1Zitapita zimenezi, Abisalomu adadzipezera galeta lokokedwa ndi akavalo, napezanso anthu makumi asanu omamperekeza.
2Abisalomu ankadzuka m'mamaŵa, namaima pa njira ya ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi mlandu kuti apite kwa mfumu kukaweruzidwa, Abisalomu ankamuitana, namufunsa kuti, “Ukuchokera ku mzinda uti?” Akayankha kuti, “Mtumiki wanune, ndine wa fuko lakutilakuti, m'dziko la Israele,”
3Abisalomu ankamuuza kuti, “Taona, zimene ukunenazi nzabwino ndi zolungama. Koma mfumu sidaike munthu woti azimva madandaulo anu.”
4Ndipo ankapitirira kunena kuti, “Achikhala adaaika ine, kuti ndikhale woweruza m'dziko muno! Bwenzi munthu aliyense amene ali ndi mlandu, kapena vuto lina lililonse, atabwera kwa ine, ndipo ine ndikadamuweruza molungama munthuyo.”
5Choncho nthaŵi zonse munthu ankati akasendera pafupi kudzalambira Abisalomuyo, iye ankatambalitsa mkono, ndipo ankamgwira munthuyo namumpsompsona.
6Umu ndimo m'mene Abisalomu ankachitira ndi Aisraele onse amene ankabwera kwa mfumu kuti akaweruzidwe. Motero Abisalomu adaŵagwira mitima Aisraele.
7Patapita zaka zinai, Abisalomu adapempha mfumu kuti, “Chonde mundilole kuti ndipite ku Hebroni kuti ndikachite zimene ndidalumbira kwa Chauta.
8Nthaŵi imene ndinkakhala ku Gesuri ku Aramu, ndidachita lumbiro lakuti, ‘Chauta akadzandibwezeradi ku Yerusalemu, ndidzampembedza ku Hebroni.’ ”
9Apo mfumu idamuuza kuti, “Upite ndi mtendere.” Choncho Abisalomu adanyamuka napita ku Hebroni.
10Koma Abisalomu adatuma amithenga m'seri kwa mafuko onse a Aisraele kukanena kuti, “Malinga mukangomva kulira kwa lipenga, munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu ya ku Hebroni.’ ”
11Abisalomu popita, adatenga anthu okwanira 200 a ku Yerusalemu. Iwoŵa anali alendo oitanidwa chabe, mwakuti ankangopita osadziŵa chilichonse.
12Pamene Abisalomu ankapereka nsembe ku Hebroni, adatumiza mau kukaitana Ahitofele, mlangizi wa Davide wa ku mzinda wa Gilo. Motero chiwembucho chidakula kwambiri. Nawonso anthu otsatira Abisalomu adanka nachulukirachulukira.
Davide athaŵa Abisalomu.13Tsiku lina wamthenga adafika kwa Davide kudzanena kuti, “Aisraele onse ali pambuyo pa Abisalomu.”
14Ndiye Davide adauza ankhondo ake amene anali naye ku Yerusalemu kuti, “Nyamukani, tiyeni tithaŵe kuti tingasoŵe mpata wothaŵira Abisalomu. Fulumirani, kuti angatipeze mwamsanga, ndipo angatithire nkhondo ndi kutipha tonse mumzinda muno.”
15Apo nduna za mfumu zija zidauza mfumu kuti, “Amfumu, ife ankhondo anu tili okonzeka kuchita chinthu chilichonse chimene inu mungachitsimikize kuchita.”
16Choncho mfumu idatuluka, nipita pamodzi ndi anthu onse a pabanja pake. Koma mfumuyo idasiya azikazi ake khumi kuti azisunga mudzi.
17Pamene mfumu idatuluka, anthu onse adaitsata. Onsewo adakaima pa nyumba yomalizira.
18Ankhondo ake onse adayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti kudzanso Agiti okwanira 600 amene adamtsata kuchokera ku Gati, nawonso adayenda pamaso pa mfumu.
19Zitatero, mfumu idafunsa Itai Mgiti kuti, “Chifukwa chiyani ukupita nafe pamodzi? Bwerera, ukakhale ndi mfumu ija. Paja iwe ndiwe mlendo, ndiponso ndiwe munthu wothaŵa kwanu, motero bwerera.
20Iwe wangobwera dzulo. Ndiye ine ndikutenge lero, kuti uzinka nuyenda nane? Ine ndemwe sindikudziŵa kumene ndikupita. Bwerera ndi anthu akwanu, ndipo Chauta akukomere mtima ndi kukuchitira zabwino mwa kukhulupirika kwake.”
21Koma Itai adayankha mfumu kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe mbuyanga mfumu, kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzakhale, kaya mpa imfa kaya mpa moyo, ine mtumiki wanu ndidzakhalanso komweko.”
22Choncho Davide adauza Itai kuti, “Chabwino, tiye.” Motero Itai Mgiti uja adaoloka mtsinje wa Kidroni, pamodzi ndi anthu ake, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe amene anali naye.
23Tsono anthu onse adayamba kulira mofuula pamene mfumu ndi otsatira ake ankapita. Choncho mfumuyo idaoloka mtsinjewo, ndipo anthu onse adamtsatira kupita ku chipululu.
24Ansembe, Abiyatara ndi Zadoki adapita nao pamodzi ndi Alevi onse, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adatula pansi Bokosilo, mpaka anthu onse atatuluka mumzindamo.
25Pamenepo mfumu idauza Zadoki kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chautali, mubwerere nalo mu mzinda. Chauta akandikomera mtima, adzandibweza kuti ndidzaliwonenso Bokosilo pamodzi ndi malo ake omwe.
26Koma akapanda kukondwera nane, chabwino, andichite zomwe zimkomere.”
27Ndipo mfumuyo idauzanso Zadoki wansembe uja kuti, “Bwerera ku mzinda mwamtendere, iwe pamodzi ndi Abiyatara, ndi ana anu aŵiri, mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.
28Tsono ine ndidzadikira ku madooko a Yordani ku chipululu mpaka nditalandira mau ochokera kwa inu ondiwuza m'mene ziliri zinthu.”
29Pamenepo Zadoki ndi Abiyatara adanyamula Bokosi lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo adakakhala kumeneko.
30Koma Davide adakwera phiri la Olivi, akunka nalira, osavala kanthu kuphazi, atafundira kumutu. Anthu onse amene anali naye adafundanso kumutu, ndipo nawonso adakwera phiri akunka nalira.
31Kenaka Davide adamva kuti Ahitofele ali pakati pa anthu ogalukira, pamodzi ndi Abisalomu. Tsono Davideyo adayamba kupemphera, adati, “Ine Chauta ndikukupemphani, musandutse uphungu wa Ahitofele kuti ukhale uchitsiru.”
32Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki adadzakumana naye atang'amba mwinjiro ndi kudzithira dothi kumutu.
33Davide adamuuza kuti, “Ukapita nane, sizindithandiza kwenikweni.
34Koma makamaka iwe ubwerere ku mzinda, ukamuuze Abisalomu kuti, ‘Inu amfumu, ine ndidzakhala mtumiki wanu. Monga kale ndinali mtumiki wa bambo wanu, momwemonso tsopano ndidzakhala mtumiki wanu.’ Ukakatero ukandigonjetsera uphungu wa Ahitofele.
35Kodi Zadoki ndi Abiyatara si ansembe amene ali nawe kumeneko? Tsono chilichonse chimene ungachimve kunyumba kwa mfumu, ukaŵauze ansembe amenewo.
36Ahimaazi, mwana wa Zadoki ndiponso Yonatani, mwana wa Abiyatara, nawonso ali komweko. Ndipo podzera mwa iwowo udzandiwuza zonse zimene udzamve.”
37Choncho Husai, bwenzi la Davide, adaloŵa mu mzinda, nthaŵi yomwe Abisalomu ankaloŵa mu Yerusalemu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.