1 Yes. 10.5-34; 14.24-27; Zef. 2.13-15 Uwu ndi uthenga wonena za mzinda wa Ninive. Uthengawu ukufotokoza za zimene Nahumu wa ku Elikosi adaziwona m'masomphenya.
2Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira.
Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali.
Chauta amalipsira amaliwongo ake
amakwiyira adani ake.
3Chauta ndi wamphamvu zedi.
Ndi wosakwiya msanga,
komabe sadzalola kuti munthu wochimwa
akhale wosalangidwa.
Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu
ndi mphepo yamkuntho,
mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
4Akangoilamula nyanja, imauma,
amaumitsanso mitsinje yonse.
Zomera za ku Basani ndi za ku Karimele zimauma,
maluŵa a ku Lebanoni amafota.
5Mapiri amagwedezeka pamaso pake,
magomo amasungunuka.
Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake,
ndiye kuti dziko ndi zonse zokhala m'menemo.
6Kodi ndani angathe kuima pamaso pa Chauta,
Iye atakwiya?
Kodi ndani angathe kupirira ukali wake?
Ukali wake umayaka ngati moto,
matanthwe amadyukuka pamaso pake.
7Chauta ndi wabwino,
ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto.
Amasamala onse amene amadalira Iye.
8Koma ndi madzi achigumula adzaononga adani ake,
ndipo adzaŵapirikitsira ku malo amdima.
9Kodi mukukonzekera kumchita Chauta
chiwembu chotani?
Adzakuwonongani kotheratu.
Sadzalira kuŵalipsira kaŵiri adani akewo.
10Adzaŵatentha kotheratu
ngati ziyangoyango za minga
ndiponso ngati ziputu zouma.
11Ku Ninive kudachokera munthu wa cholinga choipa,
wofuna kuchita Chauta chiwembu.
12Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti,
“Ngakhale Aasiriyawo ndi amphamvu ndiponso ndi ambiri,
adzaonongeka ndi kutheratu.
Koma inu anthu anga, ngakhale ndidakulangani,
sindidzakulanganinso.
13Tsopano ndidzathyola goli
limene adakuikani m'khosi,
ndipo ndidzadula maunyolo anu.”
14Za inu a ku Ninive Chauta walamula kuti,
“Simudzakhala ndi adzukulu otchedwa dzina lanu.
Ndidzaononga mafano osema ndi oumba
m'nyumba ya milungu yanu.
Ndidzakukumbirani manda,
chifukwa ndinu opandapake.”
15 Yes. 52.7 Ona, kumapiri kukubwera munthu,
iyeyu ali ndi uthenga wabwino,
akulengeza za mtendere.
Inu a ku Yuda muzisunga masiku achikondwerero;
zimene mudalumbira, muzizichitadi.
Anthu oipawo sadzakuthiraninso nkhondo.
Adaonongeka kotheratu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.