1Uwu ndi uthenga umene mneneri Habakuku adalandira kwa Mulungu m'masomphenya.
Dandaulo loyamba la Habakuku2Kodi Inu Chauta,
ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo
nthaŵi yaitali bwanji,
Inuyo osandiyankha?
Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,”
Inuyo osatipulumutsa?
3Chifukwa chiyani mukufuna
kuti ndiziwona mavuto otereŵa.
Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa?
Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo.
Pali ndeu ndi kukangana kwambiri.
4Ndiye kuti malamulo atha mphamvu.
Chilungamo sichikugwira ntchito.
Anthu oipa akupambana anthu abwino,
motero chilungamo chalephereka.
Yankho la Chauta5 Ntc. 13.41 Onani mitundu ya anthuyi, muipenyetsetse.
Kudzakhala zododometsa ndipo mudzangoti kakasi.
Pakuti ndidzachita zinthu
zimene simudzakhulupirira mukadzazimva.
6 2Maf. 24.2 Ndiye kuti ndidzakweza Ababiloni
mtundu woopsa ndi wamphamvu.
Iwowo amapita pa dziko lonse lapansi
kuti akalande malo a eniake.
7Kulikonse kumene amapita, amachititsa mantha,
amadzipangira okha malamulo,
amadzipezera okha ulemu.
8Akavalo ao ndi aliŵiro kwambiri kupambana akambuku,
ndi oopsa kupambana mimbulu yolusa.
Okwerapo ao akuthamanga molunjika kuchokera kutali.
Akuchita kugudukira ngati chiwombankhanga
chofuna kugwira nyama.
9Gulu lao lankhondo likubwera ndi nkhanza,
anthu akuchita mantha iwo asanafike.
Amagwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
10Amanyoza mafumu,
amanyazitsa atsogoleri.
Amapeputsa linga lililonse,
poti amangounjika dothi lokwererapo,
nalanda mzinda wake.
11Kenaka amapitirira mofulumira ngati mphepo.
Anthuwo amene mphamvu ndiye mulungu wao.
Dandaulo lachiŵiri la Habakuku12Inu Chauta, kodi suja ndinu wachikhalire?
Ndinu Mulungu wanga, Woyera wanga uja, wosafa.
Inu Chauta, ndinu amene mudaŵasankha anthuwo
kuti abweretse chiweruzo pa ife.
Inu Thanthwe lathu, mudaŵaika iwowo kuti atilange.
13Maso anu ndi oyera, safuna kuwona zoipa,
simungalekerere anthu ochita uchimo ndi zolakwa.
Chifukwa chiyani nanga mukulekerera
anthu osakhulupirikawo?
Bwanji simuchitapo kanthu
pamene anthu oipa akuwononga anthu abwino
kupambana iwowo?
14Mumasandutsa anthu kuti azikhala
ngati nsomba zam'nyanja,
ngati zokwaŵa zimene zilibe wozilamulira?
15Adani ao amachita ngati kuŵedza anthuwo ndi mbedza,
kapena kuŵakola m'kombe.
Amaŵakokera m'matchera ao,
ndipo amakondwa ndi kusangalala.
16Tsono amaperekera nsembe makombe ao,
ndipo amafukizira lubani matchera ao.
Chifukwa zimenezi ndizo zimaŵabweretsera
moyo wapamwamba, ndipo amadya bwino.
17Kodi adzapitirirabe kugwiritsa ntchito makoka ao,
ndi kumapha mitundu ya anthu mopanda
chifundo mpakampaka?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.