1Chaka cha 27 cha ufumu wa Yerobowamu mfumu ya ku Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2Iyeyu anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3Azariya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya.
4Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.
5Tsono Chauta adailanga mfumuyo ndi nthenda ya khate mpaka kufa kwake, ndipo inkakhala m'nyumba yakeyake yapadera. Choncho Yotamu mwana wa mfumuyo ndiye amene ankayang'anira banja la mfumu, namalamulira anthu m'dzikomo m'malo mwake.
6Tsono ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
7 mfumu ya ku Yuda, ndipo adalamulira mwezi umodzi ku Samariya.
14Tsono Menahemu mwana wa Gadi, adachoka ku Tiriza nakafika ku Samariya. Adapha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariyako, iyeyo nkuloŵa ufumu m'malo mwa Salumu.
15Tsono ntchito zonse za Salumu ndi chiwembu chimene adachita, zonsezi zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
16Nthaŵi imeneyo, kuchokera ku Tiriza Menahemu adakaononga mzinda wa Tapuwa ndi anthu onse amene anali m'menemo, kuphatikiza dziko lonse lozungulira, poti iwo sadamgonjere. Adaphanso akazi apathupi amumzindamo naŵang'amba.
Menahemu mfumu ya ku Israele17Chaka cha 39 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Menahemu mwana wa Gadi adaloŵa ufumu wa ku Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ku Samariya.
18Menahemu ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Masiku onse a moyo wake sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
19Pambuyo pake Pulo, mfumu ya ku Asiriya, adadzathira nkhondo dziko la Israele. Ndipo Menahemu adakapereka kwa Pulo siliva wokwanira makilogramu 34,000, kuti Puloyo amthandize kukhazikitsa ufumu wake.
20Menahemu adapeza ndalamazo kuchokera ku msonkho umene ankakhometsa Aisraele. Anthu onse olemera ankaŵakhometsa aliyense masekeli asiliva makumi asanu. Motero mfumu ya ku Asiriya idabwerera, ndipo sidakhale m'dzikomo.
21Tsono ntchito zina za Menahemu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
22Ndipo Menahemu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo. Tsono Pekahiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Pekahiya mfumu ya ku Israele23Chaka cha 50 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.
24Pekahiya adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
25Tsono Peka mwana wa Remaliya nduna yake, pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi, adapangana za chiwembu napha Pekahiya ku Samariya m'chipinda choteteza nyumba ya mfumu. Pambuyo pake Pekayo adaloŵa ufumu m'malo mwake.
26Tsono ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
Peka mfumu ya ku Israele27Chaka cha 52 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Peka mwana wa Remaliya adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka makumi aŵiri.
28Koma adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
29Nthaŵi ya Peka mfumu ya ku Israele, Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adadzagonjetsa mizinda iyi: Iyoni, Abele-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi, Hazori, dziko la Giliyadi ndi la Galilea, ndiponso dziko lonse la Nafutali. Ndipo anthu onse am'menemo adaŵagwira ukapolo, napita nawo ku Asiriya.
30Nthaŵi imeneyo Hoseya mwana wa Ela adachita chiwembu kuchitira mfumu Peka, namupha. Ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwake pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda.
31Tsono ntchito zina za Peka ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Israele.
Yotamu mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 27.1-9)32Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
33Anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa, mwana wa Zadoki.
34Yotamu adachita zolungama pamaso pa Chauta ndipo kutsata zonse zimene ankachita Uziya bambo wake.
35Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe namafukiza lubani pa malo amenewo. Yotamu ndiye adamanga chipata chakumpoto cha Nyumba ya Chauta.
36Tsono ntchito zina za Yotamu, ndi zonse zimene ankachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
37Nthaŵi imene Yotamu ankalamulira, mpamene Chauta adayambapo kutuma Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa mfumu ya ku Israele, kuti akathire nkhondo dziko la Yuda.
38Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.