1Tsopano ndifuna kunena za chakudya choperekedwa kwa mafano. Nzoonadi kuti tonse tili nazo nzeru, komatu nzeru zokha zimangotukumula anthu. Chikondi ndicho chimapindulitsa.
2Munthu amene amadziyesa wodziŵa kanthu, ndiye kuti sakudziŵabe kwenikweni monga momwe akadayenera kudziŵira.
3Koma munthu akamakonda Mulungu, ndiye kuti amadziŵika ndi Mulungu.
4Ndinene tsono za chakudya choperekedwa kwa mafano. Tikudziŵa kuti fano si kanthu konse, ndiponso kuti palibe mulungu wina, koma Mulungu mmodzi yekha.
5Ena amati kuli zinthu zina kumwambaku, kapena pansi pano, zimene iwo amazitchula milungu, ndipo anthuwo ali nayodi milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.
6Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
7Komabe si onse amene amadziŵa zimenezi. Ena adazoloŵera kupembedza mafano, ndipo mpaka lero akamadya chakudya choperekedwa kwa mafano, amaganiza ndithu kuti chakudyacho chidaperekedwadi kwa mafano. Tsono popeza kuti ali ndi mitima yofooka, mitima yaoyo imaipitsidwa.
8Nzoona kuti chakudya sichitifikitsa pafupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya chakudyacho, sititayapo kanthu, komanso tikachidya, sitipindulapo kanthu.
9Komabe chenjerani kuti ufulu wanuwu pochita zinthu, ungaphunthwitse ena amene chikhulupiriro chao nchosalimba kwenikweni.
10Ngati iweyo amene uli wodziŵa udya m'nyumba yopembedzeramo fano, nanga tsono munthu wosadziŵa kwenikweni, atakuwona ukuchita zimenezi, kodi chimenechi sichidzamlimbitsa mtima kuti nayenso azidya chakudya choperekedwa kwa mafano?
11Motero amene chikhulupiriro chake nchosalimba kwenikweni, adzatayika chifukwa cha iwe amene uli wodziŵa. Chonsecho tsono iyeyo ndi mbale wako amene Khristu adamufera!
12Mukamachimwira abale anu achikhristu motero, ndi kulakwitsa amene ali ndi mitima yofooka, mukuchimwiranso ndi Khristu yemwe.
13Nchifukwa chake, ngati chakudya chingaphunthwitse mbale wanga wachikhristu, sindidzadya konse nyama, kuti ndingamuphunthwitse mbale wangayo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.