1Chauta adauza Mose kuti,
2“Ulamule Aisraele, uŵauze kuti, ‘Posachedwa muloŵa m'dziko la Kanani, (dziko limenelo ndilo lidzakhala choloŵa chanu, dziko lonse la Kananilo).
3Chigawo chakumwera cha dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini kulambalala malire a Edomu. Malire anu akumwera ayambira kuvuma, kumathero a Nyanja ya Mchere.
4Malire anuwo apite kumwera, ndipo akwere phiri la Akarabimu ndi kuwolokera ku Zini. Mathero ake akhale kumwera kwa Kadesi-Baranea. Tsono apitirire mpaka ku Hazaradara, ndipo alambalale kukafika ku Azimoni.
5Malirewo akhotere ku Azimoni ndi kumapita ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo akathere ku Nyanja.’
6“Malire anu akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu ndi gombe lake. Ameneŵa ndiwo malire akuzambwe.
7“Malire anu akumpoto ndi aŵa, mulembe malire kuyambira ku Nyanja yaikulu mpaka ku phiri la Hori.
8Kuchokera ku phiri la Horiko, mulembe malire kufikira ku chipata cha Hamati, ndipo mathero a malirewo akhale ku Zedadi.
9Tsono malirewo afike mpaka ku Zifuroni, ndipo mathero ake akhale ku Hazarenani.
10“Mulembe malire anu akuvuma kuyambira ku Hazarenaniko mpaka ku Sefamu.
11Atsike kuchokera ku Sefamu mpaka ku Ribula, kuvuma kwa Aini. Atsikebe mpaka ku gombe la Nyanja ya Galilea, kuvuma,
12atsike ndithu mpaka ku mtsinje wa Yordani, ndipo akathere ku Nyanja ya Mchere. Limeneli ndilo dziko lanu pamodzi ndi malire ake ozungulira dzikolo.”
13 Num. 26.52-56 Yos. 14.1-5 Mose adalamula Aisraele kuti, “limeneli ndilo dziko limene mudzalandira mwamaere kuti likhale choloŵa chanu, limene Chauta walamula kuti lipatsidwe kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka.
14Fuko la ana a Rubeni mwa mabanja a makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi mwa mabanja a makolo ao, pamodzi ndi theka la fuko la Manase, adalandira kale choloŵa chao.
15Mafuko aŵiriwo ndi thekalo adalandira kale choloŵa chao patsidya pa mtsinje wa Yordani ku Yeriko chakuvuma kotulukira dzuŵa.”
Atsogoleri ogaŵa dziko16Chauta adauza Mose kuti,
17“Maina a anthu amene adzakugaŵireni dzikolo kuti likhale choloŵa chanu, ndi wansembe Eleazara ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse, kuti agaŵe dzikolo ngati choloŵa.
19Maina a anthuwo naŵa: M'fuko la Yuda akhale Kalebe mwana wa Yefune.
20M'fuko la ana a Simeoni akhale Semuele mwana wa Amihudi.
21M'fuko la Benjamini akhale Elidadi mwana wa Kisiloni.
22M'fuko la ana a Dani akhale Buki mwana wa Yogili.
23Mwa ana a Yosefe, m'fuko la ana a Manase akhale Haniyele mwana wa Efodi.
24M'fuko la ana a Efuremu akhale Kemuwele mwana wa Sifutani.
25M'fuko la ana a Zebuloni akhale Elizafani mwana wa Paranaki.
26M'fuko la ana a Isakara akhale Palatiele mwana wa Azani.
27M'fuko la ana a Asere akhale Ahihudi mwana wa Selomi.
28M'fuko la ana a Nafutali akhale Pedahele, mwana wa Amihudi.
29Ameneŵa ndiwo amene Chauta adalamula kuti agaŵe choloŵa cha Aisraele m'dziko la Kanani.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.