1 Ntc. 18.1 Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi mbale wathu Timoteo.
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, ndiponso anthu onse a Mulungu okhala m'dziko lonse la Akaiya.
2Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Paulo athokoza Mulungu3Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
4Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
5Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri.
6Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva.
7Chikhulupiriro chathu pa inu ncholimba. Tikudziŵa kuti monga mulikumva zoŵaŵa pamodzi nafe, momwemonso mudzapeza chokulimbitsani mtima pamodzi nafe.
8 1Ako. 15.32 Tsono abale, tifuna kuti mudziŵe, masautso amene tidakumana nawo ku dziko la Asiya, adatipsinja koopsa, kopitirira mphamvu zathu, kotero kuti sitinkayembekezanso kuti nkukhala ndi moyo.
9Ndithu m'mitima mwathu tinkangoganiza kuti basi talandira chilango chokaphedwa. Zimenezi zidachitika kuti tisamadzikhulupirire, koma kuti tizikhulupirira Mulungu amene amaukitsa akufa.
10Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
11Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake.
Paulo atchula zifukwa zosinthira ulendo wake12Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima.
13Timakulemberani zokhazokha zimene mungathe kuziŵerenga ndi kuzimvetsa bwino. Ndikhulupirira kuti,
14monga mwayamba kale kutidziŵa pang'ono, mudzatidziŵa kwenikweni, ndiye kuti pa tsiku la Ambuye Yesu mudzatha kutinyadira ife, monga momwe ifenso tidzakunyadirani inu.
15Popeza kuti pa zimenezi ndinali wotsimikiza ndithu, ndidaaganiza zoti ndiyambe ndafika kwanuko. Ndidaafuna kuti mulandire madalitso paŵiri:
16Ntc. 19.21ndidaakonza ulendo wanga kuti ndidzere kwanu popita ku Masedoniya, ndi kuti ndidzerenso kwanu pochokera ku Masedoniyako. Ndinkafuna kuti potero mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga wopita ku Yudeya.
17Kodi pamene ndidaaganiza kuchita zimenezi, inu mukuyesa kuti ndidaachita zinthu mwachibwana? Kaya zimene ndimaganiza kuzichita, kodi ndimangoziganiza mwaukapsala, kotero kuti ndingathe kunena kuti, “Inde, inde” ndiponso “Ai, ai” pa nthaŵi imodzi?
18Pali Mulungu woona, ndikulumbira kuti mau athu amene timakuuzani sali “Inde” ndiponso “Ai”.
19Ntc. 18.5Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene ine ndi Silivano ndi Timoteo tidakulalikirani, sanali “Inde” ndiponso “Ai” pa nthaŵi imodzi, koma nthaŵi zonse anali “Inde” wa Mulungu.
20Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
21Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza,
22natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
23Mulungu akhale mboni yanga, chifukwa chenicheni chimene sindidafikirenso ku Korinto chinali chakuti ndisakumvetseni chisoni.
24Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.