1 Mas. 38.1 Inu Chauta, musandikalipire ndi kundidzudzula,
musapse mtima ndi kundilanga.
2Ndichitireni chifundo, Inu Chauta,
chifukwa chakuti ndine wofooka.
Limbitseni, Inu Chauta,
chifukwa m'nkhongono mwanga mwaweyeseka.
3Mtima wanganso wazunzika kwambiri.
Nanga Inu Chauta,
zimenezi zidzakhala zikuchitika mpaka liti?
4Bwerani, Inu Chauta, mudzandilanditse.
Mundipulumutse
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5Anthu akufa sangathe kukutamandani ku manda.
M'dziko la akufa ndani angathe kukuyamikani?
6Ndatopa nkubuula kwambiri.
Ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi
usiku uliwonse.
Ndimakhathamiza pogona panga
chifukwa cha kulira kwanga.
7Maso anga atupa chifukwa cha kulira,
afooka chifukwa cha adani anga onse.
8 Mt. 7.23; Lk. 13.27 Chokani apa, inu nonse ochita zoipa,
Chauta wamva kulira kwanga.
9Chauta wamva pemphero langa
ndipo wandiyankha.
10Adani anga onse adzagonjetsedwa mwa manyazi
ndipo adzagwidwa ndi mantha,
modzidzimuka onse adzathaŵa motaya mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.