1Yudasi amene ankatchedwa Makabeo, mwana wa Matatiasi, adaloŵa m'malo mwa bambo wake.
2Abale ake onse ankamuthandiza, pamodzi ndi ena onse amene ankatsata bambo wake. Onsewo ankamenyera Israele nkhondo mokondwa.
3Yudasiyo adakulitsa ulemerero wa anthu a mtundu wake.
Adavala malaya achitsulo ankhondo ngati chiphona,
namangirira zida zankhondo m'chiwuno mwake.
Ankamenya nkhondo, natchinjiriza zithando zake
ndi lupanga lake.
4Anali ngati mkango pa zochita zake,
ngati mwanawamkango wobangula polumphira nyama.
5Ankalondola ndi kupirikitsa anthu okana chipembedzo
ankatentha onse ovutitsa anthu a mtundu wake.
6Anthu okana chipembedzo ankachita mantha,
nkumamthaŵa.
Onse ochita zoipa ankasokonezeka.
Dzanja lake lidabweretsa chipulumutso mokhoza.
7Pogwira ntchito zake, adakwiyitsa mafumu ambiri,
koma adakondwetsa banja la Yakobe.
Choncho mbiri yake idzakhala yotamandika mpaka muyaya.
8Adayendera mizinda ya ku Yuda,
naononga okana chipembedzo.
Motero adaletsa mkwiyo wa Mulungu
kuti usaŵagwere Aisraele.
9Dzina lake lidamveka
mpaka ku malekezero a dziko lapansi,
ndipo adasonkhanitsa amene anali otayika.
Nkhondo zoyamba za Yudasi Makabeo10Apoloniyo adasonkhanitsa ankhondo a akunja ndi chinamtindi cha anthu a ku Samariya, kuti akamenye nkhondo ndi Aisraele.
11Yudasi atamva zimenezo, adadzakumana naye, ndipo adamgonjetsa, namupha. Adani ambiri adaphedwa, ena nkuthaŵa.
12Ayuda adalanda chuma chao, ndipo Yudasi adatenga lupanga la Apoloniyo namamenyera nkhondo limenelo pa moyo wake wonse.
13Seroni, wolamulira ankhondo a ku Siriya, adazimva zoti Yudasi wasonkhanitsa gulu la anthu omkhulupirira ndi odziŵa kumenya nkhondo.
14Tsono Seroniyo adati, “Ndidzabukitsa dzina langa kuti ndiwone ulemu m'dziko. Ndidzamenyana nkhondo ndi Yudasi ndiponso ndi anthu ake amene amanyoza malamulo a mfumu.”
15Choncho iyenso adanyamuka, ndipo pamodzi naye gulu lalikulu lankhondo la anthu oletsa chipembedzo lidabwera kudzalipsira pa ana a Israele.
16Anthuwo atafika pafupi ndi phiri la Betoroni, Yudasi adapita ndi anthu oŵerengeka kukakumana nawo.
17Anthu ake ataona gulu lalikulu lankhondo likuŵafika pafupi, adafunsa Yudasi kuti, “Kodi ife oŵerengekafe tingamenye bwanji nkhondo ndi gulu lalikulu chotere? Kuwonjezera apo, ndife olefuka kwambiri, popeza kuti sitidadye kanthu lero.”
18Apo Yudasi adayankha kuti, “Kugonjetsa gulu lalikulu ndi anthu oŵerengeka mwina nkwapafupi. Kwa Mulungu kubweretsa chipulumutso ndi anthu ambiri kapena oŵerengeka nchimodzimodzi.
19Pajatu anthu sapambana ku nkhondo chifukwa cha unyinji wa ankhondo ao, koma chifukwa cha mphamvu zochokera kwa Mulungu.
20Adani athuwo akudzatithira nkhondo monyada kwambiri ndi monyoza za Mulungu, kuti atiwononge ifeyo, akazi athu ndi ana athu, ndiponso kuti atilande zathu zonse.
21Koma ife timenya nkhondo kuti tipulumutse moyo wathu ndi kusunga chipembedzo chathu.
22Ndithu Mulungu aŵatswanya ife tikuwona. Ndiye inu musachite nawo mantha ai.”
23Atatha kulankhula, pompo adadudukira Seroni ndi ankhondo ake, nkuŵathyoleratu onse.
24Adaŵalondola ku phiri la Betoroni mpaka ku chigwa. Adaphapo mazana asanu ndi atatu, opulumuka adathaŵira ku dziko la Afilisti.
25Choncho m'madera onse ozungulira, anthu a mitundu ina adayamba kuwopa Yudasi ndi abale ake, ankanjenjemera nkumada nkhaŵa.
26Mfumu nayonso idamva mbiri ya Yudasi, ndipo anthu a mitundu ina ankakamba za nkhondo za Yudasi.
Mfumu ituma Lisiyasi kukalamulira dziko la Ayuda27Atamva zimenezi, mfumu Antioko adapsa mtima kwambiri. Ndipo adalamula kuti asonkhanitse ankhondo onse a m'dziko lake lonse, kupanga gulu lalikulu.
28Tsono adatsekula mosungira chuma chake, napatsa ankhondo ake malipiro a chaka chimodzi. Adaŵalamula kuti akhale okonzeka kukamenya nkhondo kulikonse.
29Pamenepo adaona kuti chuma chake chatha, ndiponso msonkho wa m'dziko mwake watsika, chifukwa cha chisokonezo ndi masautso zomwe iyeyo adazidzetsa, pothetsa malamulo amene anthu adaaŵazoloŵera ndi kuŵatsata chikhalire.
30Pomwepo adayamba kuda nkhaŵa kuti alephera kupeza ndalama zonga zimene anali nazo kale, zogulira zosoŵa zake, ndi zogulira mphatso zimene ankangopatsa anthu mosakaza, kupambana mafumu amene analipo kale.
31Zimenezi adavutika nazo kwambiri mu mtima, motero adatsimikiza zopita ku Persiya, kuti akakhometse msonkho m'madera akumeneko, kuti potero adzapeze ndalama zambiri.
32Adapatsa Lisiyasi, munthu wina wotchuka wa m'banja la mfumu, udindo wolamulira dziko, kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku malire a Ejipito.
33Adamuikanso kuti akhale wophunzitsa mwana wake Antioko mpaka iye atabwerako.
34Adampatsanso hafu la asilikali ankhondo, pamodzi ndi njovu zake. Adamlamulanso kuti akachite zonse zimene iye yemwe adaafuna kuzichita. Za anthu a ku Yudeya ndi a ku Yerusalemu,
35Antioko adauza Lisiyasi kuti adzatume gulu lankhondo kukatswanya ndi kuwononga Aisraele ndi onse otsala ku Yerusalemu, mpaka kufafaniziratu dzina lao.
36Adamuuzanso kuti adzakhazike anthu achilendo m'dziko limenelo, nkuŵagaŵira minda yonse pochita maere.
37Tsono mfumu itatenga hafu lina la gulu lankhondo, idachoka ku Antiokeya, mzinda wake waukulu, pa chaka cha 147, niwoloka mtsinje wa Yufurate nkubzola zigawo za dziko zakumpoto.
Gorjiyasi ndi Nikanore38Lisiyasi adasankhula Ptolemeyo, mwana wa Dorimene, Nikanore ndi Gorjiyasi, anthu atatu olimba mtima, abwenzi a mfumu.
39Iwoŵa adaŵatuma pamodzi ndi ankhondo oyenda pansi 40,000 ndi okwera pa akavalo 7,000, kuti akalande dziko la Yudeya ndi kuliwononga monga momwe mfumu idaalamulira.
40Iwowo adapita ndi ankhondo ao onse, nakafika pafupi ndi Emausi ku chigwa, nkumangako zithando zao zankhondo.
41Amalonda a m'dziko limenelo atamva zimenezo, adatenga siliva ndi golide wambiri ndi maunyolo. Adabwera nazo ku zithando zankhondo za adaniwo, kuti adzaguleko ana a Aisraele nkuŵasandutsa akapolo. Magulu ankhondo a ku Siriya ndi a ku dziko la Afilisti adatsagana nawo.
42Yudasi ndi abale ake adaona kuti zovuta zaŵachulukira, ndipo kuti ankhondo a adani ao aloŵeratu m'dziko lao. Adamvanso za lamulo la mfumu lakuti aononge ndi kufafaniza mtundu wa Aisraele.
43Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni timangenso mtundu wathu woonongekawu, ndipo tichite nkhondo kumenyera mtundu wathu ndi malo athu oyera.”
44Pamenepo anthu onse adasonkhana kuti akonzekere nkhondo, ndi kuchita mapemphero opempha chifundo cha Mulungu.
45Yerusalemu anali wopanda anthu ngati
chipululu,
panalibe ndi mmodzi yemwe mwa ana ake
woloŵamo kapena kutulukamo.
Malo ake oyera adaaponderezedwa.
Alendo adaalanda nsanja yake yankhondo,
ndipo anthu akunja adaakhazikika m'menemo.
Kunalibenso chimwemwe kwa Aisraele,
zitoliro ndi zeze sizinkamvekanso.
Ayuda asonkhana ku Mizipa46Ayuda adasonkhana ku Mizipa, kuyang'anana ndi Yerusalemu, chifukwa kale kumeneko nkomwe kunali malo opembedzerako Aisraele.
47Pa tsikulo adasala zakudya, adavala ziguduli, nkudzithira phulusa ku mutu. Zovala adang'amba kuwonetsa chisoni.
48Adafutukula buku la Malamulo, kuti apezemo chiwongolero cha Mulungu, monga ankachitira akunja pa zotere, kupempha nzeru kwa milungu yao.
49Adabwera ndi zovala zaunsembe, zipatso zoyambirira kucha ndi zopereka zachikhumi, naitana Anaziri amene anali atatsiriza masiku a malonjezo ao.
50Tsono adapemphera mokweza mau kwa Mulungu kuti:
“Kodi tichite nawo chiyani Anaziri ameneŵa?
Tipite nawo kuti?
51Malo anu oyera adaponderezedwa ndi kuipitsidwa,
ansembe anu akungolira ali ndi manyazi aakulu.
52Taonani, anthu a mitundu ina asonkhana kuti atiwononge.
Inu mukudziŵa zimene apangana kuti atichite.
53Ifeyo tingalimbane nawo bwanji,
Inu mukapanda kutithandiza?”
54Tsono adaliza malipenga, ndipo kudamveka mfuu waukulu.
55Pambuyo pake Yudasi adasankhula atsogoleri a anthu, ena oyang'anira magulu a anthu zikwi, ena magulu a anthu mazana, ena magulu a anthu makumi asanu, ena magulu a anthu khumi.
56Deut. 20.5-8; Owe. 7.3Potsata lamulo, adauza anthu amene ankamanga nyumba kumene, kapena amene anali atakwatira chatsopano, kapena amene anali atabzala munda wamphesa watsopano, kapenanso wina aliyense wa mtima wamantha, adaŵauza kuti abwerere kwao.
57Tsono gulu lankhondo lidanyamuka, lidakamanga zithando zankhondo kumwera kwa Emausi.
58Yudasi adaŵauza kuti, “Valani dzilimbe ndipo mulimbe mtima. Mukhale okonzeka kuti m'mamaŵa timenyane nkhondo ndi magulu a anthu a mitundu inaŵa amene asonkhana kuti atiwononge pamodzi ndi malo athu oyera.
59Chifukwatu ndi bwino kuti tifere pa nkhondo, kupambana kuti tiwone zovuta zodzagwera mtundu wathu ndi malo athu oyera.
60Koma zonse zichitika monga m'mene afunire Mulungu.”
Nkhondo ya ku EmausiWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.