1Tsono Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasuri, Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malakiya, adamva zimene Yeremiya ankauza anthu zoti
2Chauta akunena kuti, “Aliyense amene atsalire mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene atuluke kukadzipereka kwa Ababiloni adzakhala moyo, adzapulumutsa moyo wake.
3Mzinda uno udzaperekedwadi kwa ankhondo a mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.”
4Tsono akuluakulu adauza mfumu kuti, “Munthuyu ayenera kuphedwa. Akutayitsa mtima ankhondo ndi anthu onse otsalira mu mzinda, chifukwa cha zolankhula zakezi. Munthu ameneyu sakuŵafunira zabwino anthu, angofuna kuti aonongedwe basi.”
5Mfumu Zedekiya adati, “Suyu, ali m'manja mwanu. Ine mfumu sindingakuletseni ai.”
6Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m'chitsime chimene adaakumba Malakiya mwana wa mfumu, m'bwalo la alonda a mfumu. Adamtsitsira m'menemo ndi chingwe. M'chitsimemo munalibe madzi, munali matope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m'matopemo.
7Tsono Ebedemeleki, Mkusi wina wofulidwa wogwira ntchito ku nyumba ya mfumu, adamva kuti Yeremiya amponya m'chitsime. Nthaŵi imeneyo nkuti mfumu ili ku Chipata cha Benjamini.
8Ebedemeleki adatuluka ku nyumba ya mfumu kukaiwuza kuti,
9“Mfumu mbuyanga, anthu aŵa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m'chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mzinda, adzafa ndi njala m'menemo.”
10Tsono mfumu idalamula Mkusi Ebedemeleki kuti, “Tenga anthu atatu, mukamtulutse mneneri Yeremiya asanafe.”
11Apo Ebedemeleki adapita ku nyumba ya mfumu ndi anthuwo, nakatenga nsanza m'chipinda cha zovala. Nsanzazo adazitsitsa ndi zingwe m'chitsime m'mene munali Yeremiya.
12Ebedemeleki Mkusi uja adauza Yeremiya kuti, “Ikani nsanzazi m'kwapa mwanu kuti zingwe zingakupwetekeni.” Yeremiya adachitadi zimenezo.
13Tsono adamtulutsira kunja ndi zingwe, ndipo Yeremiya adakakhalanso konkuja ku bwalo la alonda.
Zedekiya apempha nzeru kwa Yeremiya14Tsiku lina mfumu Zedekiya adaitana mneneri Yeremiya namlandira pa chipata chachitatu cha ku Nyumba ya Chauta. Adamuuza kuti, “Ndifuna kukufunsa kanthu, usati undibisire ai.”
15Yeremiya adayankha kuti, “Ndikakuuzani, mosapeneka konse mundipha. Ndikakulangizani simumvera.”
16Apo mwachinsinsi mfumu Zedekiya adalumbira pamaso pa Yeremiya kuti, “Pali Chauta wamoyo amene adatipatsa moyo, ine sindikupha. Ndipo sindikupereka kwa anthu amene afuna kukuphaŵa.”
17Yeremiya adauza Zedekiya kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzinda uno sadzautentha. Inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhala moyo.
18Koma mukangopanda kudzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'manja mwa Ababiloni, ndipo adzautentha, tsono inu simudzapulumuka m'manja mwao.’ ”
19Mfumu Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Ndikuwopa Ayuda amene adathaŵira kale kwa Ababiloni. Ndikuwopa kuti Ababiloni adzandipereka kwa Ayudawo, ndipo iwowo adzandichita zoipa.”
20Yeremiya adayankha kuti, “Iyai, sadzakuperekani. Ngati mumvera Chauta pa zonse, ndikukuuzani kuti zinthu zonse zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala ndi moyo.
21Koma mukakana kutuluka kuti mukadzipereke, Chauta wandiwululira kuti
22akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda, adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni. Popita ku Babiloniko, akazi amenewo azidzaimba kuti,
“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja adakunyenga,
ndipo adakugonjetsa.
Tsopano poti miyendo yako yazama m'matope,
abwenzi akowo akusiya.’
23Akazi anu onse pamodzi ndi ana adzaŵapereka m'manja mwa Ababiloni. Ndipo inuinuyo simudzalephera kugwa m'manja mwao. Mudzagwidwa ndi mfumu ya ku Babiloni, kenaka mzinda uno adzautentha.”
24Pamenepo Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Usauze munthu wina aliyensetu zimenezi, kuti ungaphedwe.
25Akuluakulu akamva kuti ndakhala ndikulankhula nawe, makamaka abwera kwa iwe kudzanena kuti, ‘Utiwuze zimene wauza amfumu, ndi zimene iwowo akuuza, usatibisire, ndipo sitidzakupha.’
26Tsono udzaŵayankhe kuti, ‘Ndinalikupempha kwa amfumu kuti asandibwezenso ku nyumba ya Yonatani, kuti ndikafe kumeneko.’ ”
27Akuluakulu onse adabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye adaŵayankha monga momwe mfumu idamuuzira. Motero nkhani zao zidathera pomwepo, chifukwa mau aja anali asanamveke kwa munthu wina aliyense.
28Ezek. 33.21Tsono Yeremiya adakhalabe m'bwalo la alonda, mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu udagonjetsedwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.