Mla. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.

2Ndinkaganiza kuti akufa aja amene adapita kale ndi amwai kwambiri kupambana amene akadali ndi moyo.

3Koma wopambana onsewo ndi amene sadabadwe nkomwe, ndipo ntchito zoipa zimene zimachitika pansi pano sadaziwone.

4Tsono ndidazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

5Paja akuti chitsiru chimangoti manja khodobala, nkumasoŵa chakudya mpaka kumafa ndi njala.

6Komabe nkwabwino kukhala ndi moyo wabata wodzaza dzanja limodzi, kupambana kutekeseka ndi ntchito zolemetsa zodzaza manja aŵiri, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungozivuta chabe.

7Ndidazindikira chinanso chopanda phindu pansi pano:

8Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa.

9Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana.

10Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.

11Ndiponso aŵiri akagona pamodzi amafunditsana. Koma nanga mmodzi angathe kudzifunditsa bwanji?

12Nkotheka kuti munthu apambane mnzake amene ali yekha, koma pakakhala aŵiri, iwoŵa adzalimbana naye. Chingwe cha nkhosi zitatu sichidukirapo.

13Mnyamata wosauka ndi wanzeru ali bwino kupambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene siikumvanso malangizo.

14Mnyamatayo atha kukhala kuti adachita kuchokera ku ndende kudzaloŵa ufumu, kapenanso kuti adabadwa mmphaŵi m'dziko mwake momwemo.

15Ndinkaganiza za anthu onse amene amakhala pansi pano, ndipo ndidazindikira kuti pakati paopo panali mnyamata uja amene anali wodzatenga malo a mfumu.

16Mfumu ikhoza kulamulira anthu osaŵerengeka, komabe itamwalira, palibe aliyense amene adzayamikire zomwe mfumuyo idachita. Ndithudi, zimenezinso nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help