Yer. 34 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chenjezo kwa Zedekiya

1 2Maf. 25.1-11; 2Mbi. 36.17-21 Inalipo nthaŵi pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi gulu lake lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankaŵalamulira, ndiponso anthu a mitundu yonse, ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira. Nthaŵi imeneyo Chauta adauza Yeremiya kuti,

2“Pita ukauze Zedekiya mfumu ya ku Yuda kuti Chauta akunena kuti Mzinda uwu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzautentha.

3Iweyo sudzapulumuka m'manja mwake. Udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka m'manja mwake. Udzamuwona maso ndi maso, ndipo udzalankhula naye pakamwa ndi pakamwa. Tsono adzakutenga kupita nawe ku Babiloni.

4Komabe imva mau a Chauta, iwe Zedekiya mfumu ya ku Yuda. Akuti, Sudzafera pa nkhondo.

5Koma udzafera pa mtendere. Ndipo paja anthu ankafukiza lubani poika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iweyo usanaloŵe ufumu, tsono nawenso podzaika maliro ako adzafukiza lubani. Pokuimbira nyimbo yamaliro azidzati, ‘Ogo nanu! Mbuyathu uja!’ Ndalankhula zimenezi ndine Mwiniwakene,” akuterotu Chauta.

6Tsono zonsezi mneneri Yeremiya adakakambira Zedekiya, mfumu ya ku Yuda ku Yerusalemu.

7Nthaŵi imeneyo nkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yotsala ya ku Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiyo inali mizinda yamalinga yotsala ya ku Yuda.

Za kuzunza akapolo

8Mau a Chauta adamvekanso kwa Yeremiya. Nthaŵiyo nkuti mfumu Zedekiya atapangana nawo anthu onse a ku Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo ao adzaŵamasule.

9Onse amene anali ndi akapolo Achihebri, aamuna kapena aakazi, aŵamasuledi. Sankayenera kumsunga mu ukapolo Myuda mnzao.

10Akulu onse pamodzi ndi anthu wamba, atachita chipangano kuti akapolo aŵamasule, kuti asaŵasungenso mu ukapolo, zimenezi zidachitikadi ndipo adaŵamasula.

11Komabe pambuyo pake adasintha maganizo ao. Amuna ndi akazi amene adaaŵamasula aja, adaŵagwiranso ukapolo.

12Tsono Chauta adauza Yeremiya kuti

13akalengeze kwa anthu mau a Chauta akuti, “Ndidachita chipangano ndi makolo anu pa tsiku limene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito ku nyumba ya ukapolo ija. Chipanganocho chidati:

14Eks. 21.2; Deut. 15.12 Zaka zisanu ndi ziŵiri zitatha, aliyense mwa inu ammasule mu ukapolo Muhebri aliyense amene adadzigulitsa kwa inu nagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma makolo anu sadandimve ndipo sadasamaleko konse.

15Komabe masiku omwe apitaŵa mudatembenuka mtima ndipo nkuyamba kuchita zomwe ndimafuna Ine. Nonse mudamvana zoŵapatsa ufulu Aisraele anzanu. M'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa mudalonjeza kuti mudzachitadi zimenezi.

16Koma tsono mudasinthanso maganizo, ndipo mwaipitsa dzina langa. Nonsenu mudaŵagwiranso anthu amene mudaaŵamasula aja, nkuŵasandutsanso akapolo anu.”

17Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Simudandimvere, simudalengeze ufulu kuti mumasule abale ndi anansi anu. Chabwino! Ineyo tsono ndidzalengeza ufulu wina kwa inu, ufulu wake wa kufa ndi lupanga, mliri kapena njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu a pa dziko lapansi.

18Simudasamale chipangano chimene mudachita ndi Ine, ndipo simudasunge lonjezo limene mudachita pamaso panga. Tsono Ine ndidzakusandutsani ngati mwanawang'ombe uja amene ankamdula paŵiri napita pakati pa zigawozo.

19Amene ankadutsa pakati pa zigawo ziŵiriwo anali akulu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, atsogoleri a boma, ansembe, ndiponso anthu a m'dzikomo.

20Onsewo ndidzaŵapereka kwa adani ao ndi kwa amene amafuna kuŵapha. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi nyama zakuthengo.

21Ndidzapereka Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi nduna zake, kwa adani ao amene amafuna kuŵapha, ndiye kuti kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni limene nthaŵi ino layamba kubwerera m'mbuyo.

22Koma ndidzaŵalamula, ndidzaŵabwezeranso ku mzinda uno. Adzauthira nkhondo ndi kuulanda, ndipo adzautentha. Motero mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa chipululu, mopanda anthu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help