1 Yes. 47.1-15; Yer. 50.1—51.64 Nawu uthenga wonena za Babiloni umene Yesaya, mwana wa Amozi, adalandira kwa Mulungu.
2Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see.
Muŵafuulire ankhondo ndi kuŵakodola
kuti adzaloŵe pa zipata za mzinda.
3Ine Mulungu mwini wake ndapereka
malamulo kwa anthu anga opatulika.
Ndasonkhanitsa ankhondo amphamvu,
amene amakondwerera kupambana kwanga,
kuti akhale zida zanga zolangira
amene ndimaŵakwiyira.
4Tamvani phokoso kumapiriku!
Likumveka ngati phokoso la chinamtindi cha anthu.
Imvani chiwawa m'maufumu!
Ndiye ngati mitundu ya anthu
ikusonkhana pamodzi.
Chauta Wamphamvuzonse akukhazika
ankhondo ake mokonzekera kumenya nkhondo.
5Iwowo akuchokera ku maiko akutali,
ku malekezero a dziko.
Ndiye kuti Chauta wanyamula zida
zake zija mokwiya,
akubwera kuti adzaononge dziko lonse lapansi.
6 Yow. 1.15 Lirani kwamphamvu pakuti tsiku
la Chauta layandikira.
Likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.
7Tsono manja onse adzafooka,
ndipo mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8Onse adzada nkhaŵa, adzavutika
ndi kumva zoŵaŵa,
zoŵaŵa zake zonga zimene amazimva mkazi pochira.
Azidzayang'anana mwamantha,
nkhope zao zidzagwa ndi manyazi.
9Zoonadi, tsiku la Chauta likudza,
tsiku lopanda chisoni,
laukali ndi lamkwiyo.
Chauta akubwera kuti asandutse dziko
lapansi chipululu ndi kuwononga
anthu ochimwa am'menemo.
10 Ezek. 32.7; Mt. 24.29; Mk. 13.24, 25; Lk. 21.25; Chiv. 6.12, 13; 8.12 Nyenyezi zonse zakumwamba
sizidzaonetsanso kuŵala.
Dzuŵa lidzada potuluka,
ndipo mwezi sudzaŵala konse.
11Chauta akuti,
“Ndidzalanga anthu a dziko lapansi
chifukwa cha kuipa kwao,
ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao.
Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza
ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa
anthu ankhanza.
12Anthu ndidzaŵasandutsa
osapezekapezeka kuposanso m'mene
aliri golide wangwiro,
mtundu wa anthu udzakhala wosoŵa ngati
golide wa ku Ofiri.
13Tsono ndidzagwedeza mlengalenga,
ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.
Zonsezi zidzachitika chifukwa cha ukali
wa Ine Chauta Wamphamvuzonse pa tsiku
la mkwiyo wanga woopsa.
14Choncho munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwao,
aliyense adzathaŵira ku dziko lake,
ngati mbaŵala zothaŵa anthu auzimba
kapenanso ngati nkhosa zopanda wozikusa.
15Aliyense amene adzapezeke adzabayidwa chipyoza.
Aliyense amene adzagwidwe adzaphedwa ndi lupanga.
16Ana ao akhanda adzatswanyidwa iwo akuwona.
M'nyumba mwao mudzafunkhidwa,
ndipo akazi ao adzaŵachimwitsa mwakhakhamizo.
17“Ine Chauta ndidzadzutsa Amedi kuti
amenyane ndi Ababiloni.
Iwo safuna siliva
ndipo sakondwa ndi golide.
18Adzapha anyamata ndi mauta ao.
Sadzachitira chifundo ana.
Mitima yao siidzamva chisoni ndi ana akhanda omwe.
19 Gen. 19.24 Babiloni ufumu wake ndi waulemerero
kuposa maufumu ena onse,
ndipo anthu ake amaunyadira.
Koma Ine Chauta ndidzaononga
mzinda wa Babiloniwo
monga ndidaonongera Sodomu ndi Gomora
pa nthaŵi imene ndidagonjetsa mizindayo.
20Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo
pa mibadwo yonse.
Mluya aliyense woyendayenda sadzamangako hema kumeneko,
abusa sadzaŵetako ziŵeto zao kumeneko.
21 Yes. 34.14; Zef. 2.14; Chiv. 18.2 Koma nyama zakuthengo ndizo zimene
zidzakhale kumeneko,
nyumba zake zidzadzaza ndi akadzidzi.
Kuzidzayendayenda nthiŵatiŵa,
ndipo atonde akuthengo azidzavinavinako.
22M'nsanja zake muzidzalira afisi,
m'nyumba zake zaufumu zokongola muzidzalira nkhandwe.
Nthaŵi yake yayandikira,
ndithu masiku ake ali pafupi kutha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.