1Nthaŵi imene mfumu Davide anali atakhazikika m'nyumba mwake, Chauta adampumuza kwa adani ake onse omzungulira.
2Tsono adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.”
3Natani adauza mfumu kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Chauta ali nanu.”
4Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti,
5“Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo?
6Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema.
7Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti, bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?
8Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele.
9Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzakumveketsa dzina lako kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.
10Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija,
11kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse. Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako.
12Mas. 89.3, 4; 132.11; Yoh. 7.42; Ntc. 2.30 Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako ku manda, ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba.
13Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba yomveketsa dzina langa, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya.
14Mas. 89.26, 27; 2Ako. 6.18; Ahe. 1.5 Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake.
15Koma sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo, amene ndidamkana, kuti uloŵe ufumu ndiwe.
16Mas. 89.36, 37 Tsono banja lako pamodzi ndi ufumu wako ndidzazikhazikitsa mpaka muyaya pamaso panga. Ndithudi, ufumu wako udzakhazikika osatha konse.”
17Natani adalankhula ndi Davide potsata mau onseŵa, ndiponso potsata zimene adaziwona m'masomphenyaŵa.
Pemphero la Davide lothokoza.(1 Mbi. 17.16-27)18Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa?
19Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Chauta Wamphamvuzonse. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandionetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Ambuye Chauta.
20“Nanga ine ndingathe kunena chiyaninso kwa Inu? Paja mumandidziŵa mtumiki wanune, Inu Chauta Wamphamvuzonse.
21Mwachita zazikulu zonsezi chifukwa cha lonjezo lanu, ndiponso potsata zimene mtima wanu umafuna, kuti mtumiki wanune ndidziŵe.
22“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
23Deut. 4.34 Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola ku Ejipito kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamodzi ndi milungu yao, pamene ankafika anthu anu.
24Mudadzikhazikitsira anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anuanu mpaka muyaya. Ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao.
25“Tsopano Inu, Chauta Mulungu, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa. Muchite monga momwe mudaanenera.
26Choncho dzina lanu lidzalemekezedwa mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wolamulira Aisraele.’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.
27“Inu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Aisraele, mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pemphero limeneli kwa inu.
28Ndipo tsopano Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu, ndipo mau anu ngoona. Mwalonjeza kuti mudzandichitira zabwino zotere ine mtumiki wanu.
29Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti mwatero ndinu Ambuye Chauta, choncho banja la mtumiki wanune lidzadalitsidwadi mpaka muyaya.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.