1 Am. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mfumu ya ku Ejipito idasonkhanitsa ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Idasonkhanitsanso zombo zambiri, nkuyesa kulanda dziko la Aleksandro mochenjera kuti aliphatikize ku dziko lake.

2Tsono adanyamuka kupita ku Siriya, akunena mau amtendere. Anthu am'mizinda adamtsekulira zipata za mizinda yao, nadzakumana naye, chifukwa mfumu Aleksandro anali atalamula kuti akakumane naye, popeza kuti anali mpongozi wake.

3Koma Ptolemeyo, poloŵa mu mzinda uliwonse, ankaikamo kaboma ka ankhondo ake.

4Atafika ku Azoto, anthu akumeneko adamuwonetsa nyumba ya Dagoni imene inali itapsa, ndiponso mzinda wa Azoto ndi mizinda yozungulira imene inali itaonongedwa. Adamuwonetsanso mitembo ya anthu amene anali atatenthedwa pa nkhondo, chifukwa adaaiwunjika pa njira imene ankayenera kudzera.

5Kenaka adafotokozera mfumu zimene Yonatani adaaŵachita, kuti amuimbe mlandu, koma mfumu sidanene kanthu.

6Yonatani adabwera ku Yopa kudzachingamira mfumu ndi ulemu waukulu. Atalonjerana, adagona komweko.

7Yonatani adaperekeza mfumu mpaka ku mtsinje wa Eleutere, nabwerera ku Yerusalemu.

8Tsono mfumu Ptolemeyo adalanda mizinda ya m'mbali mwa nyanja mpaka ku Seleukiya, ndipo monsemo ankalingalira za kuchita nkhondo ndi Aleksandro.

9Adatuma amithenga kwa mfumu Demetriyo kukamuuza kuti, “Ubwere, tidzapalane chibwenzi, ndidzakupatsa mwana wanga wamkazi yemwe ali ndi Aleksandro, ndipo udzakhala wolamulira mu ufumu wa bambo wako.

10Ndikumva chisoni kuti mwana wanga wamkazi ndidampereka kwa munthu amene adaafuna kundipha.”

11Ankaika mlandu pa Aleksandro, chifukwa ankasirira ufumu wake.

12Motero adalandadi mwana wake wamkazi nampereka kwa Demetriyo. Chibwenzi chake ndi Aleksandro chidathera pomwepo, ndipo chidani chaocho chidadziŵika kwa onse.

13Pambuyo pake Ptolemeyo adaloŵanso mu Antiokeya, nalanda chisoti chaufumu cha ku Asiya, kotero kuti ankavala zisoti ziŵiri zaufumu, china cha ku Ejipito, china cha ku Asiya.

14Nthaŵiyo Aleksandro anali ku Silisiya, chifukwa anthu akumeneko adaamugalukira.

15Atamva zonsezo, Aleksandro adabwera kudzamenya nkhondo ndi mpongozi wake. Mfumu Ptolemeyo adatuluka, adadzakumana naye ndi gulu lalikulu lankhondo, namthaŵitsa.

16Aleksandro adathaŵira ku Arabiya kuti akapezeko chitetezo. Motero mfumu Ptolemeyo adasanduka wamkulu kopambana.

17Zabidiele, Mluya, adadula mutu wa Aleksandro nautumiza kwa Ptolemeyo.

18Koma pakutha masiku aŵiri Ptolemeyo nayenso adafa, ndipo ankhondo ake okhala m'timaboma tankhondo, anthu akomweko adaŵapha.

19Choncho Demetriyo adaloŵa ufumu wake chaka cha 167.

Demetriyo ayanjana ndi Ayuda

20Masiku amenewo Yonatani adasonkhanitsa anthu a ku Yudeya kuti akalande boma lankhondo la ku Yerusalemu. Adakonza makina ambiri ankhondo odzathyolera bomalo.

21Koma anthu ena okana chipembedzo chao ndi odana ndi mtundu wao, adanka kwa mfumu Demetriyo ndi kukamdziŵitsa kuti Yonatani wazinga boma lija.

22Mfumu itamva, idapsa mtima. Idapita mofulumira ku Ptolemaisi, nkumulembera Yonatani kalata yomuuza kuti aleke kuzinga boma lija. Idamuuzanso kuti abwere ku Ptolemaisi msanga kudzakambirana naye.

23Yonatani atalandira kalatayo, adalamula anthu ake kuti abazingabe boma lija. Adasankhula akuluakulu ena a Aisraele ndi ansembe, napita nawo ngakhale kunali koopsa kutero.

24Adatenga golide, siliva, zovala ndi mphatso zina zambiri, napita kukaonana ndi mfumu ku Ptolemaisi. Adapeza kuyanja pamaso pa mfumuyo.

25Anthu ena odana ndi chipembedzo chao adayesanso kumnenera zoipa.

26Koma mfumu Demetriyo adamchitira zomwe mafumu akale adaamuchitira. Adamlemekeza pakhamu pa abwenzi ake onse.

27Adavomereza ukulu wake wa unsembe ndi ulemu umene anali nawo kale, nafuna kuti akhale mmodzi mwa abwenzi ake apamtima.

28Yonatani adapempha mfumu kuti ileke kuŵakhometsa msonkho anthu a ku Yudeya ndi a ku madera atatu a ku Samariya aja, ndipo adalonjeza kuti adzapereka kwa mfumu makilogramu 10,000 a siliva.

29Mfumu idavomera, nilembera Yonatani kalata yolongosola zonsezo ndi mau akuti,

30“Ndine mfumu Demetriyo, ndikulonjera Yonatani mbale wake, pamodzi ndi Ayuda onse.

31Naŵa mau a m'kalata imene tidalembera mbale wathu Lasitene yonena za inu:

32Ndine mfumu Demetriyo, ndikupereka moni kwa bambo wanga Lasitene.

33Tikufuna kuŵachitira zabwino Ayuda amene ali abwenzi athu okhulupirika, chifukwa cha chifundo chimene adaonetsa.

341Am. 10.30Taŵatsimikizira kuti dziko la Yudeya ndi lao pamodzi ndi madera atatu aŵa a Samariya: Aferema, Lida ndi Ramataimu, pamodzi ndi midzi yake. Madera ameneŵa tikuŵachotsa ku Samariya kuti akhale a ku Yudeya. Zimenezi zidzakhala zaphindu kwa anthu onse opita ku Yerusalemu kukapembedza. Zidzaloŵa m'malo mwa msonkho umene mfumu inkalandira kale chaka chilichonse pa dzinthu dzam'munda ndi pa zipatso zam'mitengo.

35Ndiponso zina zonse zimene ankayenera kupereka kwa ine mpaka tsopano, monga chachikhumi ndi msonkho weniweni, kapenanso msonkho wa mchere ndi misonkho ina yapadera, tikufuna kuŵachotsera zonsezi.

36Zaufulu zonsezi zisadzafafanizike konse m'tsogolo muno.

37Ndiye inu musalephere kulemba kalata yonga yomwe ino ndi kuipereka kwa Yonatani. Mumuuze kuti akaipachike ku phiri loyera, pa malo abwino pamene izikaonekera bwino lomwe.”

Yonatani athandiza Demetriyo

38Mfumu Demetriyo poona kuti dziko lili pa mtendere, popanda zomuvuta, adachotsa ankhondo ake onse kuti aliyense apite kunyumba kwake. Adangosunga magulu a asilikali achilendo amene adaaŵalemba ku zisumbu za mitundu ina ya anthu. Choncho ankhondo amene ankatumikira makolo ake adayamba kudana naye.

39Trifo, amene kale anali mmodzi mwa abwenzi a Aleksandro, ataona kuti ankhondo aja akumuŵiringulira Demetriyo, adapita kwa Yamuleku Mluya, amene ankalera Antioko mwana wamng'ono wa Aleksandro.

40Adamuumiriza kuti ampatse mwanayo kuti amlonge ufumu m'malo mwa atate ake. Adamsimbira zimene Demetriyo adaachita, nanena kuti ankhondo ake akudana naye. Adakhala kumeneko masiku ambiri.

41Nthaŵi yomweyo Yonatani adatuma anthu kukapempha Demetriyo kuti achotse ankhondo ake okhala m'boma lankhondo la ku Yerusalemu ndi m'malinga ena a ku Yudeya, chifukwa ankalimbana ndi Aisraele.

42Demetriyo adatuma anthu kukauza Yonatani mau aŵa akuti, “Sindidzangokuchitira iwe ndi a mtundu wako zimenezo, koma ndikufuna kuti ndikapeza mpata ndipereke ulemu woŵirikiza kwa iwe ndi mtundu wako nthaŵi zonse.

43Tsopano ndi bwino kuti utume anthu adzandithandize, chifukwa ankhondo anga onse adandisiya.”

44Yonatani adatumiza ku Antiokeya ankhondo 3,000 amphamvu ndi olimba mtima. Atafika kwa mfumu, iyo idakondwera nako kufika kwao.

45Pamenepo anthu amumzindamo okwanira 120,000, adasonkhana pakati pa mzinda, kuti aphe mfumu.

46Koma mfumuyo idathaŵira m'nyumba yake yaufumu. Apo anthu amumzindamo adalanda miseu yaikulu, nayamba zachipolowe.

47Tsono mfumu idaitana Ayuda aja kuti adzamthandize. Onsewo adasonkhana pafupi naye, kenaka nkubalalikira mu mzinda. Pa tsiku limenelo Ayudawo adapha anthu ngati 100,000.

48Adatentha mzindawo, adafunkha chuma chake chochuluka, napulumutsa mfumu.

49Anthu aja ataona kuti Ayuda alanda mzindawo, adataya mtima nayamba kulira kwa mfumu ndi mau aŵa opemba akuti,

50“Pepani ndithu, tikupempha mtendere, tikupemphanso kuti Ayudaŵa aleke kuchita nkhondo ndi ife ndi mzinda wathu.”

51Atatero adaponya pansi zida zao, napangana za mtendere. Ayuda adakhala ndi ulemu waukulu pamaso pa mfumu ndi pa anthu ena a m'dziko lake. Ndipo adabwerera ku Yerusalemu, ali ndi chuma chofunkha chambiri.

52Tsono mfumu Demetriyo adakhazikika bwino mu ufumu wake, ndipo dziko lake lidakhala pa mtendere.

53Koma sadachite zonse zimene adaalonjeza, ndipo adaleka kuyanjana ndi Yonatani. M'malo momubwezera zabwino zimene adaamchitira, ankamuvuta kwambiri.

Yonatani amenyana nkhondo ndi Demetriyo

54Patapita nthaŵi, Trifo adabwerera pamodzi ndi mnyamata uja Antioko, namlonga ufumu, ndi kumuveka chisoti chaufumu.

55Ankhondo aja, amene Demetriyo adaaŵachotsa, adasonkhana nakaphatikana ndi Antioko. Onsewo adayamba nkhondo ndi mfumu, iyoyo nkuthaŵa, ataigonjetsa.

56Trifo adalanda njovu zake, nalandanso mzinda wa Antiokeya.

57Tsono Antioko adalemba kalata kwa Yonatani yonena kuti, “Ndikutsimikiza kuti ukhalebe mkulu wa ansembe, ukhalenso wolamulira madera anai aja ndiponso ukhale mmodzi mwa abwenzi a mfumu.”

58Adamtumizira ziŵiya zagolide ndi mbale zodyera, namlola kumamwera m'zikho zagolide, ndi kuvala nsalu zofiirira ndi bakolo lomangira lagolide.

59Kenaka adasankhula Simoni, mbale wa Yonatani, kuti akhale bwanamkubwa wolamulira, kuyambira ku malire a Tiro mpaka ku malire a Ejipito.

60Tsono Yonatani adanyamuka, nayendera dziko la kutsidya kwa mtsinje ndi mizinda yake. Magulu onse ankhondo a ku Siriya adadzaphatikana naye, kuti amthandize kumenya nkhondo. Atafika ku Askaloni, anthu akumeneko adamlandira ndi ulemu.

61Pochoka kumeneko adakafika ku Gaza. Koma anthu amumzindamo adamtsekera zipata zao. Apo Yonatani adazinga mzindawo, nautentha pamodzi ndi midzi yake, nkufunkha chuma chao.

62Tsono anthu a ku Gaza adapepesa Yonatani, ndipo iye adapangana nawo za mtendere. Koma adatenga ana a atsogoleri ao ngati chigwiriro, naŵatumiza ku Yerusalemu. Kenaka adayendera dziko lonse mpaka ku Damasiko.

63Tsiku lina Yonatani adamva kuti atsogoleri ankhondo a Demetriyo ali ku Kadesi ku Galileya ndi gulu lalikulu lankhondo, akufuna kuchotsa pa mpando wake.

64Adapita kukakumana nawo, nasiya mbale wake Simoni m'dzikomo.

65Simoni adapita kukamanga zithando zake pafupi ndi Betizure. Adamenya nawo nkhondo masiku ambiri, naŵatsekera adaniwo m'kati mwa mzindawo.

66Ankhondo amumzindamo adampempha kuti pakhale mtendere, iyeyo nkuvomera. Adaŵatulutsa mumzindamo, naulanda, kenaka nkuikamo kaboma ka asilikali ake.

67Yonatani ndi gulu lake adaamanga zithando zao pafupi ndi nyanja ya Genezarete, ndipo m'mamaŵa adaloŵa m'chigwa cha Azore.

68Gulu lankhondo la anthu achilendo lija lidadzakumana naye ku chigwa. Adaamuikira obisalira m'mapiri, pamene iwowo ankadzakumana naye maso ndi maso.

69Tsono anthu obisalira aja adatuluka mobisala muja nkudzailoŵa nkhondo ija.

70Anthu a Yonatani adathaŵa onse. Panalibe otsala kupatula Matatiasi mwana wa Abisalomu, ndi Yudasi mwana wa Khalifi, atsogoleri a ankhondo.

71Tsono Yonatani adang'amba zovala zake, nadzithira fumbi kumutu, nkuyamba kupemphera.

72Pambuyo pake adabwerera kunkhondo kuja. Adaŵagonjetsa adaniwo, iwowo nkuthaŵa.

73Poona zimenezo anthu a Yonatani amene adaathaŵa aja adabwerera nadzaphatikana naye. Onse pamodzi adalondola adani ao mpaka ku Kadesi kumene anali atamanga zithando zao. Iwo omwe adamanga mahema ao komweko.

74Pa tsikulo ankhondo achilendo adaphedwa ngati 3,000. Tsono Yonatani adabwerera ku Yerusalemu.

Yonatani atuma amithenga ku Roma ndi ku Sparta
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help