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu, monga mudalembedwera m'Malamulo.
37Num. 18.21 Ndipo ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, tidzaperekanso kwa ansembewo mtanda wathu wa buledi wa ufa woyamba, ndiponso mphatso zathu zina, monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa Alevi chimodzi mwa zigawo khumi za zinthu za m'minda mwathu, pakuti Alevi ndiwo amene amasonkhanitsa zigawo zonse zachikhumi m'midzi yathu yonse.
38Num. 18.26 Wansembe, mdzukulu wa Aroni, adzakhale pamodzi ndi Alevi, pamene Aleviwo akulandira zigawo zachikhumizo. Ndipo Alevi adzabwera ndi zigawozo ku Nyumba ya Mulungu wathu, ku zipinda zosungiramo katundu.
39Aisraele ndiponso a m'banja la Levi adzapereka tirigu, vinyo ndi mafuta kuzipinda kosungira ziŵiya za m'malo opatulika, ndiponso kokhala ansembe amene akutumikira, pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndi anthu oimba nyimbo. Ndithu ife tidzasamala Nyumba ya Mulungu wathu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.