1 Ntc. 4.25, 26 Bwanji anthu akunja
akufuna kuchita chiwembu?
Chifukwa chiyani anthu ameneŵa
akulingalira zopandapake?
2Mafumu ao akuchita upo,
olamula ao akhala pamodzi kuti apangane zoipa,
zoukira Chauta ndi mfumu yake yodzozedwa.
3Akuti,
“Tiyeni timasule maunyolo aoŵa,
tichokeretu mu ulamuliro wao.”
4Chauta amene amalamulira kumwambako
akungoŵaseka ndi kuŵanyoza.
5Tsono adzaŵadzudzula ali wokwiya
adzaŵaopseza ali wokalipa.
6Adzati,
“Ine ndakhazika kale mfumu yanga,
ili pa phiri langa loyera la Ziyoni.”
7 Ntc. 13.33; Ahe. 1.5; 5.5 Tsono mfumuyo ikuti,
“Ndidzalalika zimene Chauta walengeza.
Adandiwuza kuti,
‘Iwe ndiwe mwana wanga,
Ine lero ndakubala.
8Tandipempha uwone,
ndidzasandutsadi mitundu ya anthu
kuti ikhale choloŵa chako,
ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala lako.
9 Chiv. 2.26, 27; 12.5; 19.15 Udzaŵaphwanya ndi ndodo yachitsulo,
ndi kuŵatekedza zidutswazidutswa monga mbiya.’ ”
10Nchifukwa chake tsono khalani anzeru,
inu mafumu.
Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi.
11Tumikirani Chauta mwamantha ndi monjenjemera.
12Mumgonjere molapa,
kuwopa kuti angakukwiyireni,
ndipo inu mungaonongeke,
chifukwa ukali wake umayaka msanga.
Ngodala onse amene amathaŵira kwa Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.