1Yotamu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa mwana wa Zadoki.
2Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, kutsata zonse zimene ankachita Uziya, bambo wake, kupatula kuti sadakaloŵe mwamphamvu ku Nyumba ya Chauta. Koma anthu ankachitabe zoipa.
3Iyeyo adamanga khomo lapamwamba la ku Nyumba ya Chauta, ndipo adagwira ntchito yaikulu yomanga linga la Ofele.
4Komanso adamanga mizinda ku dziko lonse lamapiri la Yuda. Adamanganso malinga ndi nsanja ku nkhalango zakumapiri.
5Adamenyana nkhondo ndi mfumu ya Aamoni, ndipo adaŵagonjetsa Aamoniwo. Nchifukwa chake, chaka choyamba Aamoni aja adapereka makilogramu 3,400 a siliva, matani 1,000 a tirigu, ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni ankalipira kwa Yotamuyo zinthu zonga zomwezo pa chaka chachiŵiri ndi chachitatu.
6Choncho Yotamu adasanduka wamphamvu chifukwa chakuti adasunga makhalidwe oongoka pamaso pa Chauta Mulungu wake.
7Tsono ntchito zonse za Yotamu, ndi nkhondo zake zonse ndiponso makhalidwe ake, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi mafumu a ku Yuda.
8Iyeyo anali wa zaka 25 pamene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu.
9Pambuyo pake Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.