1Davide adapempha nzeru kwa atsogoleri a anthu zikwi, kwa atsogoleri a anthu mazana, ndi kwa mtsogoleri wina aliyense.
2Pambuyo pake adauza msonkhano wonse wa Aisraele kuti, “Ngati zikukukomerani inu, ndipo ngati chimenecho ndiye chifuniro cha Chauta, Mulungu wathu, tiyeni titumize mau kwa abale athu onse amene akukhala m'dziko lonse la Israele ndiponso kwa ansembe ndi kwa Alevi okhala ku mizinda ndi ku miraga yake, kuti anthuwo adzasonkhane pamodzi kwa ife kuno.
3Tsono tibwere nalonso bokosi lachipangano la Chauta wathu. Paja pa nthaŵi ya Saulo sitidalisamale Bokosilo.”
4Msonkhano wonse udavomereza zimenezo, poti anthu onse adaaona kuti nzabwino.
5
12 2Am. 7.19 Davide adachita mantha ndi Mulungu tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndingathe bwanji kufika nalo kwathu Bokosi la Mulunguli?”
13Motero sadabwere nalo Bokosilo kwao ku mzinda wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.
141Mbi. 26.4, 5Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu kwa Obededomu, m'nyumba mwake. Ndipo Chauta adadalitsa banja la Obededomu pamodzi ndi zonse zimene adaali nazo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.