1 Yos. 21.1-42 Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko, kuti,
2“Ulamule Aisraele kuti pa choloŵa chaocho, apatseko Alevi mizinda yoti azikhalamo. Ndipo Aleviwo muŵapatsenso mabusa pozungulira mizindayo.
3Mizindayo idzakhala yao yoti azikhalamo, ndipo mabusa ao adzakhala odyetseramo ng'ombe zao, zoŵeta zao ndi nyama zao zonse.
4Mabusa a mizindayo amene mudzapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mzinda, adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mzindawo.
5Uyese kunja kwa mzindawo, kuvuma mamita 900, kumwera mamita 900, kuzambwe mamita 900, kumpoto mamita 900, ndipo mzindawo ukhale pakati. Dziko limeneli lidzakhala busa la mizinda yaoyo.”
Mizinda yopulumukirako(Deut. 19.1-13; Yos. 20.1-9)6“Mizinda imene mudzapatse Aleviyo idzakhale mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako, kumene muzidzalola kuti munthu wopha mnzake mwangozi athaŵireko. Ndipo mudzaŵapatsenso mizinda ina 42, kuwonjezera pa mizinda imeneyo.
7Mizinda imene mudzapatse Alevi idzakhale 48 yonse pamodzi, kuphatikizanso ndi mabusa ao.
8Pamene mukupatula mizinda imeneyi pa choloŵa cha Aisraele, muchotse mizinda yambiri pa mafuko aakulu, ndipo muchotse mizinda pang'ono pa mafuko aang'ono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa choloŵa chimene lalandira.”
9 Deut. 19.2-4; Yos. 20.1-9 Tsono Chauta adauza Mose kuti,
10“Uza Aisraele kuti: Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko la Kanani,
11mupatule mizinda ina kuti ikhale mizinda yanu yothaŵirako, kumene munthu wopha mnzake mwangozi azithaŵirako.
12Mizindayo idzakhala malo obisalamo pothaŵa munthu wofuna kubwezera choipa, kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo asaphedwe, mpaka akaime pamaso pa mpingo kuti umuweruze.
13Mizinda imene mudzaperekeyo idzakhala mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako.
14Mudzapereke mizinda itatu patsidya la kuvuma la mtsinje wa Yordani, ndi mizinda itatu m'dziko la Kanani, kuti ikhale mizinda yothaŵirako.
15Mizinda isanu ndi umodziyo idzakhala yothaŵirako Aisraele, alendo ndi anthu okhala pakati pao, kuti wina aliyense wopha munthu mnzake mwangozi azithaŵirako.
16“Koma ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo nkufa, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Ndipo wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
17Ngati munthu amenya mnzake ndi mwala, mwala wake woti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
18Kapena munthu akamenya mnzake ndi chibonga choti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
19Mbale wake wa munthu wakufayo ndiye adzaphe wopha mnzakeyo. Akadzangokumana, wopha mnzakeyo adzamuphe ndi munthu wolipsira magaziyo.
20Ndipo ngati munthu abaya mnzake chifukwa cha chidani, kapena amulasa ndi chida atamubisalira, mnzakeyo naafa,
21kapena kumpanda ndi dzanja lake modana naye, mnzakeyo naafa, ndiye kuti amene adamenya mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ndi wopha munthu ameneyo. Mbale wa munthu wakufayo ndiye aphe wopha mnzakeyo akangokumana naye.
22“Koma ngati munthu abaya mnzake mwangozi osati chifukwa cha chidani, kapena alasa mnzake ndi chida osamubisalira,
23kapena amulasa ndi mwala woti nkupha munthu, koma amlasa osamuwona mnzakeyo,
24pamenepo mpingo uweruze pakati pa munthu wopha mnzakeyo ndi mbale wa munthu wakufayo, potsata malangizo ameneŵa.
25Mpingo umpulumutse munthu wopha mnzakeyo m'manja mwa mbale wa munthu wakufayo. Ndipo um'bweze munthuyo ku mzinda wake wothaŵirako kumene adathaŵira. Adzakhala komweko mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira.
26Koma ngati munthu wopha mnzake mwangoziyo atuluka nthaŵi iliyonse kunja kwa malire a mzinda umene adathaŵiramo,
27ndipo mbale wa munthu wakufa uja ampeza ali kunja kwa malire a mzindawo, nkupha wopha mnzake uja, sadzapalamula mlandu wopha munthu.
28Pajatu munthuyo ayenera kukhala mu mzinda umene adathaŵiramo mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira. Koma mkulu wa ansembe onse atamwalira, wopha mnzakeyo angathe kubwerera ku dziko lake.
29“Zimenezi zikhale malamulo ndi malangizo kwa inu pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.
30Deut. 17.6; 19.15 Ngati wina aliyense apha mnzake, wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa, mboni zitapereka umboni wao. Koma munthu asaphedwe pamene munthu mmodzi yekha wapereka umboni.
31Kuwonjezera apo, musalandire dipo loombolera munthu wopha mnzake amene wapalamula mlandu wopha munthu. Koma munthu ameneyo ayenera kuphedwa ndithu.
32Ndipo musalandire dipo loombolera munthu amene ali mu mzinda wake wothaŵirako kuti abwerere ndi kukakhala ku dziko lake, mkulu wa ansembeyo asanamwalire.
33Musaipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amaipitsa dziko, ndipo nkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa m'menemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene adakhetsa magaziyo.
34Musaipitse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndikukhalamo. Paja Ine Chauta ndimakhala pakati pa Aisraele.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.