1Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mpango wa nsalu yabafuta, ukavale m'chiwuno, koma osakauviika m'madzi.”
2Choncho ndidakagula mpango, monga momwe Chauta adaandiwuzira, ndipo ndidauvala m'chiwuno.
3Chauta adandiwuzanso mau kachiŵiri kuti,
4“Tenga mpango uja udagula nkuvala m'chiwuno mwakowu. Unyamuke nkupita msanga ku mtsinje wa Yufurate. Kumeneko ukabise mpangowo m'ming'alu yam'mathanthwe.”
5Tsono ndidapitadi kukaubisa mpangowo ku Yufurate, monga momwe Chauta adaandiwuzira.
6Patapita masiku ambiri Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka, pita ku Yufurate, ukatenge mpango wam'chiwuno uja umene ndidaakuuza kuti ukaubise kumeneko.”
7Ine ndidapita ku Yufurate, ndipo ndidakumba pa malo amene ndidaubisa paja, nkuutenga. Koma ndidaona kuti ndi woonongeka kotheratu, wopandanso ntchito.
8Apo mau a adandifikanso:
9Chauta adandiwuza kuti, “Ndimotu m'mene ndidzaonongere zimene a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amanyadira.
10Anthu oipaŵa akana kumvera mau anga. Atsata milungu ina, namaitumikira nkumaipembedza. Iwowo adzakhala ngati mpango wopanda ntchitowu.
11Monga mpango umakanirira m'chiwuno mwa munthu, chonchonso ndidakonza kuti banja lonse la Israele ndi la Yuda lindikangamire kuti onse akhale anthu anga, kuti adzatamande dzina langa ndi kundilemekeza. Koma iwowo sadamvere.
Aneneratu za tsoka lakutsogolo12“Ukaŵauze anthu mau amene Ine Chauta Mulungu wa Israele ndikunena, akuti: Mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo. Iwowo adzakuyankha kuti, ‘Tikudziŵa bwino kuti mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo.’
13Tsono ukaŵauze kuti, Chauta akuti, Ndidzaŵamwetsa vinyo anthu onse am'dzikomo mpaka kuledzera. Anthuwo ndi aŵa: mafumu okhala pa mpando wa Davide, ansembe, aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.
14Ndidzaŵagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha, atate ndi ana ao!” Akuterotu Chauta. “Sindidzaŵachitira chifundo kapena kuŵamvera chisoni, kapena kukhululuka mtima mpaka nditaŵaononga.”
Yeremiya alangiza anthu kuti asanyade15Inu Aisraele, imvani ndipo tcherani khutu.
Musakhale odzimva
chifukwa ndi Chauta amene akulankhula.
16Mlemekezeni Chauta, Mulungu wanu,
asanagwetse mdima,
mapazi anu asanakhumudwe
m'chisisira cham'mapiri,
asanasandutse kuŵala, kumene mukukufuna,
kuti kukhale mdima wandiweyani.
17Koma mukapanda kumvera,
mtima wanga udzalira m'seri
chifukwa cha kunyada kwanu.
M'maso mwanga mudzadzaza misozi yoŵaŵa
chifukwa choti nkhosa za Chauta zatengedwa ukapolo.
18Uza mfumu pamodzi ndi mai wake kuti,
“Tsikani pa mipando yaufumu,
poti zisoti zanu zokongola zaufumu zagwa pansi.
19Mizinda yanu ya ku Negebu aitsekera kunja,
palibe wina woti nkuitsekula.
Yuda yense watengedwa ukapolo,
watengedwa yense ukapolo.
20“Ŵeramukani, inu a ku Yerusalemu,
muwone adani amene akuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene adakusungitsani zili kuti,
nkhosa zanu zokongola zija?
21Kodi mudzatani akadzakuikirani kuti
azikulamulirani anthu amene munkaŵayesa abwenzi anu?
Kodi simudzamva zoŵaŵa
zonga za mkazi pa nthaŵi yochira?
22Mukamadzifunsa kuti,
‘Kodi zimenezi zatigwera bwanji?’
Nchifukwa cha machimo anu ambiri
kuti zovala zanu zikwinzidwe,
ndipo kuti akuchiteni zankhanza.
23Kodi munthu wakuda nkusintha khungu lake?
Kodi kambuku nkusintha maŵanga ake?
Ndiye kuti inuyo, ozoloŵera kuchimwanu,
mungathe kumachita zabwino ngati?
24Chifukwa cha kuipa kwanuko,
ndidzakumwazani ngati mankhusu,
onka nauluka ndi mphepo yakuchipululu.
25Zokuyenerani nzimenezi,
chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa choti mwandiiŵala,
mwakhala mukudalira milungu yonama,”
akuterotu Chauta.
26“Ine Chauta ndidzakwinza zovala zanu
mpaka kumaso,
ndipo maliseche anu adzaoneka.
27Ndaona zonyansa zanu,
zigololo zanu, kutchetcherera kwanu,
ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo.
Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu!
Mudzakhala osayeretsedwabe pa
zachipembedzo mpaka liti?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.