Mas. 91 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu mtetezi wathu.

1Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse,

iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,

2adzanena kwa Chauta kuti,

“Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa,

ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

3Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka,

ndiponso ku mliri woopsa.

4Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake,

udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo.

Kukhulupirika kwake kumateteza

monga chishango ndi lihawo.

5Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku,

kapena nkhondo nthaŵi yamasana.

6Sudzaopanso mliri wogwa usiku,

kapena zoononga moyo masana.

7Anzako chikwi chimodzi angathe kuphedwa pambali pakopa,

kapena zikwi khumi ku dzanja lako lamanja,

koma iwe zoopsazo sizidzakukhudza.

8Uzingopenya ndi maso ako,

ndipo udzaona m'mene amalangidwira anthu ochita zoipa.

9Chifukwa chakuti wavomera Chauta

kuti akhale malo ako othaŵirako,

wavomera Wopambanazonse

kuti akhale malo ako okhalamo,

10zoipa sizidzakugwera,

zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.

11 Mt. 4.6; Lk. 4.10 Chauta adzapatsa angelo ake

ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.

12 Mt. 4.6; Lk. 4.11 Adzakunyamula m'manja mwao,

kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.

13 Lk. 10.19 Udzatha kuponda mkango ndi njoka,

zoonadi udzaponda ndi phazi lako

msona wa mkango ndiponso chinjoka.

14Pakuti amene amandikangamira

Ine Mulungu mwachikondi,

ndidzampulumutsa.

Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.

15Akadzandiitana, ndidzamuyankha,

ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto.

Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

16Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help