1Tsono Zofari wa ku Naama adayankha kuti,
2“Kodi mau ambirimbiriŵa nkukhala osaŵayankha?
Kodi kulongolola nkumulungamitsa munthu?
3Iwe Yobe, kodi anthu nkukhala chete
atamva kubwebweta kwakoku?
Kodi ukamanyodola,
sadzakhalapo wina aliyense wokudzudzula?
4Iwe umati mau akowo ndi oona,
ukuti ndiwe wangwiro pamaso pa Mulungu.
5Koma ha, achikhala Mulungu adaalankhula,
achikhala adaakudzudzula,
6achikhala adaakuululira zinsinsi za nzeru!
Paja Iye uja nzeru zake ndi zozama zedi.
Udziŵe tsono kuti Mulungu akukulanga pang'ono,
mosalingana nkuchuluka kwa zolakwa zako.
7“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu?
Kodi ungathe kudziŵa kukula kwa nzeru za Mphambe?
8Malire a nzeru zake ali kutali kuposa mlengalenga.
Nanga iwe ungachitepo chiyani?
Malire a nzeru zake ndi ozama
kupitirira dziko la anthu akufa.
Nanga iwe ungathe kudziŵapo chiyani?
9Muyeso wa nzeru zake ndi wautali
kupambana kutalika kwa dziko lapansi,
ndi kupingasa kwa nyanja zamchere.
10Mulungu akabwera nakutsekera m'ndende,
ndipo akakutulutsira ku bwalo la milandu,
ndani angathe kumuletsa?
11Mulungu amazindikira anthu abodza.
Pamene pali zolakwa, Iye uja nkupanda kudziŵa?
12Paja amati, Chitsiru nchitsiru ndithu,
ndipo nyama ndi nyama ndithu.
13“Iwe Yobe, mumtima mwako ukhale wolungama,
upemphe chifundo kwa Mulungu.
14Ngati mumtima mwako muli cholakwa, uchichotse,
choipa chilichonse chisakhale m'moyo mwako.
15Ukatero, ndiye kuti manyazi ako onse adzatha,
sudzazyolikanso pamaso pa anthu.
Mtima wako udzakhazikika, ndipo sudzaopa kalikonse.
16Zoŵaŵa zakozi udzaziiŵala,
zidzakhala ngati madzi amene apita kale.
17Pamenepo moyo wako udzaŵala kupambana dzuŵa.
Usiku udzakhala ngati usana kwa iwe.
18Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo.
Mulungu adzakutchinjiriza,
ndipo udzapumula mwamtendere.
19Nthaŵi yogona palibe amene adzakuwopse.
Ambiri adzakupempha kuti uŵachitire zabwino.
20Anthu oipa nawonso adzafunafuna thandizo,
koma sadzaona njira yopulumukira,
chiyembekezo chao ndi imfa basi.”
Yobe
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.