1 2Maf. 14.25 Tsiku lina Chauta adapatsa Yona, mwana wa Amitai, uthenga uwu wakuti,
2“Nyamuka, upite ku Ninive, mzinda waukulu uja. Ukaŵadzudzule momveka ndithu anthu chifukwa ndaona kuipa kwao.”
3Koma Yona pofuna kuthaŵa Chauta, adanyamuka nkumapita ku Tarisisi. Adapita ku mzinda wa Yopa, kumene adapeza chombo chopita ku Tarisisi. Adagula tikiti naloŵa m'chombomo, kuti apite nao ku Tarisisi, kuti choncho athaŵe Chauta.
4Koma Chauta adautsa namondwe, ndipo nyanja idayamba kuŵinduka kwambiri ndi namondweyo, kotero kuti chombo chinali pafupi kuwonongeka.
5Amalinyero adachita mantha, aliyense nkumalirira mulungu wake. Adayamba kuponya katundu m'nyanja kuti chombo chipepuke. M'menemo nkuti Yona atatsikira m'katikati mwa chombo, ali m'tulo tofa nato.
6Tsono kaputeni wa chombo adafika kwa Yona uja namufunsa kuti, “Kodi iwe, nchiyani chimenechi? Monga iwe nkumagona eti? Dzuka, utame kwa Mulungu wako mopemba, mwina nkuwona watithandiza kuti tisamire.”
7Amalinyerowo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tichite maere kuti tipeze amene wabweretsa masoka ameneŵa.” Choncho adachitadi maerewo, ndipo adagwera Yona.
8Tsono adamufunsa kuti, “Tatiwuza, masoka ameneŵa atigwera chifukwa cha yani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nkuti? Ndiwe mtundu wanji?”
9Iye adayankha kuti, “Ndine Muhebri, ndimapembedza Chauta, Mulungu wa Kumwamba, amene adalenga nyanjayi ndi mtundawu.”
10Pamenepo amalinyero aja adachita mantha kwambiri, namufunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” Kudziŵa adaadziŵa kuti Yona ankathaŵa Chauta, poti anali ataŵauza kale.
11Tsono adamufunsa kuti, “Kodi tikuchite chiyani kuti nyanjayi ikhale bata?” M'menemo nkuti namondwe uja akukulirakulira.
12Yonayo adaŵauza kuti, “Chabwino, ingondiponyani m'nyanjamu, mukatero nyanjayi ikhala bata. Ndikudziŵa kuti wolakwa ndine, nkuwona namondweyu akukuvutani chotere.”
13Amalinyero adayesetsa kupalasa kwambiri kuti abwerere ku mtunda, koma adalephera ndithu, poti mafunde ankakwererakwerera.
14Tsono adatama Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, takupembani musalole kuti ifeyo tife chifukwa cha moyo wa munthu uyu. Musatizenge mlandu chifukwa cha kupha munthu wosalakwa. Zonsezi zachitika chifukwa cha kufuna kwanu Inu Chauta.”
15Atatero adagwira Yona namponya m'nyanja. Pompo nyanjayo idakhala bata.
16Amalinyerowo adachita mantha aakulu ndi Chauta. Tsono adapereka nsembe, nalonjeza kuti adzatumikira Chauta.
17 Mt. 12.40 Chauta adatuma chinsomba chachikulu kuti chimeze Yona. Motero Yonayo adakhala m'mimba mwa chinsombacho masiku atatu, usana ndi usiku.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.