1Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati,
2“Ine ndine Chauta Mulungu wako, amene ndidakutulutsa mu ukapolo ku dziko la Ejipito.
3“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha.
4 Eks. 34.17; Lev. 19.4; 26.1; Deut. 4.15-18; 27.15 “Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko.
5Eks. 34.6, 7; Num. 14.18; Deut. 7.9, 10 Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
6Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.
7 Lev. 19.12 “Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.
8 Eks. 16.23-30; 31.12-14 “Uzikumbukira tsiku la Sabata, uzilisunga loyera.
9Eks. 23.12; 31.15; 34.21; 35.2; Lev. 23.3 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito zako zonse.
10Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.
11Gen. 2.1-3; Eks. 31.17 Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera.
12 Deut. 27.16; Mt. 15.4; 19.19; Mk. 7.10; 10.19; Lk. 18.20; Aef. 6.2; Aef. 6.3 “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
13 Gen. 9.6; Lev. 24.17; Mt. 5.21; 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9; Yak. 2.11 “Usaphe.”
14 Lev. 20.10; Mt. 5.27; 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9; Yak. 2.11 “Usachite chigololo.”
15 Lev. 19.11; Mt. 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20; Aro. 13.9 “Usabe.”
16 Eks. 23.1; Mt. 19.18; Mk. 10.19; Lk. 18.20 “Usachite umboni womnamizira mnzako.”
17 Aro. 7.7; 13.9 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”
Anthu achita mantha(Deut. 5.22-23)18 Ahe. 12.18, 19 Anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga, namaona mphezi ndi utsi paphiripo, ndipo ankaopa ndi kunjenjemera, ataima kutali.
19Adauza Mose kuti, “Muzilankhula ndi ife ndinu, ndipo tidzamva. Mulungu asalankhule nafe, kuti tingafe.”
20Apo Mose adaŵayankha kuti, “Musaope, Mulungu wafika kuti akuyeseni, kuti muzimuwopa m'mitima mwanu, ndiponso kuti musachimwe.”
21Koma anthu ankaima kutali, Mose yekha ndiye adayandikira mtambo wamdima m'mene munali Mulungu.
Malamulo onena za maguwa22Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba.
23Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.
24Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani.
25Deut. 27.5-7; Yos. 8.31 Mukadzandimangira guwa lamiyala, miyala yake musadzaseme, chifukwa mukadzaisema ndi chitsulo chosemera, mudzaipitsa guwalo.
26Popita ku guwa langa, musadzaponde pa makwerero, kuti maliseche anu angaonekere.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.