Yud. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chaka cha 18 cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya Aasiriya, tsiku la 22 la mwezi woyamba, a m'nyumba ya mfumu adamvana zoti athire msimsi pa dera lonselo, monga adaalumbirira muja.

2Mwiniwakeyo adasonkhanitsa akulu onse ndi nduna zonse za ankhondo ake, nachita nawo upo wachinsinsi. Adaŵauza cholinga chake chofuna kugonjetseratu dziko lonse lapansi, malinga nkukula kwa chipongwe chimene anthu onse aja adaachita.

3Tsono adagamula kuti aliyense amene sadamvere mau ake aphedwe.

4Atatsiriza kufotokoza zolinga zake, Nebukadinezara adaitana Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wa ankhondo ake, wachiŵiri kwa mfumu, namuuza kuti,

5“Ine Nebukadinezara, mfumu yaikulu, mbuye wa dziko lonse lapansi, ndikukulamula kuti ukangochoka pano, utenge asilikali odziŵa kumenya nkhondo 120,000 oyenda pansi ndi 12,000 okwera pa akavalo.

6Ukamenyane ndi anthu a ku maiko onse akuzambwe amene sadamvere lamulo langa.

7Uŵauze kuti akonzeretu dothi ndi madzi, chifukwa ndikubwera ndi ukali kudzaŵaononga. Mapazi a ankhondo anga adzapondaponda pa dziko lao lonse, ndipo ndidzalipereka kwa ankhondo omwewo kuti alifunkhe.

8Zigwa zao zidzadzaza ndi ovulala ao, mitsinje yonse yaing'ono ndi yaikulu yomwe idzadzaza ndi mitembo mpaka kusefukira.

9Tsono otsala ndidzaŵatumiza ku ukapolo mpaka ku malire a dziko lapansi.

10“Iwe pita tsopano, ukandigonjetsere maiko ao onse ine ndisanafike. Akakugonjera, uŵasunge mpaka nthaŵi itafika yoti ndidzaŵalange.

11Koma akakachita mnjunju, usakaŵachitire chifundo, ukaŵaphe ndi kufunkha dziko lonselo.

12Ndikulumbira pali moyo wanga ndi mphamvu zanga, kuti zimene ndanenazi ndidzazichitadi monga momwe ndalumbiriramu.

13Tsono iwe usaphwanye ndi limodzi lomwe mwa malamulo a ine mbuye wako. Utsate mokhulupirika zonse zimene ndakulamula, ndipo usachedwe.”

Holofernesi amenya nkhondo

14Atalekana ndi mfumu, Holofernesi adaitana olamulira ankhondo, atsogoleri ndi akuluakulu a ankhondo a Aasiriya.

15Adaŵauza kuti asonkhanitse anthu osankhidwa, monga mfumu idaalamulira, oyenda pansi 120,000 ndi 12,000 oponya mivi okwera pa akavalo.

16Adaŵandandika pa mizere yankhondo, monga amachitira atsogoleri ankhondo.

17Adatenganso gulu lalikulu la ngamira, abulu ndi nyulu zonyamula katundu, ndiponso nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe zosaŵerengeka zoti ankhondo azikadya.

18Adatenganso zofunika zina zonse za ankhondo akewo, ndiponso golide wambiri ndi siliva kuchokera ku nyumba ya mfumu.

19Tsono onsewo adanyamuka, iye ndi gulu lake lonse lankhondo, gululo lili patsogolo pa mfumu Nebukadinezara. Adafuna kuti likaphimbe dziko lonse lakuzambwe ndi magaleta ankhondo ndi anthu okwera akavalo ndi oyenda pansi.

20Owe. 7.12; Yow. 2.2-11Pamodzi ndi iwowo kudapitanso chigulu cha anthu ochuluka ngati dzombe kapena ngati mchenga wa pa dziko lapansi. Unalidi unyinji wa anthu osaŵerengeka.

21Atachoka ku Ninive, adayenda masiku atatu nkukafika ku chigwa cha Bektileti. Kumeneko adamanga zithando zankhondo pafupi ndi phiri la kumpoto kwa Silisiya.

22Kuchokera kumeneko Holofernesi adapita ku dziko lamapiri ndi ankhondo ake onse, apansi, apakavalo ndi am'magaleta.

23Adaononga Puti ndi Ludi, nafunkha katundu wa anthu onse a ku Rasisi ndi wa Aismaele okhala m'mphepete mwa chipululu, kumwera kwa dziko la Akelea.

24Pambuyo pake adaoloka Yufurate nabzola dziko la Mesopotamiya. Adaononga mizinda yonse yamalinga ya m'mbali mwa mtsinje wa Abironi mpaka ku nyanja yamchere.

25Adagonjetsa dziko lonse la Silisiya napha anthu onse okana kumgonjera. Motero adafika ku malire akumwera a dera la Yafeti kuyang'anana ndi dziko la Arabiya.

26Adazinga Amidiyani natentha mahema ao, nkulanda nkhosa zao.

27Pa nthaŵi yodula tirigu, adatsikira ku chigwa cha Damasiko, nakatentha dzinthu dzao, nkuwononga ziŵeto zao. Kenaka adapasula mizinda yao ndi dziko lao lomwe, napha achinyamata ao onse ndi lupanga.

28Nchifukwa chake anthu onse a m'mbali mwa nyanja adayamba kuchita naye mantha. Anthu okhala ku Tiro ndi ku Sidoni, ku Suri ndi ku Okina ndi ku Yaminiya, mpaka ku Azote ndi ku Askaloni, onsewo adachita naye mantha kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help