1 Yer. 46.2-26; Ezek. 29.1—32.32 Nawu ulosi wonena za Ejipito.
Chauta wakwera pa mtambo wothamanga,
akupita ku Ejipito.
Mafano a ku Ejipito adzanjenjemera pamaso pake,
ndipo Aejipitowo mitima yao idzachokamo ndi mantha.
2Tsono Ine ndidzautsa Aejipito
kuti amenyane okhaokha.
Ndipo adzamenyana, mbale ndi mbale wake,
mnansi ndi mnansi wake,
mzinda ndi mzinda unzake,
ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
3Ndidzalepheretsa zolinga za Aejipito
mwakuti adzataya mtima.
Tsono adzapempha nzeru kwa mafano, amaula,
olankhula ndi mizimu, ndiponso anyanga.
4Ndidzapereka Aejipito kwa wolamulira wankhalwe.
Ndipo mfumu yoopsa ndiyo idzaŵalamulira,
akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
5Madzi a mtsinje wa Nailo adzaphwa,
ndipo mtsinjewo udzauma kuchita kuti gwaa.
6Ngalande zake zizidzanunkha,
ndipo mphanda za mtsinjewo ku Ejipito
zidzayamba kuchepa kenaka nkuuma.
Bango ndi mlulu zidzafota,
7ndipo zomera zonse za m'mphepete mwa Nailo
ndi ku mathiriro ake, zidzafa.
Zonse zobzalidwa m'mbali mwa Nailo zidzauma,
zidzauluzika, zosaonekanso.
8Asodzi adzadandaula ndi kulira.
Onse amene amaŵedza mu mtsinje wa
Nailo adzamva chisoni.
Onse amene amaponya khoka m'madzi adzalira.
9Anthu ogwira ntchito yopota thonje,
ndiponso anthu oomba nsalu zoyera,
adzataya mtima.
10Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,
ndipo anthu ogwira ntchito yolipidwa
adzangoti m'nkhongono zii.
11Akalonga a mu mzinda wa Zowani ndi zitsilu.
Aphungu anzeru a Farao amalangiza zopusa.
Kodi mungathe kumuuza bwanji Farao kunena kuti,
“Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,
wophunzira wa mafumu akale?”
12Iwe Farao, anzeru ako ali kuti?
Abwere kuno msanga kuti akudziŵitse
zimene Chauta Wamphamvuzonse
akunena zotsutsa Ejipito.
13Akalonga a mu mzinda wa Zowani
asanduka zitsilu,
ndipo akalonga a ku Memfisi anyengedwa.
Amene ali atsogoleri a Aejipito
alisokeza dziko lao.
14Chauta waŵasokoneza Aejipito.
Iwo akuchita dzandidzandi pa ntchito zao zonse,
ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake omwe.
15Ndipo palibe wina aliyense mu Ejipito
amene angachitepo kanthu,
wolemera kapena wosauka,
wotchuka kapena munthu wamba.
Ejipito adzapembedza Chauta16Tsiku limenelo Aejipito adzakhala ngati akazi, adzanjenjemera ndi kuchita mantha, akadzaona Chauta Wamphamvuzonse akusamula dzanja kufuna kuŵalanga.
17Dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Ejipito. Ndipo nthaŵi zonse Aejipito akadzamva za Yuda, adzaopsedwa chifukwa cha zimene Chauta Wamphamvuzonse afuna kuŵachita Aejipitowo kudzera mwa Yudayo.
18Tsiku limenelo ku dziko la Ejipito kudzakhala mizinda isanu yolankhula Chihebri, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti adzamtumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchulidwa “Mzinda wa Dzuŵa.”
19Tsiku limenelo m'kati mwa dziko la Ejipito mudzakhala guwa la Chauta, ndipo kufupi ndi malire adzaimikirako Chauta mwala wachikumbutso.
20Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Chauta Wamphamvuzonse alimo m'dziko la Ejipito. Aejipito akadzalira kwa Chauta pa zovuta zao, Iye adzatuma mpulumutsi kuti aŵateteze ndi kuŵapulumutsa.
21Tsono Chauta adzadziwulula kwa Aejipito, ndipo tsiku limenelo Aejipitowo adzadziŵa Chauta. Adzapembedza Chauta potsira nsembe ndi kupereka zopereka. Adzachita malonjezo aakulu kwa Chauta ndipo adzachitadi zimene adalonjezazo.
22Ngakhale Chauta adzaŵalange Aejipito dzolimba, adzaŵalanga inde, koma pambuyo pake adzaŵachiritsa. Iwo adzatembenukira kwa Chauta, ndipo Iye adzaŵamvera ndi kuŵachiritsa.
23Tsiku limenelo kudzakhala mseu waukulu wochoka ku Ejipito kupita ku Asiriya. Aasiriya adzayendera Aejipito, Aejipitonso adzayendera Aasiriya. Ndipo Aejipito ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi.
24Tsiku limenelo Israele adzakhala pamodzi ndi Ejipito ndi Asiriya, ndipo maiko atatuwo adzakhala dalitso pa dziko lonse lapansi.
25Chauta Wamphamvuzonse adzaŵadalitsa ndi mau aŵa akuti, “Adalitsidwe Aejipito, anthu anga; adalitsidwe Aasiriya, ntchito ya manja anga; adalitsidwe Aisraele, osankhidwa anga.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.