2 Mbi. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu Asa agonjetsa a ku Etiopiya

1Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa masiku a Asa, dziko lidakhala pa mtendere zaka khumi.

2Asa adachita zokoma ndi zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wake.

3Adagwetsa maguwa achilendo, nkuwononga akachisi ku zitunda, nagumula zipilala zamiyala zachipembedzo, nkugwetsa mafano a Asera.

4Ndipo adalamula anthu a ku Yuda kuti azitembenukira kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi kumamvera malangizo ndi malamulo ake.

5M'mizinda yonse ya ku Yuda adaononga akachisi opembedzeramo mafano nagumula maguwa ofukizirapo lubani. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere nthaŵi imene Asa ankalamulira.

6Adamanga mizinda yamalinga ku Yuda, chifukwa dzikolo linali pa mtendere. Sadamenye nkhondo masiku amenewo, popeza kuti Chauta adampatsa mtendere.

7Adauza anthu a ku Yuda kuti, “Tiyeni timange mizinda imeneyi, ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi mipiringidzo yake. Dzikoli lidakali lathu, chifukwa chakuti tachita kufuna kwa Chauta, Mulungu wathu. Tachita kufuna kwake, ndipo Iye watipatsa mtendere pa mbali iliyonse.” Choncho adamangadi zimenezo, ndipo adapeza bwino ndithu.

8Tsono Asa anali nalo gulu lankhondo la anthu 300,000 a ku Yuda. Iwoŵa anali ndi zishango ndi mikondo. Anthu a ku Benjamini analipo 280,000. Iwowo anali ndi zishango ndi mauta. Anthu onsewo anali amphamvu ndi olimba mtima.

9Zera wa ku Etiopiya adanyamuka kukamenyana ndi Ayuda atatenga gulu lake lankhondo la anthu 1,000,000, ndi magaleta 300, ndipo adakafika mpaka ku Maresa.

10Tsono Asa adanyamuka kuti akakomane naye, ndipo onsewo adandanditsa magulu ao ankhondo ku chigwa cha Zefati ku Maresa.

11Pamenepo Asa adafuula kwa Chauta, Mulungu wake, kuti, “Inu Chauta, palibe wina wofanafana nanu woti angathandize pakati pa anthu amphamvu ndi ofooka. Tithandizeni, Inu Chauta, Mulungu wathu, popeza kuti timakhulupirira Inu, ndipo tabwera kudzamenyana ndi chinamtindi cha anthu chimenechi m'dzina lanu. Inu Chauta, ndinu Mulungu wathu. Munthu asakupambaneni ai.”

12Motero Chauta adagonjetsa anthu a ku Etiopiya pamaso pa Asa ndi pa anthu a ku Yuda, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adathaŵa.

13Asa pamodzi ndi anthu ake aja adaŵathamangitsa mpaka ku Gerari, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adaphedwa onse, osatsalapo ndi mmodzi yemwe wamoyo. Zidatero chifukwa anali ndi mantha aakulu pamaso pa Chauta ndi gulu lake lankhondo. Ndipo Ayuda adatenga zofunkha zambirimbiri.

14Tsono adakantha mizinda yonse yozungulira Gerari pakuti anthu ake adaagwidwa ndi mantha oopa Chauta. Adalanda katundu m'mizinda yonse, poti munali chuma chambiri m'mizindamo.

15Ndipo adagwetsa makola a ziŵeto, ndi kutenga nkhosa zochuluka, pamodzi ndi ngamira. Kenaka adabwerera ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help