Aro. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Paulo, mtumiki wa Yesu Khristu. Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, nandipatula kuti ndikalalike Uthenga wake Wabwino.

2Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m'Malembo Oyera.

3Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide,

4koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu.

5Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumkhulupirira ndi kumumvera, kuti choncho dzina lake lilemekezedwe.

6Ena mwa anthuwo, ndinu amene Mulungu adakuitanani kuti mukhale ake a Yesu Khristu.

7Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma, amene Mulungu amakukondani, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Paulo alakalaka kukaona Akhristu a ku Roma

8Poyamba ndikuthokoza Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akusimba za chikhulupiriro chanu.

9Mulungu ndi mboni yanga. Ndimamtumikira ndi mtima wanga wonse, pakulalika Uthenga Wabwino wonena za Mwana wake. Akudziŵa kuti ndimakukumbukirani kosalekeza m'mapemphero anga onse.

10Ndimampempha Mulunguyo kuti ndipeze mpata tsopano woti ndibwere kwanuko.

11Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni.

12Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.

13 Ntc. 19.21 Abale, ndifuna kuti mudziŵe kuti kaŵirikaŵiri ndakhala ndikuganiza zobwera kwanuko, koma mpaka tsopano panali zina zondiletsa. Ndifuna kuti pakati panuponso ndidzagwire ntchito yoonetsa zipatso, monga zidachitikira pakati pa anthu enanso a mitundu ina.

14Ndili ndi udindo wolalikira anthu ovumbuluka ndi osavumbuluka, ndiwo anzeru ndi opulukira omwe.

15Chimenechi ndicho chikundikakamiza kukalalika Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.

Za mphamvu ya Uthenga Wabwino

16 Mk. 8.38 Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

17Hab. 2.4Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”

Anthu onse ndi ochimwa

18Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.

19Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi.

20Lun. 13.1-9; Mphu. 17.8Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.

21Aef. 4.17, 18Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.

22Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa.

23Deut. 4.16-18; Lun. 11.15; 12.24; 13.10-19Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

24Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao.

25Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen.

26Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo.

27Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.

28Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.

29Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,

30amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

31Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo.

32Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help