1Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Mumandisangalatsa ndipo ndinu mphotho yanga imene ndimainyadira. Okondedwa anga, limbikani choncho mogwirizana ndi Ambuye.
2Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye.
3Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo.
4Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.”
5Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.
6Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
7Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
9Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Aŵayamika chifukwa cha mphatso yao10Ndakondwa kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano, patapita nthaŵi yaitali, mwayambanso kuwonetsa kuti mumandikumbukira. Kukumbukira munkandikumbukiradi, koma munkangosoŵa mpata woti muwonetsere.
11Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo.
12Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu.
13Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.
14Komabe mudaachita bwino kundithandiza pa zovuta zanga.
15Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha.
16Ntc. 17.1
2Ako. 11.9Pamene ndinali ku Tesalonika, mudatumiza kangapo zondithandiza pa zosoŵa zanga.17Sikuti ndikuika mtima pa mphatso zanu ai, koma chimene ndikukhumba nchakuti pa zimene muli nazo, pawonjezedwe phindu.
18Eks. 29.18Ndalandiradi zonse, ndipo ndili nazo zochuluka. Ndili ndi zonse zofunika tsopano, popeza kuti ndalandira kwa Epafrodito zimene mudanditumizira. Zili ngati chopereka cha fungo lokoma, ngati nsembe imene Mulungu ailandira ndi kukondwera nayo.
19Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
20Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen.
Mau otsiriza21M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno.
22Akukupatsani moni anthu onse a Mulungu amene ali kuno, makamakanso ogwira ntchito ku nyumba ya Mfumu ya ku Roma.
23Ambuye Yesu Khristu akudalitseni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.