1Mfumu Ahabu anali ndi zidzukulu zazimuna 70 ku Samariya. Tsono Yehu adalemba makalata naŵatumiza ku Samariya kwa olamulira mzindawo, kwa akuluakulu ndiponso kwa anthu amene ankalera zidzukulu za Ahabu kuti,
2“Inu mukusamalira zidzukulu za mbuyanu Ahabu, ndipo muli nawo magaleta, zida zankhondo ndiponso mizinda yamalinga. Nchifukwa chake tsono mukangolandira kalatayi,
3mwa zidzukulu za mbuyanu musankhule mmodzi wooneka bwino kwambiri ndipo mumloŵetse ufumu wa bambo wake. Kenaka mukonzekere nkhondo kumenyera banja la mbuyanu.”
4Koma anthuwo adachita mantha kwambiri, ndipo adati, “Ha! Mafumu aŵiri aja sadathe kulimbana naye Yehu, nanga ife ndiye tingathe bwanji?”
5Motero woyang'anira nyumba ya mfumu ndiponso wina woyang'anira mzinda, pamodzi ndi akuluakulu, kudzanso amene ankalera anawo, adatumiza mau kwa Yehu kuti, “Ife ndife anthu anu, ndipo tidzachita zonse zimene mutiwuze. Sitidzaika wina aliyense kuti akhale mfumu. Muchite zonse zimene zikukomereni.”
6Tsono Yehu adaŵalemberanso kalata yachiŵiri kuti, “Ngati muli pambuyo panga, ndipo ngati muli okonzeka kundimvera, mudule mitu ya ana a mbuyanu, mudze nayo kwa ine ku Yezireele maŵa nthaŵi yonga yomwe ino.” Ndiye kuti zidzukulu za mfumu 70 zija zinkaleredwa ndi akuluakulu amumzinda aja.
7Ndiye akuluakuluwo atalandira kalata ija, adagwira zidzukulu za mfumuzo nkuzipha, 70 zonsezo, naika mitu yao m'madengu, nkuitumiza kwa Yehu ku Yezireele.
8Tsono wamthenga adafika nauza Yehu kuti, “Abwera nayo mitu ija ya zidzukulu za mfumuyi.” Apo iyeyo adati, “Kaiwunjikeni m'miyulu iŵiri pa chipata, ndipo ikhale pamenepo mpaka m'maŵa.”
9M'maŵa mwake atatuluka, Yehu adapitako nauza anthu onse kuti, “Inu sindinu ochimwa ai. Wochimwa ndine, popeza kuti ndidachita chiwembu mbuyanga, ndipo ndidamupha. Koma adapha anthu onseŵa ndani?
10Dziŵani tsono kuti mau a Chauta, amene adanena za banja la Ahabu, sadzapita padera. Ndi Chauta amene wachitadi zimene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake.”
11Hos. 1.4Pambuyo pake Yehu adapha onse otsala a banja la Ahabu ku Yezireele, akuluakulu ake onse, abwenzi ake onse ozoloŵerana naye ndiponso ansembe ake. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe.
Abale a mfumu Ahaziya aphedwa12Pambuyo pake Yehu adanyamuka napita ku Samariya. Atafika pa malo otchedwa “Pogona abusa,”
13adakumana ndi abale ake a Ahaziya mfumu ya Yuda. Adaŵafunsa kuti, “Nanga inunso ndinu yani?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abale a malemu Ahaziya, ndipo tidabwera kudzacheza ndi ana a mfumu Ahabu, ndiponso ana a mfumukazi Yezebele.”
14Tsono Yehu adati, “Atengeni amoyo.” Ndipo adaŵatenga amoyo, nakaŵaphera ku chitsime cha ku malo aja a abusaŵa, anthu okwanira 42. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe.
Abale otsala a Ahabu aphedwa15Atachoka kumeneko, Yehu adakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu akudzamchingamira. Tsono adamlonjera namuuza kuti, “Kodi maganizo ako akugwirizana ndi maganizo anga, monga momwe maganizo anga akugwirizanirana ndi ako?” Yehonadabu adayankha kuti, “Inde, zathu nzimodzi.” Yehu adati, “Ngati ndi momwemodi, gwire dzanja.” Yehonadabuyo adapereka dzanja lake, Yehu nkumgwira dzanja namkweza pa galeta lake.
16Ndipo adamuuza kuti, “Tiye kuno, uwone m'mene ndikudziperekera kwa Chauta.” Motero adayenda naye m'galeta mwake.
17Atafika ku Samariya, Yehu adapha onse amene adatsalako a banja la Ahabu, mpaka adaŵapulula onse, potsata mau a Chauta amene Eliya adaŵalankhula.
Anthu opembedza Baala aphedwa18Pambuyo pake Yehu adasonkhanitsa anthu onse a mu mzinda wa Samariya naŵauza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pang'ono chabe. Koma ine Yehu ndidzamtumikira kwambiri.
19Nchifukwa chake tsono itanireni aneneri onse a Baala, onse amene amapembedza Baalayo, pamodzi ndi ansembe ake onse. Pasasoŵeke ndi mmodzi yemwe, poti ndili ndi nsembe yaikulu yoti ndiipereke kwa Baala. Amene asoŵeke, adzaphedwa.” Koma Yehu adachita zimenezi mochenjera, kuti aononge onse amene ankapembedza Baala.
20Motero Yehu adalamula kuti: “Mulengeze kuti kuli msonkhano wolemekeza Baala.” Anthu adaulengezadi msonkhanowo.
21Yehu adatumiza mau ku dziko lonse la Israele, ndipo onse amene ankapembedza Baala adabweradi, kotero kuti sadatsalepo ndi mmodzi yemwe. Onsewo adaloŵa m'nyumba ya Baala, ndipo anthu adachita kuti thothotho m'nyumbamo. Sipadatsale malo mpang'ono pomwe.
22Tsono Yehu adauza munthu wosunga zovala kuti, “Bwera ndi zovala zopatulika zokwanira anthu onse opembedza Baala.” Munthuyo adaŵatengera zovalazo anthu aja.
23Yehu adaloŵa m'nyumba ya Baala pamodzi ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu. Ndipo adauza anthu aja opembedza Baalaŵa kuti: “Yang'anani bwino, ndipo muwone kuti pasakhale mtumiki wa Chauta pano pakati panupa, koma opembedza Baala okhaokha.”
24Tsono Yehu adaloŵa kukapereka nsembe zopsereza.
Koma Yehu anali ataika anthu 80 panja naŵauza kuti, “Adzaphedwa amene athaŵitse aliyense mwa anthu amene ndikupatseni kuti muŵapheŵa.”
25Tsono Yehu uja atangomaliza kupereka nsembe yopsereza ija, adauza asilikali ake ndi akapitao ao kuti: “Loŵani muŵaphe! Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Iwo adaloŵadi, nkukapha onse amene anali m'menemo, naponya mitembo yao panja. Adakaloŵanso m'chipinda cham'kati cha nyumba ya Baala ija.
26Ndipo adatulutsamo chipilala chopatulika chimene chinali m'nyumba ya Baala nakachitentha.
27Motero asilikaliwo adaononga chipilala chopatulika cha Baala, naononganso nyumba yake, ndipo adaisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.
28Motero Yehu adaononga kotheratu chipembedzo cha Baala m'dziko la Israele.
291Maf. 12.28-30 Koma Yehuyo sadaleke kwenikweni zoipa zimene ankachita mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene ankachimwitsa nazo Aisraele. Sadaleke kupembedza zifanizo zagolide za anaang'ombe zimene zinali ku Betele ndi ku Dani.
30Ndipo Chauta adauza Yehu kuti: “Chifukwa choti wachita zondikomera Ine, poononga banja la Ahabu monga momwe ndinkafunira, ana ako adzakhala pa mpando waufumu wa Israele mpaka mbadwo wachinai.”
31Koma Yehuyo sankasamala Malamulo a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi mtima wake wonse. Adapitirizabe kuchita zoipa zimene Yerobowamu adachimwitsa nazo Aisraele.
Imfa ya Yehu32Masiku amenewo Chauta adayamba kuchepetsa dziko la Israele. Mfumu Hazaele wa ku Siriya adagonjetsa Aisraele.
33Adayambira ku Yordani chakuvuma, nakafika ku Aroere pafupi ndi chigwa cha Arinoni. Dziko limeneli lidaphatikiza madera onse a Giliyadi ndi Basani, kumene zinkakhala zidzukulu za Gadi, Rubeni ndi Manase.
34Tsono ntchito zina za Yehu ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
35Yehu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Samariya. Ndipo Yohowahazi mwana wake adaloŵa ufumu ku Israele m'malo mwake.
36Yehu adalamulira Aisraele ku Samariya zaka 28.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.