1Litatha phwando lachikondwerero, Tobiti adaitana Tobiyasi mwana wake, namuuza kuti, “Mwana wanga, usalephere kumpatsa malipiro munthu amene adaapita nawe uja, ndipo uwonjezepo kanthu pa malipirowo.”
2Iye adayankha kuti, “Atate, ndingatani kumlipira kwake pa chithandizo chonse chimene adandipatsa? Ngakhale nditampatsako hafu la chuma chimene adabwera nacho pamodzi ndi ine, sindikutayapo kanthu.
3Wadzanditulanso kuno ndili bwino, adachiritsa mkazi wanga, wabwera nazo ndalama zija, ndipo inunso wakuchiritsani. Kodi ndimpatse malipiro otani pa zonsezi?”
4Tobiti adayankha kuti, “Mwana wanga, potsata chilungamo, akuyenera ndithu kulandira hafu la zonse zimene wabwera nazo kuno.”
5Motero Tobiyasi adaitana mnzakeyo namuuza kuti, “Nali theka la zonse zimene wafika nazo kuno. Zimenezi zikhale malipiro ako. Ukagone kutali ndi moto.”
6Koma Rafaele adaitana aŵiriwo pambali, naŵauza kuti, “Yamikani Mulungu ndi kumthokoza pamaso pa amoyo onse, chifukwa cha zabwino zimene wakuchitirani. Mulemekeze ndi kutamanda dzina lake. Mulalike kwa anthu onse ntchito zonse za Mulungu monga kuyenera. Muzimthokoza nthaŵi zonse, osatopera.
7Nkwabwino kubisa chinsinsi cha mfumu, koma nkwabwinonso kuulula ndi kulalika ntchito za Mulungu monga kuyenera. Muzichita zabwino, ndipo zoipa sizidzakugwerani.
8 Mphu. 29.8-13 “Kupemphera kophatikizana ndi kusala zakudya, ndipo kuthandiza osauka kophatikizana ndi chilungamo, nkwabwino kwambiri koposa kukhala ndi chuma koma wosalungama. Kuli bwino kwambiri kuthandiza osauka kupambana kudziwunjikira golide.
9Miy. 11.4; Dan. 4.27; Mphu. 3.30Ntchito zothandiza osaukazo zimapulumutsa ku imfa ndi kufafaniza machimo. Amene amathandiza osauka, adzakhala ndi moyo wosefukira.
10Koma amene amachimwa ndi kuchita zoipa amadziitanira zovuta.
11“Ndikuululirani zonse monena zoona, sindikubisirani kanthu. Paja ndakuuzani kuti nkwabwino kubisa chinsinsi cha mfumu, koma nkofunikanso kulalika ntchito za Mulungu ndi kuzitamanda mwaulemu.
12Yob. 33.23, 24; Ntc. 10.4; Chiv. 8.3, 4Pa nthaŵi ija imene iwe Tobiti ndi Sara munkapemphera, ndine amene ndinkapereka mapemphero anu pamaso pa Ambuye aulemerero, chimodzimodzinso pamene unkaika akufa m'manda.
13Pamene unkachoka podyera ndi kusiya chakudya chako popanda kupeneka konse, kuti ukaike munthu wina wakufa, Mulungu adaandituma kuti ndidzakuyese.
14Koma pambuyo pake Mulungu wanditumanso kuti ndidzakuchiritse, iwe pamodzi ndi mpongozi wako Sara.
15Zek. 4.10; Lk. 1.19; Chiv. 8.2Ine ndine Rafaele, mmodzi mwa Angelo asanu ndi aŵiri amene nthaŵi zonse amakhala pamaso pa Mulungu waulemerero, kukonzekera kuti amtumikire.”
16Pamenepo aŵiriwo adachita mantha nadzigwetsa moŵerama pansi ali njenjenje.
17Koma Mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, khalani ndi mtendere! Muyamike Mulungu nthaŵi zonse!
18Ine ndakhala nanu osati mwa kufuna kwa ine ndekha, koma mwa kufuna kwa Mulungu. Tsono muyamikeni Iyeyo nthaŵi zonse ndi kumuimbira nyimbo.
19Mwandiwona ndilikudya, koma mwangoona maonekedwe okha.
20Ndipo tsopano yamikani Ambuye pansi pano ndi kuthokoza Mulungu. Ine ndikubwerera kumwamba, kwa amene adandituma. Lembani zimene zakuwonekeranizi.”
21Atatero, Rafaeleyo adakwera kumwamba. Iwo adaimirira, koma sadathe kumpenyanso.
22Tsono adayamika Mulungu pakumuimbira nyimbo ndi kumuthokoza chifukwa cha ntchito zazikulu zonse zimene adazichita pakuŵatumizira Mngelo wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.