1Tsopano tiyeni titamande anthu otchuka
ndi kunyadira makolo athu potsata mibadwo yao.
2Mulungu adaonetsa mwa iwo kukula kwa ulemerero wake,
ndipo adasonyeza ukulu wake chiyambire.
3Ena adakhala mafumu m'maiko ao,
ndipo adatchuka chifukwa cha mphamvu zao.
Ena anali aphungu anzeru
ndipo ankalankhula zolosa.
4Ena ankatsogolera anthu ndi malangizo ao,
ankamvetsa bwino za m'mitima mwa anthu,
ndipo ankaphunzitsa anthu ao mwanzeru.
5Ena anali opeka nyimbo zokoma
ndipo ankalemba ndakatulo.
6Ena anali olemera ndi amphamvu,
ankakhala mwamtendere m'nyumba mwao.
7Anthu onseŵa adatchuka pakati pa anthu a mbadwo wao,
ndipo ankaŵanyadira pa moyo wao.
8Ena adasiya mbiri yabwino,
ndipo anthu akuŵakumbukirabe mpaka pano.
9Pali ena amene anthu saŵakumbukira,
amene adangoti zii, ngati sadakhalepo ndi moyo.
Iwo achita ngati sadabadwe konse,
chimodzimodzinso ana ao oŵatsatira.
10Koma nawu mndandanda wa anthu otchuka,
amene ntchito zao zabwino siziiŵalika.
11Chuma chao adzachilandira ndi ana ao,
ndipo choloŵa chao chidzakhala cha mibadwo yakutsogolo.
12Ana ao amasungabe chipangano,
zidzukulu zao zidzateronso chifukwa cha makolo ao.
13Zidzukulu zao zidzakhala mpaka muyaya,
ndipo ulemerero wao sudzazimirira.
14Mitembo yao adaiika mwamtendere,
koma mbiri yao idzakhala mpaka muyaya.
15Mitundu ya anthu idzalalika nzeru za anthu ameneŵa,
ndipo anthu a Mulungu adzaimba nyimbo zoŵatamanda.
Enoki16 Gen. 5.24; Ahe. 11.5; Yuda 1.14 Enoki adakondwetsa Ambuye, ndipo adatengedwa
kupita kumwamba.
Iye adapatsa mibadwo yonse chitsanzo cha
kutembenuka mtima.
Nowa17 Gen. 6.9—9.17 Nowa adapezeka kuti anali munthu wangwiro
ndi wolungama.
Pa nthaŵi ya chilango iye adakhala ngati chiphukira,
chifukwa cha iye pa nthaŵi ya chigumula
padatsalira anthu ena pansi pano.
18Ambuye adachita naye chipangano chamuyaya
chakuti zamoyo zonse sizidzaonongekanso ndi chigumula.
Abrahamu19 Gen. 15.1—17.27; 22.1-18 Abrahamu anali kholo lotchuka la mitundu
yambiri ya anthu.
Palibe amene adakhala womveka ngati iyeyo.
20Adatsata malamulo a Mulungu Wopambanazonse,
ndipo adachita naye chipangano.
Adakhazikitsa chipanganocho m'thupi mwake,
ndipo atamuyesa, adampeza kuti ali wokhulupirika.
21Nchifukwa chake Ambuye adamlonjeza molumbira
kuti adzadalitsa mitundu ya anthu mwa zidzukulu zake,
ndiponso kuti zidzukulu zakezo zidzachuluka
ngati fumbi la pa dziko lapansi,
zidzakwezedwa ngati nyenyezi.
Adalonjezanso kuti dziko laolo lidzakhala lalikuludi,
kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina,
ndiponso kuchokera ku mtsinje waukulu mpaka
ku malire a dziko lapansi.
Isaki ndi Yakobe22 Gen. 17.19; 26.3-5; 27.28; 28.14 Isakinso adamlonjeza zomwezo
chifukwa cha bambo wake Abrahamu.
23Madalitso oyenerera mtundu wonse wa anthu ndi chipangano,
adazigoneka pa Yakobe.
Adamlimbitsa m'madalitso amene adampatsawo
ndipo adampatsa dziko kuti likhale choloŵa chake.
Adaliduladula m'zigawo
naligaŵira mafuko khumi ndi aŵiri aja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.