1Aisraele anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi Abenjamini.”
2Anthuwo adafika ku Betele, nakhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu mpaka madzulo, ndipo adafuula nalira ndi chisoni chambiri.
3Iwowo ankati, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani zimenezi zachitika m'dziko la Aisraele, kuti lero fuko la Benjamini lilipafupi kuchotsedwa m'dziko la Israele?”
4M'maŵa mwake anthuwo adadzuka m'mamaŵa. Adamanga guwa kumeneko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere.
5Aisraele adati, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Aisraele amene sadafike ku msonkhano wa Chauta?” Paja anali atachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene sadapite kwa Chauta ku Mizipa kuti, “Munthu wotero ayenera kuphedwa.”
6Koma Aisraele adamvera chifundo abale ao a fuko la Benjamini nati, “Fuko limodzi lachotsedwa m'dziko la Israele lero lino.
7Kodi tidzaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti talumbira kwa Chauta kuti sitidzaŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire?”
8Tsono iwowo adafunsa kuti, “Kodi m'fuko la Aisraele ndani amene sadabwere kwa Chauta ku Mizipa?” Tsono kudapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi amene adabwera ku msonkhano kuzithando kuja.
9Pakuti m'mene anthu ankasonkhana, adangoona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi.
10Choncho mpingo udatumiza kumeneko anthu 12,000 mwa anthu ao, olimba kwambiri, naŵalamula kuti, “Pitani mukaŵaphe anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndi lupanga. Mukaphenso akazi ndi ana omwe.
11Zimene mukachite ndi izi, ‘Mukaphe amuna onse ndiponso mkazi aliyense amene adadziŵapo kale mwamuna.’ ”
12Pakati pa anthu a ku Yabesi-Giliyadi adapeza anamwali 400 amene sadadziŵepo amuna. Amenewo adabwera nawo ku zithando ku Silo, mzinda umene uli m'dziko la Kanani.
13Pamenepo mpingo wonse udatumiza uthenga kwa Abenjamini amene anali ku thanthwe la ku Rimoni kukaŵauza kuti nkhondo yatha.
14Abenjamini adabwera nthaŵi imeneyo. Ndipo Aisraele adaŵapatsa Abenjaminiwo akazi a ku Yabesi-Giliyadi amene sadaŵaphe aja. Koma adapereŵera, osakwanira.
15Aisraele adaŵamvera chifundo Abenjaminiwo chifukwa chakuti Chauta anali atachotsako anthu ena mu fuko limodzi la Aisraele.
16Tsono akuluakulu a mpingo adati, “Kodi tikaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti akazi a fuko la Benjamini adaphedwa?”
17Iwowo adati, “Nkofunika kuti anthu otsalira a fuko la Benjamini akhale nazo zidzukulu, kuti fuko lao lisafafanizike pa mtundu wa Israele.
18Komabe sitingathe kuŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire.” Paja Aisraele anali atalumbira kuti, “Akhale wotembereredwa munthu amene apatse Mbenjamini mkazi.”
19Choncho adati, “Paja kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Chauta ku mzinda wa Silo.” Silo ali kumpoto kwa Betele, kuvuma kwa Lebona.
20Ndiye adalamula Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale m'minda yamphesa,
21ndipo muzikapenyetsetsa. Ana aakazi a ku Silo akamakabwera kudzavina magule, pomwepo mutuluke m'minda yamphesa ndi kukaŵagwira, aliyense wake, nkupita nawo ku dziko la Benjamini.
22Tsono pamene azibambo kapena alongo ao adzabwere kuno kudzadandaula, ife tidzaŵauza kuti, ‘Chonde, tiloleni kuti tiŵatenge, popeza kuti anthuŵa sitidaŵapezere akazi pomenya nkhondo, ndipo inunso simudachita kuŵapatsa akaziwo. Mukadatero bwenzi tsopano mutapalamula.’ ”
23Abenjaminiwo adachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja adatengapo ao, molingana ndi chiŵerengero chao, napita nawo. Kenaka adanyamuka kubwerera ku dziko lakwao nakamanganso mizinda yatsopano ndi kumakhalamo.
24Tsono Aisraele adachoka kumeneko nthaŵi yomweyo, napita aliyense ku fuko lake ndiponso ku banja lake, ndipo kuchokera kumeneko aliyense adapita ku dera la choloŵa chake.
25 Owe. 17.6 Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israele. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkakomera mwiniwakeyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.