1Titapulumuka choncho, tidamva kuti chilumbacho dzina lake ndi Melita.
2Anthu apamenepo adatichitira zabwino kwambiri. Adatilandira bwino natisonkhera moto, chifukwa kudaayamba kugwa mvula ndipo kunkazizira.
3Paulo adakatola nkhuni nabwerako ndi mtolo, ndipo pamene ankaziika pa moto, mumtolomo mudatuluka mphiri chifukwa cha kutenthako. Idamluma nkukanirira ku dzanja lakelo.
4Pamene anthuwo adaona njokayo ili lende ku dzanja lake, adayamba kuuzana kuti, “Ndithudi munthu ameneyu nchigaŵenga. Ngakhale wapulumuka pa nyanja, koma Mulungu wachilungamo sadamlole kuti akhale ndi moyo.”
5Komabe Paulo adaikutumulira pa moto njokayo, osapwetekedwa konse.
6Anthu aja ankayembekeza kuti thupi lake litupa, kapena kuti agwa mwadzidzidzi nkufa. Adakhala akumuyang'ana nthaŵi yaitali, koma ataona kuti palibe chilichonse chachilendo chimene chamchitikira, adasintha maganizo nati, “Ameneyu ndi mmodzi wa milungu.”
7Pafupi ndi malowo panali minda ya Publio, mkulu wa pachilumbapo. Iye adatilandira natisamala bwino masiku atatu.
8Bambo wake wa Publioyo anali gone, chifukwa ankadwala malungo ndi kamwazi. Paulo adaloŵa m'chipinda chake nayamba kupemphera, ndipo adamsanjika manja nkumuchiritsa.
9Zitachitika zimenezi, anthu ena onse odwala pachilumbapo adabwera, Paulo nkuŵachiritsa.
10Anthu aja adatipatsa mphatso zambiri, ndipo pamene tidanyamukanso ulendo wathu wapachombo, adatipatsa zonse zosoŵeka.
Paulo afika ku Roma11Patapita miyezi itatu, tidanyamukadi ulendo wathu pa chombo china, chimene chidaakhala pachilumbapo pa nthaŵi yachisanu. Chombocho chinali chochokera ku Aleksandriya, ndipo chinkatchedwa “Ana Amapasa.”
12Titafika ku Sirakusa, tidakhalako masiku atatu.
13Kuchokera kumeneko tidapitirira nkukafika ku Regio. Patapita tsiku limodzi, mphepo ya mwera idayamba kuwomba, choncho pa tsiku lotsatira tidafika ku Puteoli.
14Kumeneko tidapeza abale, ndipo adatiitana kuti tikhale nawo masiku asanu ndi aŵiri. Motero tidakafika ku Roma.
15Abale akumeneko atamva za ife, adabwera mpaka ku Bwalo la Apio ndiponso ku Nyumba za Alendo Zitatu kudzatichingamira. Paulo ataona ataŵaona, adayamika Mulungu, nalimba mtima.
16Pamene tidaloŵa mu mzinda wa Roma, Paulo adaloledwa kukhala kwayekha ndi msilikali womulonda.
Paulo alalika kwa Ayuda ku Roma17Patapita masiku atatu, Paulo adasonkhanitsa atsogoleri a Ayuda akomweko. Atasonkhana, iye adaŵauza kuti, “Abale anga, ine ndili kuno ngati mkaidi wochokera ku Yerusalemu. Ngakhale sindidalikwire mtundu wathu, kapena miyambo ya makolo athu, komabe ndidaperekedwa kwa Aroma.
18Iwo atandifunsa, adaafuna kundimasula, chifukwa sadapeze mlandu woyenera kundiphera.
19Ntc. 25.11Koma pamene Ayuda adakana, ndidakakamizidwa kupempha kuti mlandu wangawo ndidzagwade kwa Mfumu ya ku Roma kuno. Sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga ai.
20Nkuwona ndakuitanani kuti ndilankhule nanu. Pakuti ndamangidwa ndi unyolo uwu chifukwa chokhulupirira chinthu chimene Aisraele akuyembekeza.”
21Atsogoleriwo adamuyankha kuti, “Ife sitidalandirepo makalata ochokera ku Yudeya onena za inu. Palibenso wina mwa abale athu amene adafika kuno kudzatifotokozera kapena kudzatiwuza zoipa za inu.
22Koma makamaka nkwabwino kuti mutiwuze maganizo anu, pakuti za gulu lanu lopatulikali tikudziŵa kuti ponseponse anthu akutsutsana nalo.”
23Pamenepo iwo adapangana naye tsiku, ndipo ambiri adaabwera kunyumba kumene iye ankakhala. Kuyambira m'maŵa mpaka madzulo Paulo adakhala akulankhula nawo, naŵafotokozera za ufumu wa Mulungu. Pakuŵatchulira mau a m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri, ankayesa kuŵakopa kuti akhulupirire Yesu.
24Ena adakopekadi ndi zimene iye adanena, koma ena sadakhulupirire.
25Tsono popeza kuti anthuwo sadamvane, adangochokapo. Komabe asanachoke, Paulo adaawonjezapo mau amodzi aŵa akuti, “Mzimu Woyera adaanena zoona pamene adaauza makolo anu mwa mneneri Yesaya kuti,
26 Yes. 6.9, 10 “ ‘Pita kwa anthu a mtundu uwu ndi kuŵauza kuti:
Kumva mudzamva, koma osamvetsa,
kupenya mudzapenya, koma osazindikira.
27Ndithu mtima wa anthu a mtundu uwu wauma,
agonthetsa makutu ao
ndipo atseka maso ao,
kuwopa kuti angaone ndi maso ao,
ndipo angamve ndi makutu ao,
angamvetse ndi mtima wao,
natembenukira mwa Ine
kuti ndiŵachitiritse.’ ”
28Paulo adaŵauza kuti, “Dziŵani tsono kuti Mulungu watumiza chipulumutso chakechi kwa anthu a mitundu ina. Iwowo adzamva.”
30Tsono Paulo adakhala kumeneko zaka ziŵiri zathunthu m'nyumba yake yobwereka, ndipo ankaŵalandira bwino lomwe onse obwera kudzamuwona.
31Ankalalika za ufumu wa Mulungu, ndi kumaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu poyera, popanda wina aliyense womuletsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.