1Potsiriza tsono, abale, tifuna tikupempheni kanthu. Mudalandira kwa ife mau onena za m'mene muziyendera kuti mukondweretse Mulungu. Mukutsata mayendedwe otere kumene, koma tikukupemphani kolimba m'dzina la Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale.
2Pakuti mukudziŵa malangizo amene tidakupatsani ochokera kwa Ambuye Yesu.
3Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama.
4Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
5Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
6Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere.
7Paja Mulungu sadatiitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.
8Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera.
9Kunena za kukondana pakati pa akhristu, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani, popeza kuti ndi Mulungu mwini amene adakuphunzitsani za m'mene muyenera kukonderana.
10Ndipo mumakondana nawodi abale onse a m'dziko lonse la Masedoniya. Koma tikukupemphani abale, kuti muchite zimenezi koposa kale.
11Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,
12kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.
Za kubwera kwa Ambuye13Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo.
14Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
15 1Ako. 15.51, 52 Mphu. 48.11 Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai.
162Es. 6.23Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka.
17Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
18Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.