1 Mbi. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu oimba nyimbo

1Davide pamodzi ndi akuluakulu osamalira za utumiki adapatulanso anthu ena otumikira mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni amene ankalosa poimba ndi apangwe ndi azeze ndiponso ziwaya zamalipenga. Mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchitoyo ndiponso mndandanda wa ntchito zao nawu:

2Mwa ana a Asafu panali Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asarela. Amene ankaŵatsogolera ndi Asafu. Ameneŵa ankalalika, mfumu ikaŵalamula kutero

3Panali ana asanu ndi mmodzi a Yedutuni, maina ao naŵa: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Amene ankaŵatsogolera ndi bambo wao Yedutuni. Iwoŵa ankalalika ndiponso kuimba ndi pangwe pothokoza ndi kutamanda Chauta.

4Ana a Hemani naŵa: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, Romamiti-Yezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, kudzanso Mahaziyoti.

5Onseŵa anali ana a Hemani, mneneri wa mfumu, potsata malonjezo a Mulungu akuti adzamkweza iyeyo. Pakuti Mulungu adaampatsa Hemaniyo ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.

6Iwowo ankaimba potsata malangizo a bambo wao m'Nyumba ya Mulungu. Ankaimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira ku Nyumba ya Mulungu. Asafu, Yedutuni ndi Hemani inkaŵalamulira ndi mfumu imene.

7Anthu onseŵa anali aluso pa zoimba, achibale ao nawonso adaaphunzira kwambiri kuimbira Chauta. Onse pamodzi analipo 288.

8Poŵagaŵira ntchito zao ankachitira maere, osasiyanitsa pakati pa ang'onoang'ono ndi akuluakulu, aphunzitsi ndi ophunzira.

9Maere oyamba adagwera Yosefe, wa banja la Asafu. Achiŵiri adagwera Gedaliya, iyeyo ndi abale ake ndi ana ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

10Maere achitatu adagwera Zakuri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

11Maere achinai adagwera Iziri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

12Maere achisanu adagwera Netaniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

13Maere achisanu ndi chimodzi adagwera Bukiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

14Maere achisanu ndi chiŵiri adagwera Yesarela, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

15Maere achisanu ndi chitatu adagwera Yesaya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

16Maere achisanu ndi chinai adagwera Mataniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

17Maere akhumi adagwera Simei, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

18Maere a 11 adagwera Azarele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

19Maere a 12 adagwera Hasabiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

20Maere a 13 adagwera Subaele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

21Maere a 14 adagwera Matitiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

22Maere a 15 adagwera Yeremoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

23Maere a 16 adagwera Hananiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

24Maere a 17 adagwera Yosibekasa, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

25Maere a 18 adagwera Hanani, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

26Maere a 19 adagwera Maloti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

27Maere a 20 adagwera Eliyata, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

28Maere a 21 adagwera Hotiri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

29Maere a 22 adagwera Gidaliti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

30Maere a 23 adagwera Mahaziyoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

31Maere a 24 adagwera Romamiti-Yezere, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help