1Yeremiya atatsiriza kuuza anthu zonse zimene Chauta Mulungu wao adamtuma kuti akaŵauze,
2Azariya mwana wa Hesaya, Yohanani mwana wa Kareya, ndiponso anthu onse achipongwe, adauza Yeremiya kuti, “Iwe ukunama. Chauta Mulungu wathu sadakutume kudzanena kuti, ‘Musapite ku Ejipito kukakhala kumeneko.’
3Baruki mwana wa Neriya ndiye wakukakamiza kuti utiletse, ndipo kuti tigwe m'manja mwa Ababiloni, kuti atiphe kapena kutitenga ukapolo kupita ku Babiloni.”
4Tsono Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, adakana kumvera Chauta ndipo sadakhale ku Yuda.
52Maf. 25.26 Choncho Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, adatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene adabwerera kuchokera ku maiko kumene adaabalalikira kuti akakhale ku Yuda.
6Anthuwo anali aŵa: amuna, akazi ndi ana, kuphatikizapo ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu onse amene Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo adaaŵasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya.
7Onsewo adapita nawo ku Ejipito monyoza mau a Chauta, nakafika ku Tapanesi.
Yeremiya aneneratu kuti Nebukadinezara adzagonjetsa Ejipito8Chauta adalankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi. Adamuuza kuti,
9“Tenga miyala ina yaikulu, uikwirire m'dothi pa chiwundo cha poloŵera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Ayuda akuwone ukuchita zimenezo.
10Tsono uŵauze kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ndidzaitana mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaika mpando wake pa miyala imene ndaibisa apoyo. Ndipo adzafunyulula hema lake laufumu pa miyalayo.
11Adzabwera kudzaononga Ejipito, adzatumiza mliri pa anthu oyenera kufa ndi mliri, adzatenga ukapolo anthu oyenera kutengedwa ukapolo, ndipo adzaŵapha ndi lupanga oyenera kuphedwa ndi lupanga.
12Adzasonkha moto m'nyumba za milungu ya ku Ejipito. Adzatentha nyumbazo, ndipo milunguyo adzaitenga kupita nayo ku ukapolo. Adzayeretsa dziko la Ejipito monga momwe mbusa amamangira chovala chake m'chiuno, momwemonso ndimo adzaŵachitire Aejiptio ndipo adzachoka ku Ejipito osaona vuto lililonse.
13Adzaphwanya zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzeramo mulungu wa dzuŵa ku Ejipito. Ndipo adzatentha nyumba za milungu ya ku Ejipito.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.