1 Yak. 5.17 Mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, adauza Ahabu kuti, “Pali Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene ndimamtumikira, sipakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, mpaka ine ntanena.”
2Kenaka Chauta adauza Eliyayo kuti,
3“Chokako kuno, upite chakuvuma, ukabisale ku mtsinje wa Keriti, kuvuma kwa Yordani.
4Uzikamwa mumtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”
5Choncho Eliyayo adapita nakachita monga momwe Chauta adaanenera. Adapita nakakhala m'mbali mwa mtsinje wa Keriti kuvuma kwa Yordani.
6Tsono makwangwala ankadzampatsa buledi ndi nyama m'maŵa ndi madzulo. Ndipo ankamwa madzi kumtsinjeko.
7Patangopita kanthaŵi, mtsinjewo udaphwa, poti kunalibe mvula m'dzikomo.
Eliya ndi mai wamasiye wa ku Zarefati8Tsono Chauta adauzanso Eliya kuti,
9Lk. 4.25, 26 “Nyamuka upite ku Zarefati, mudzi wa ku Sidoni, ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mai wamasiye wakumeneko kuti azikakudyetsa.”
10Choncho Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mai wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana maiyo namuuza kuti, “Patseniko madzi pang'ono, ndimwe.”
11Pamene mai uja ankapita kukatunga madziwo, Eliya adamuitananso namuuza kuti, “Munditengerekonso kabuledi.”
12Apo maiyo adati, “Pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang'ono m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.”
13Koma Eliya adauza maiyo kuti, “Musade nkhaŵa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang'ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu.
14Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
15Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri.
16Ufa umene unali m'mbiyamo sudathe, mafuta amene anali m'nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Eliya.
17Tsiku lina mwana wa mkazi wamasiye uja, mwini wake nyumba, adadwala. Matenda adakula kwambiri, kotero kuti mwanayo adamwalira.
18Mkazi uja adafunsa Eliya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu mneneri wa Mulungu? Kodi mwadza kwa ine kuno kudzakumbutsa Mulungu machimo anga ndi kundiphera mwana wanga?”
19Eliya adauza maiyo kuti, “Tandipatsani mwanayo.” Pompo Eliya adatenga mwanayo pa mfukato ya mai uja, napita naye ku chipinda chapamwamba, kumene ankagona, ndipo adakamgoneka pa bedi lake.
20Kenaka Eliya adatama Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, kodi mai wamasiyeyu, amene akundisunga, mwamchitiranji choipa chotere, pomuphera mwana wake?”
212Maf. 4.34, 35 Tsono adafungatira mwanayo katatu, natamanso Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, mubwezereni moyo wake mwanayu.”
22Ndipo Chauta adamumvera Eliyayo. Pomwepo moyo wa mwana uja udabwereranso mwa iye natsitsimuka.
23Eliya adatenga mwanayo, natsika naye kuchoka m'chipinda chapamwamba chija, ndipo adampereka kwa mai wake. Tsono adauza maiyo kuti, “Onani, mwana wanu ali moyo.”
24Ndipo mai uja adauza Eliya kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndipo Chauta walankhula kudzera mwa inu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.