1Naŵa mau a Aguri, mwana wa Yake, wa ku Masa:
Inu Mulungu, ine ndatopa.
Inu Mulungu, ine ndatopa, ndalefukiratu.
2Ndithudi, ine ndine wopusa koposa anthu onse.
Ndilibe nzeru zonga za munthu.
3Sindidaphunzire nzeru,
ndipo Woyera uja sindimdziŵa.
4Kodi ndani adaakwera kumwamba natsikako?
Ndani adafumbatapo mphepo m'manja?
Ndani adafukusapo madzi m'chovala?
Ndani adakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi?
Dzina lake ndani, ndipo mwana wake dzina lake ndani?
Tanenatu ngati ukudziŵa!
5Mau aliwonse a Mulungu ndi oona.
Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
6Pa mau ake usamaonjezeko kanthu,
kuwopa kuti angakudzudzule,
ndipo ungapezeke kuti ndiwe wabodza.
7Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri,
musandimane zimenezo ndisanafe:
8Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama.
Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha.
Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,
9kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri,
ndingayambe kukukanani nkumanena kuti,
“Chauta ndiye yaninso?”
Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba,
potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
10Wantchito usamsinjirire kwa mbuyake,
kuti angakutemberere,
ndipo iweyo ungapezeke kuti ndiwe wolakwa.
11Pali ena amene amatemberera atate ao,
ndipo sadalitsa amai ao.
12Pali ena amene amadziyesa oyera mtima,
koma sadachotse zoipa zao.
13Pali ena amene amadzitukumula kwambiri,
amadziyesa abwino kwabasi.
14Pali ena amene amasongola mano ao ngati malupanga,
amaŵanola ngati mipeni,
kuti adye amphaŵi ndi kuŵachotsa pa dziko lapansi,
kutinso achotse anthu osauka pakati pa anzao.
15Mtsundu uli ndi ana aakazi aŵiri.
Anawo amangokhalira kulira kuti,
“Tipatseni chakuti, tipatseni chakuti.”
Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta.
Pali zinthu zinai zimene siziti, “Takwana.”
16Manda, mkazi wosabala, nthaka yachiwumire
ndiponso moto womangoyakirayakira.
17Aliyense amene amaseka bambo
ndi kumanyozera kumvera mai,
makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso,
ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa kwambiri.
Pali zinthu zinai zimene sindizimvetsa konse,
zinthuzo ndi izi:
19 Lun. 5.10-12 M'mene umaulukira mphamba mu mlengalenga,
m'mene imayendera njoka pa thanthwe,
m'mene chimayendera chombo pa nyanja yakuya,
ndiponso m'mene mwamuna amachitira akakhala ndi namwali.
20M'mene amachitira mkazi akachita chigololo amatere:
amati akadya nkupukuta pakamwa,
namanena kuti, “Palibe chimene ndalakwa.”
21Pali zinthu zitatu zimene dziko lapansi
limanjenjemera nazo.
Pali zinthu zinai zimene dziko lapansi
silingathe kuzipirira:
22kapolo akasanduka mfumu,
chitsiru chikakhuta,
23mkazi wonyozeka akakwatiwa,
ndiponso mdzakazi akalanda malo a mbuyake.
24Pali zinthu zinai zing'onozing'ono pa dziko lapansi,
koma ndi zochenjera kwambiri:
25Nyerere zili ngati anthu opanda nyonga,
komabe zimakonzeratu chakudya chake m'chilimwe.
26Mbira zili ngati anthu opanda nyonga,
komabe zimakonza pokhala pake m'matanthwe.
27Dzombe lilibe mfumu,
komabe lonse limakhala m'magulumagulu poyenda.
28Buluzi ungathe kumugwira ndi manja,
komabe amakhala m'nyumba za mafumu.
29Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya.
Pali zinthu zinai zimene zimayenda monyadira:
30Mkango umene uli ndi mphamvu kupambana nyama zonse,
ndipo suthaŵa kanthu kalikonse.
31Tambala woyenda chinyachinya, ndi tonde,
ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza,
kapena wakhala ukukonzekera kuchita zoipa,
yamba wati chete, uziganize bwino.
33Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika.
Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka,
ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.