2 Ate. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Khristu asanabwerenso, kudzafika Munthu Woipitsitsa uja

1 1Ate. 4.15-17 Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikakumane naye, tifuna kukupemphani kanthu, abale.

2Maganizo anu asasokonezeke msanga, ndipo musaopsedwe ndi mau akuti, “Tsiku la Ambuye lafika,” ngakhale anene kuti mauwo ngochokera kwa Mzimu Woyera, kapena kuti taŵanena ndife, kapena tachita kuŵalemba m'kalata.

3Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu.

4Dan. 11.36; Ezek. 28.2 Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

5Kodi simukukumbukira kuti ndinkakuuzani zimenezi muja ndinali kwanuko?

6Mukudziŵanso chimene chikumletsa kuwoneka tsopano, koma adzaululuka ndithu pa nthaŵi yake.

7Ngakhale tsopano lomwe lino uchimo wayamba kugwira ntchito mobisika. Koma zoyenera kuchitikazo sizidzachitika mpaka amene akuletsa uchimowo tsopano atayamba wachotsedwa.

8Yes. 11.4 Tsono pamenepo Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ndipo Ambuye Yesu adzamthetsa ndi mpweya wa m'kamwa mwake, nkumuwonongeratu ndi maonekedwe ake aulemerero a kubwera kwake.

9 Mt. 24.24 Munthu Woipitsitsa uja adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzachita zamphamvu zosiyanasiyana, ndiponso zizindikiro ndi zozizwitsa zonyenga.

10Mwa njira iliyonse adzanyenga anthu amene adzaonongedwa chifukwa chokana kukonda choona chimene chikadaŵapulumutsa.

11Nchifukwa chake Mulungu adzatumiza mphamvu zoŵasokoneza, kuti akhulupirire zonama.

12Motero adzalangidwa onse amene sadakhulupirire choona, koma adakondwerera kusalungama.

Mulungu adakusankhani kuti mupulumuke

13Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.

14Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.

15Tsono abale, khalani olimbika, ndipo mugwiritse miyambo imene tidakuphunzitsani ndi mau apakamwa kapena am'makalata.

16Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma.

17Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help