1Chauta wakwiya kwambiri,
taonani m'mene waphimbira Ziyoni ndi mdima!
Ulemerero wa Israele wautaya pansi kuuchotsa Kumwamba.
Pa tsiku la mkwiyo wake sadakumbukirenso
kuti Ziyoni anali ngati mphondero yake.
2Chauta adaononga midzi yonse ya Yakobe
popanda ndi chifundo chomwe.
Chifukwa cha kupsa mtima
adathyola malinga a mizinda ya Yuda.
Adagwetsera pansi mochititsa manyazi,
ufumu wa Israele ndi olamulira ake.
3Chauta atapsa mtima
adathyola nyonga zomwe ankanyadira Israele.
Adabweza dzanja lake loteteza,
adani atayandikira.
Mkwiyo wake udalanga fuko la Yakobe
ngati moto walaŵilaŵi wonka nuwononga zonse.
4Adalozetsa mivi yake kwa ife ngati mdani wathu,
wasamuladi dzanja ngati mdani.
Adapha onse amene tinkaŵayang'ana monyadira,
pakati pa anthu a mu mzinda wa Ziyoni.
Ukali wake unkachita kuyaka ngati moto.
5Chauta adakhala ngati mdani,
adaononga Israele.
Adaononga nyumba zonse zachifumu,
malinga ao onse adaŵasandutsa mabwinja.
Adachulukitsa kulira ndi kudandaula
pakati pa anthu a ku Yuda.
6Adapasula Nyumba yake ngati khumbi lam'munda,
malo ake a msonkhano adaŵasandutsa bwinja.
Chauta adathetseratu ku Ziyoni
masiku achikondwerero ndi a Sabata.
Ndipo atakwiya kwambiri
adanyoza mfumu pamodzi ndi ansembe.
7Chauta adanyoza ngakhale guwa lake lomwe,
ndipo adaŵakana malo ake opatulika.
Adapereka malinga a nyumba zake zachifumu
m'manja mwa adani ake.
M'nyumba yeniyeni ya Chauta
adaniwo adafuula ndi chimwemwe
monga momwe zimachitikira pa tsiku lachikondwerero.
8Chauta adaatsimikiza
zoti aononge malinga a mzinda wa Ziyoni.
Adauyesa ndi chingwe chake,
ndipo sadafune kuleka kuuwononga kotheratu.
Adaliritsa okhala pa malinga ndi pa makoma ake,
onsewo akuzunzikira limodzi.
9Zipata za mzindawo zakwiririka pansi.
Mipiringidzo yake yathyoka ndi kusakazika.
Mfumu yake ndi akalonga ake ali ku ukapolo
pakati pa anthu akunja,
malamulo a Mulungu palibenso oŵalalika.
Aneneri ake omwe sakuchitanso
zija zoona zinthu m'masomphenya zochokera kwa Mulungu.
10Akuluakulu a mu mzinda wa Ziyoni,
akhala pansi atangoti chete.
Adzithira fumbi kumutu, ndipo avala ziguduli.
Anamwali a ku Yerusalemu aŵeramitsa mitu yao pansi.
11Maso anga atopa nkulira,
moyo wanga wazunzika zedi,
Mumtima mwanga mwadzaza chisoni,
chifukwa choti anthu anga aonongeka,
ana ndi makanda omwe akukomoka m'miseu yamumzinda.
12Anawo akufunsa amai ao kuti,
“Kodi chakudya ndi chakumwa tingazipeze kuti?”
Akufunsa zimenezi pamene akukomoka m'miseu yamumzinda
ngati anthu olasidwa.
Akuthatha ndi moyo pa mfukato wa amai ao.
13Iwe mzinda wa Yerusalemu,
ndinganene chiyani za iwe,
kaya nkukuyerekeza ndi chiyani?
Iwe mzinda wangwiro wa Ziyoni,
kodi ndingakufanizire ndi yani,
kuti choncho ndikusangalatse?
Kuwonongeka kwako nkwakukulu ngati nyanja.
Ndani angathe kukukonzanso?
14Zinthu zimene aneneri ako adakuwonera m'masomphenya
zinali zabodza ndi zonyenga.
Iwo sadaonetse uchimo wako, kuti ukhalenso pabwino.
Mau amene adakutengeraniwo anali abodza ndi osokeretsa.
15Onse odutsa m'njira akukuwombera m'manja mokunyodola.
Akukutsonya ndi kukupukusira mitu,
iwe mzinda wa Yerusalemu.
Akunena kuti,
“Kodi mzinda uja ndi uwu
umene kale lija ankautcha wodala kotheratu,
mzinda wokondweretsa dziko lonse lapansi?”
16Adani ako onse akukuyasamira kukamwa mwaukali,
ndipo akukunyodola.
Akukutsonya ndi kumakukuta mano ao namanena kuti,
“Tafikapodi pousakaza!
Ah! Tsiku lija tinkafunali ndi lero.
Tagonera, taliwonadi.”
17Chauta wachitadi zimene adakonzekera kuti achite.
Wachitadi zimene ankanena moopseza.
Monga momwe adaakonzeratu masiku amakedzana,
wakuwononga mopanda chifundo,
walola adani kuti akondwe
chifukwa cha tsoka lako,
ndipo wakulitsa kwambiri mphamvu za adani ako.
18Fuulani kwamphamvu kwa Ambuye, inu anthu a ku Ziyoni.
Misozi yanu ichite kuti yoyoyo,
ngati mtsinje, usana ndi usiku.
Musadzipatse nthaŵi yoti mupumule.
Misozi yanu isalekeze.
19Dzukani, ndipo mufuule usiku
pachiyambi penipeni pa maulonda.
Nenani zanu zonse zakukhosi pamaso pa Ambuye.
Kwezani manja ndi kupemphera kwa Ambuyewo
chifukwa cha moyo wa ana anu
amene akukomoka ndi njala m'miseu yonse.
20Inu Chauta onani, ndipo mupenye!
Kodi ndani amene Inu mwamuvuta chotereyu?
Kodi akazi achite kudya ana ao,
ana amene iwo omwe adaŵalera bwino?
Nanga ansembe ndi aneneri,
kodi achite kuŵaphera m'malo opatulika a Ambuye?
21Anyamata ali gonegone m'miseu
pamodzi ndi nkhalamba zomwe.
Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi nkhondo.
Mwaŵapha pa tsiku la mkwiyo wanu,
mwaŵapha mopanda chifundo.
22Monga momwe mumaitanira ku chikondwerero,
ndi m'mene mwandiitanira zoopsa kuchokera mbali zonse.
Inu Chauta, pa tsiku la mkwiyo wanu,
palibe amene adathaŵako kapena kupulumuka.
Onse amene ndidaŵabala ndi kuŵalera,
adani anga adaŵaononga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.