2 Am. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Simoni uja, amene adaulula za chuma chija nkuukira dziko lake lomwe, ankasinjirira Oniyasi. Ankati ndiye amene adaanyenga Heliodoro namchititsa zoipa zonse zija.

2Tsono Oniyasiyo, amene ankachitira mzinda zaufulu, namateteza anthu a m'dziko lake, ndi kusunga bwino Malamulo a Mulungu, Simoni uja sadaope kumneneza kuti ndi munthu woukira boma.

3Chidani chake chidakula kotero kuti mmodzi mwa abwenzi a Simoniyo adapha anthu ena.

4Pamenepo Oniyasi adaona kuti chidanicho chinali choopsadi, ndipo kuti Apoloniyo mwana wa Menesiteo, bwanamkubwa wa ku Celesiriya ndi ku Fenisiya, ankakwerezera njiru ya Simoni.

5Tsono adanka kwa mfumu, osati kuti akaneneze anthu a m'dziko lake, koma chifukwa chofuna ubwino wa onse pamodzi ndi wa aliyense.

6Iye adaamvetsa bwino kuti popanda chigamulo cha mfumu, kunali kosatheka kuti mtendere uwonekenso kapena kuti Simoni aleke makhalidwe ake openga.

7 1Am. 1.10 Seleuko uja atafa, Antioko Epifane adaloŵa ufumu wake. Tsono Yasoni, mbale wa Oniyasi, adalanda udindo wa mkulu wa ansembe popereka chiphuphu.

8Adanka kwa mfumu nailonjeza kuti adzaipatsa makilogramu 12,000 asiliva ndi makilogramu ena 2,700 ochokera kwina.

9Adalonjezanso kuti adzapereka makilogramu ena 5,000, ngati adzamloleza kumanga sukulu yophunzitsa maseŵera osiyanasiyana ndi kukhazikitsa gulu la achinyamata, kenaka kulemba anthu a ku Yerusalemu kuti asanduke nzika za ku Antiokeya.

10Mfumu idavomera, ndipo Yasoni chifukwa cha udindo wake, adayamba kuphunzitsa anthu am'dzikomo makhalidwe achigriki.

111Am. 8.17Adafafaniza zilolezo zachifundo zimene mafumu adaapatsa Ayuda chifukwa cha Yohane, bambo wa Eupoleme, amene adaamtuma kwa Aroma kuti akachite nawo chipangano cha chigwirizano ndi cha chibwenzi. Yasoniyo adathetsa miyambo yotsata Malamulo, nayambitsa miyambo ina yotsutsana ndi Malamulowo.

12Sadaope kumanga sukulu yophunzitsa maseŵera ija pansi pa boma lankhondo, ndipo adachita zoti anyamata a mabanja aulemu aziphunzirako miyambo Yachigriki.

13Tsono Chigriki chidabuka, ndipo ambiri adayamba kutsata miyambo yachilendo, chifukwa cha kuipa kwakukulu kwa Yasoni uja, amene anali munthu wosasamala za Mulungu ndi wosayenera kukhala mkulu wa ansembe mpang'ono pomwe.

14Pakati pa zoipa zonsezi ansembe nawonso adayamba kuleka changu chogwira ntchito zapaguwa. Adanyoza Nyumba ya Mulungu, nalekanso kupereka nsembe. Koma ankati akangomva chingerengere choitana anthu ku maseŵera, iwo ndiye liŵiro kuthamangira komweko kukachita nawo maseŵerawo.

15Adaaleka kusamala zaulemu za makolo ao, koma ankangokonda ulemu Wachigriki.

16Nchifukwa chake adapeza zovuta kwambiri. Anthu aja amene ankaŵatsanzira makhalidwe ao, nafuna kuti afanefane nawo, omwewo adasanduka adani ao oŵalanga.

17Zoonadi, munthu sanganyoze Malamulo a Mulungu popanda kulangidwa konse. Motero zimene zidachitika pambuyo pake zidatsimikizadi mau ameneŵa.

18Nthaŵi ina ku Tiro kunali maseŵera a pa chaka chachisanu chilichonse, ndipo mfumu inali komweko.

19Tsono Yasoni woipa uja adatuma nthumwi kumeneko kuchokera ku Yerusalemu, zolembedwa ngati nzika za ku Antiokeya. Zidatenga makilogramu 10,000 a siliva kukalipirira nsembe zopereka kwa Herkulesi. Koma onyamula ndalamazo adaganiza zoti asaperekere nsembe ndalamazo, chifukwa kunali kulakwa kutero, tsono adaganiza zoti achitire zinthu zina.

20Motero ndalama zimene eni ake oŵatuma adaafuna kuti aperekere nsembe kwa Herkulesi, iwo adapangira zombo zankhondo.

21Apoloniyo, mwana wa Menesiteo, atamtuma ku Ejipito kuti akaonerere nao mwambo wokhazika mfumu Filometore pa mpando, Antioko adamva kuti mfumuyo sinkaukonda ufumu wa Menesiteo. Tsono iye adaganiza zodziteteza, motero atafika ku Yopa, adapitirira mpaka ku Yerusalemu.

22Yasoni adamlandira mwaulemu, pamodzi ndi anthu onse amumzindamo. Pomulandira anthu adayatsa miyuni, namaimba nyimbo zomulemekeza. Pambuyo pake Antioko adapita ku Fenisiya ndi gulu lake lankhondo.

Menelasi asautsa Ayuda abale ake

23Patapita zaka zitatu, Yasoni adatuma Menelasi, mbale wa Simoni uja, kuti akapereke ndalama kwa mfumu, ndi kukampempha kuti apereke chigamulo pa nkhani zina zikuluzikulu.

24Koma Menelasi atadzaima pamaso pa mfumu adaikoka mtima ndi maonekedwe ake aulamuliro, ndipo adalanda Yasoni udindo wake wokhala mkulu wa ansembe onse popereka kwa mfumu makilogramu 10,000 a siliva kuposa ndalama zija zimene adaapereka Yasoni.

25Atalandira makalata kwa mfumu otsimikizira ukuluwo adabwerera ku Yerusalemu. Analibe kanthu kalikonse komuyenereza kukhala mkulu wa ansembe onse, koma anali ndi makhalidwe a munthu wankhalwe ndi waukali ngati chilombo.

26Choncho Yasoni amene adaalanda ukulu wa mbale wake, nayenso wina adamlanda, ndipo adathaŵira ku dziko la Aamoni.

27Tsono Menelasi adakhala mkulu wa ansembe, koma sankapereka ndalama zija zimene adaalonjeza kwa mfumu.

28Komabe Sositrate, mkulu wolamulira ku boma lankhondo, ankamulonjerera kuti alipire, malinga nkuti inali ntchito yake kukhometsa msonkho. Choncho mfumu idaŵaitana onse aŵiriwo.

29Menelasi adasiyira mbale wake Lisimake ngati mbadiri wake pa ntchito ya ukulu wa ansembe, ndipo Sositrate adasiyira Krate, mkulu wa ankhondo a ku Kipro ngati mbadiri wake.

30Nthaŵi imeneyo anthu a ku Tariso ndi a ku Malusi adachita chiwembu, chifukwa choti mfumu idaapereka mizinda yao iŵiriyo kwa Antiokisi, mzikazi wake.

31Mfumu idapita mofulumira kuti ikaweruze milanduyo, nisiya ngati mbadiri wake Androniko, mmodzi mwa akuluakulu.

32Menelasi adaaganiza kuti imeneyo ndiyo inali nthaŵi yabwino. Choncho adaba ziŵiya zina zagolide ku Nyumba ya Mulungu, nazipereka kwa Androniko ngati mphatso. Zina anali atazigulitsa kale ku Tiro ndi ku mizinda ina pafupi pake.

33Oniyasi atamva zimenezo, adakabindikira m'malo opulumukiramo ku Dafine, pafupi ndi ku Antiokeya, ndipo adadzudzula Menelasi poyera.

34Dan. 9.26Nchifukwa chake Menelasi adatenga Androniko paseri, namuuza kuti aphe Oniyasi. Tsono Androniko adapita kwa Oniyasi namunyengerera kuti akungofuna kugwirako dzanja lake lamanja, nalumbira za mtendere. Ngakhale Oniyasi ankapenekabe mu mtima, adavomera kutulukako kumene ankabindikira kuja, ndipo Androniko adamupha pomwepo, osasamala za chilungamo.

35Nchifukwa chake si Ayuda okha, komanso anthu ambiri a maiko ena adamva chisoni nakhumudwa chifukwa cha kupha munthu wotere popanda chilungamo.

36Motero mfumu itabwerera kuchokera ku Silisiya, Ayuda a ku Antiokeya ndi Agriki ena odana ndi makhalidwe ankhalwe, adafika kwa mfumu naidandaulira za imfa ya Oniyasi, amene adaphedwa popanda chifukwa.

37Antioko adamva chisoni mumtima mwake navutika kwambiri, ndipo adalira misozi pokumbukira makhalidwe ofatsa ndi nzeru za munthu wakufayo.

38Ali wopsa mtima kwambiri, adamlanda Androniko mwinjiro wake wofiirira, namung'ambira zovala zake. Adayenda naye mu mzinda monsemo mpaka kukafika pamalo pomwe adaaphera Oniyasi. Ndipo pomwepo, adamupha munthu wokhetsa magaziyo. Choncho Ambuye adamlanga monga momwe kudamuyenera.

39Masiku amenewo Lisimake uja adaba zinthu zambiri za m'Nyumba ya Mulungu mumzindamo, mbale wake Menelasi nkumamuthandiza. Mbiri imeneyo itamveka, anthu adasonkhana nkumuukira Lisimakeyo chifukwa ziŵiya zambiri zagolide zinkasoŵa.

40Ataona ukali ndi unyinji wa omuukirawo, Lisimake adapatsa anthu 3,000 zida zankhondo, naŵalamula kuti akaŵathire nkhondo Ayudawo. Mtsogoleri wa asilikaliwo anali munthu wina dzina lake Aurano, wa zaka zambiri ndi wopusanso kwambiri.

41Koma Ayuda adaadziŵa kuti nkhondoyo yachokera kwa Lisimake, ena adatola miyala, ena adatenga mitengo, enanso ngakhale phulusa lomwe linali pomwepo, zonsezo nkumamuponya Lisimake ndi ankhondo ake; motero padachitika chisokonezo chachikulu.

42Adalasa adani ambiri, ena nkuŵapha, ndipo ena onse adathaŵa. Ngakhale Lisimakeyo, amene adaaba zinthu zoyera, adamupha pafupi ndi chipinda cha bokosi la chuma.

43Tsono mlanduwo adausenzetsa Menelasi.

44Pamene mfumu idadza ku Tiro, anthu atatu amene akuluakulu adaŵatuma, adabwera kudzamuimba mlandu.

45Atadziŵiratu kuti mlandu umuipira, Menelasi adalonjeza kwa Ptolemeyo, mwana wa Dorimene, kuti adzampatsa ndalama zambiri ngati amnenerako zabwino kwa mfumu.

46Tsono Ptolemeyo adatengera mfumu pambali m'khonde, ngati kuti akufuna kukapumula mozizira, ndipo adachita zoti mfumu isinthe maganizo.

47Tsono mfumu idagamula kuti Menelasi ngwosapalamula konse, chonsecho amene adaayambitsa zoipa ndi iyeyo. Kenaka idagamula kuti aphedwe anthu aja amene adaatulutsa mlandu. Koma tsono anthu opanda mwaiwo akadadandaula kwa Asiti ankhalwe aja, bwenzi iwo atagamula kuti ngosapalamula.

48Motero anthuwo, amene adaafuna kuteteza mzinda ndi anthu ake ndiponso zinthu zoyera, adaphedwa choncho mofulumira popanda cholakwa konse.

49Tsono anthu a ku Tiro adanyansidwa nacho choipacho, ndipo adapereka chuma chao kuti anthu akufawo aikidwe mwaulemu kwambiri.

50Koma Menelasi uja sadamchotse pa udindo wake, poti akukuakulu olamulira m'dzikomo ankakonda chuma kwambiri. Kuipa kwake kudanka kukulirakulira, mpaka adasanduka mdani wamkulu wa anthu a mtundu wake.

Anthu aona nkhondo m'masomphenya
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help