1Chaka cha 18 cha ufumu wa Yehosafati m'dziko la Yuda, Yoramu mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri.
2Yoramu ankachimwira Chauta, koma kuipa kwake sikudafanefane ndi kwa bambo wake ndi kwa mai wake Yezebele. Yoramuyo adagumula fano la Baala limene bambo wake adaamanga.
3Komabe adaumirira kuchita zoipa zomwe ankachita Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adaachimwitsa nazo Aisraele, osafuna konse kuzileka.
4Kale Mesa, mfumu ya Amowabu, ankaŵeta nkhosa. Ndipo chaka ndi chaka ankapereka ngati msonkho kwa mfumu ya Israele anaankhosa okwanira 100,000, ndiponso ubweya wa nkhosa zamphongo 100,000.
5Koma Ahabu atamwalira, mfumu ya Amowabuyo idagalukira mfumu ya ku Israele.
6Motero mwamsangamsanga mfumu Yoramu adatuluka kuchoka ku Samariya, nasonkhanitsa gulu lonse la ankhondo la Aisraele.
7Kenaka Yoramuyo adatumiza mau kwa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Mfumu ya Amowabu yandigalukira ine. Kodi sungapite nane kunkhondo, kuti tikamenyane ndi Amowabu?” Tsono Yehosafatiyo adayankha kuti, “Ndidzapita. Ine ndi iwe ndife amodzi, anthu anga ndi ako omwe, akavalo anga ndi akonso.”
8Tsono Yehosafatiyo adafunsa kuti, “Kodi tidzere njira iti popita kunkhondoko?” Yoramu adayankha kuti, “Tidzere ku chipululu cha Edomu.”
9Motero mfumu ya ku Israele pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda kudzanso mfumu ya ku Edomu, onsewo adapita limodzi. Ndipo atayenda mozungululira m'chipululu masiku asanu ndi aŵiri, kunalibe madzi oti amwe asilikali pamodzi ndi nyama zosenza katundu.
10Tsono mfumu Yoramu adati, “Kalanga ine! Chauta waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.”
11Apo mfumu Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri woti angatithandize kupempha nzeru kwa Chauta?” Mmodzi mwa atsogoleri a gulu la ankhondo la mfumu Yoramu adayankha kuti, “Aliko Elisa, mwana wa Safati, amene anali mtumiki wa Eliya.”
12Pomwepo Yehosafati adati, “Elisayo ndiye mneneri weniweni wa Chauta.” Choncho mafumu atatu aja adapita kwa mneneri Elisa.
13Tsono Elisa adafunsa mfumu Yoramu kuti “Inu kwanga kuno mwadzatani? Bwanji osapita kwa aneneri amene bambo wanu ndi mai wanu ankapemphako nzeru.” Koma Yoramu adati, “Iyai, pakuti Chauta ndiye amene waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.”
14Elisa adati, “Pali Chauta Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamtumikira, pakadapanda kuti ndimamchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikadakusamalani ngakhale kukuyang'anani komwe.
15Koma tsono mundiitanire munthu wodziŵa kuimba bwino zeze.” Woimba zezeyo atabwera, adaimba nyimbo ndipo mphamvu za Chauta zidadza pa Elisayo.
16Tsono adati, “Chauta akuti, ‘Mukumbe migwere mu mtsinje wopanda madziwu, ndipo Ine ndidzadzazamo madzi.
17Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe mtsinje wopanda madziwu udzadzaza ndi madzi, ndipo inuyo mudzamwa, pamodzi ndi ng'ombe zanu ndi zoŵeta zanu zina zomwe.’
18Koma zimenezi nzochepa kwa Chauta. Iye adzaperekanso Amowabu m'manja mwanu.
19Mudzagonjetsa mizinda yao yonse yamalinga ndi yabwinoyabwino ija. Mudzagwetsa mitengo yabwino yonse ndi kutseka akasupe onse a madzi, ndipo mudzaononga minda yao yonse yachonde, pakuponyamo miyala.”
20M'maŵa mwake, nthaŵi yopereka nsembe ili pafupi, adangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, mpaka malowo adadzaza madzi.
21Tsono Amowabu atamva kuti mafumu atatu abwera kuti achite nawo nkhondo, adaitana onse amene ankatha kumenya nkhondo kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Onsewo adakandanda ku malire.
22Amowabuwo atadzuka m'mamaŵa pamene dzuŵa linkaŵala pa madzi, adaona madzi ali psuu ngati magazi kutsogolo kwao.
23Tsono adati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha, ndipo ankhondo ao aphana. Tiyeni tikafunkhe.”
24Koma Amowabu aja atafika ku zithando za Aisraele, Aisraelewo adaŵathira nkhondo, iwowo nkuyamba kuthaŵa. Koma Aisraele aja ankapha Amowabuwo akuŵapirikitsa.
25Tsono Aisraele adagumula mizinda yao, ndipo pa munda uliwonse wachonde aliyense ankaponyapo mwala, mpaka minda yonse idadzaza ndi miyala. Adatseka akasupe onse, nagwetsa mitengo yonse yabwino. Kudatsala mzinda wa Kiri-Haresefi wokha, koma pambuyo pake ankhondo oponya miyala adabwera naugonjetsa.
26Mfumu ya Amowabu itaona kuti nkhondo yaŵaipira, idatenga anthu 700 amalupanga, kuti athaŵe modutsa ankhondo kupita kwa mfumu ya ku Edomu, koma adalephera.
27Choncho idatenga mwana wake wachisamba amene adaayenera kudzaloŵa ufumu wake, nimpereka pa linga ngati nsembe yopsereza kwa mulungu wa Amowabu. Zimenezi zidadzetsa ukali waukulu wokwiyira Aisraele, mwakuti iwo adangoithaŵa mfumuyo, nabwerera ku dziko lakwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.