Yob. 34 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Elihu popitiriza kulankhula adati,

2“Imvani mau anga, inu anthu anzeru,

mutchere khutu, inu odziŵa zinthunu.

3Pakuti khutu limamvetsa mau

monga momwe m'kamwa mulaŵira chakudya.

4Tiyeni tisankhe zolungama,

titsimikize tokha zimene zili zabwino.

5Pakuti aYobe anena kuti,

‘Ndine wosalakwa,

koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.

6Ngakhale ndine wolungama, akundiyesa wabodza.

Mavuto anga ndi osatha, ngakhale ndine wosachimwa.’

7Kodi pali munthu amene angafanefane ndi aYobe?

Iwoŵa apambana kunyoza Mulungu.

8Amayenda ndi anthu ochita zoipa,

amayanjana ndi anthu a mtima woipa.

9Paja ankanena kuti, ‘Palibe phindu

kuti munthu azikondwerera Mulungu.’

10“Tsono mumve, inu anthu anzerunu,

Mulungu sangathe kuchita choipa,

Mphambe sangathe kulakwa mpang'ono pomwe.

11 Mas. 62.12 Amambwezera munthu potsata ntchito zake,

munthuyo zinthu zimamgwera

malinga ndi mayendedwe ake.

12Ndithudi, Mulungu sangachite choipa,

Mphambe sangaweruze mosalungama.

13Kodi ndani adampatsa Mulungu

udindo wolamulira dziko lapansi?

Ndani adaika dziko lapansi m'manja mwake?

14Iye akadalanda moyo wake,

akadamulamula kuti mpweya wake

ubwerere kwa Iye mwini,

15bwenzi zamoyo zonse zitaonongeka,

bwenzi anthu onse atabwerera ku fumbi.

16“Ngati ndinu omvetsa, mumve zimenezi,

mumvetsere bwino zimene ndikunenazi.

17Kodi munthu wodana ndi

chilungamo angathe kukhala wolamulira?

Kodi mungathe kumuweruza Mulungu

Wolungama ndi Wamphamvu uja kuti ndi wolakwa?

18Mulungu amadzudzula mafumu

kuti, ‘Ndinu opanda pake,’

amauza akalonga kuti, ‘Ndinu oipa.’

19Iye sachita zokondera kwa akuluakulu,

kapena kulemekeza olemera kupambana osauka,

pakuti onsewo Mulungu adaŵalenga ndi manja ake.

20Iwowo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku

Mulungu amakantha anthu, iwowo nkufa,

anthu amphamvu amaŵalanda moyo mosavuta.

21“Mulungu amapenya njira zonse za anthu,

amaona mayendedwe ao onse.

22Palibe usiku kapena mdima wandiweyani

kumene anthu ochita zoipa angathe kubisalira Mulungu.

23Mulungu sasoŵa kuchita

kumuikira munthu wina aliyense

nthaŵi yoti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.

24Iye amatsitsa atsogoleri,

mlandu wao osaufufuza nkomwe,

ndipo m'malo mwao amaikamo ena.

25Iyeyo amadziŵa bwino ntchito zao,

amaŵagubudula usiku, iwowo nkutswanyika.

26Amaŵakantha chifukwa cha kuipa kwao,

anthu ena onse akupenya,

27chifukwa adapatuka osamtsata,

ndipo sankasamala malamulo ake.

28Adaliritsa amphaŵi kuti afuule kwa Mulungu,

ndipo Iyeyo adamva kufuula kwa ovutikawo.

29Kodi Mulungu akangoti duu,

ndani anganene kuti walakwa?

Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumpenyabe.

Komabe ndiye amene amasamalira

munthu kapena mtundu wa anthu,

30kuti asalamulidwe ndi anthu osadziŵa Mulungu,

ndipo asakodwe m'misampha yao.

31“Kodi alipo amene adauza Mulungu kuti,

‘Ndalangika, sindidzachimwanso,

32mundiphunzitse zimene sindikuziwona:

ngati ndidachita choipa, sindidzachitanso’?

33Kodi Mulungu akuweruzeni

potsata m'mene inuyo mukuganizira,

pamene inu mukukana kulapa?

Inu ndinu amene muyenera kusankha osati ine.

Nchifukwa chake munene zimene mukudziŵa.

34Anthu omvetsa zinthu adzandikambira,

anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,

35‘Yobe akulankhula mosadziŵa,

mau ake ndi opanda nzeru.’

36Kunali bwino aYobe akadayesedwa mpaka ku mapeto,

chifukwa choti amayankha

monga m'mene amayankhira anthu oipa.

37Pa tchimo lao aonjezerapo upandu,

akunyadira zochita zao,

ndipo akuchulukitsa mau onyoza Mulungu ife tilikumva.”

Mulungu amasamalira zochitika pa dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help