1Inu Mulungu mwatitaya ife,
mwatiwonongera otiteteza.
Mwatikwiyira,
tibwezeni mwakale.
2Inu mwagwedeza dziko ndi chivomezi,
Inu mwaling'amba.
Konzani ming'alu yake,
pakuti likugwedezeka koopsa,
3Inu mwalola anthu anu
kuti aone mavuto aakulu.
Mwatipatsa vinyo wachilango kuti timwe,
ndipo tikudzandira naye.
4Komabe Inu mwatikwezera mbendera
ife amene timakuwopani,
kuti tisonkhanireko pothaŵa uta wankhondo.
5Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja,
mutiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke.
6Mulungu ali ku malo ake oyera, walonjeza kuti,
“Ndidzakugaŵirani dziko la Sekemu mokondwa,
ndidzakulemberani malire m'chigwa cha Sukoti.
7“Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga.
Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera,
Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu.
8“Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine.
Edomu adzakhala poponda nsapato zanga.
Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.”
9Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga?
Ndani adzanditsogolere ku Edomu?
10Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya,
ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu.
11Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo,
pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake.
12Mulungu akakhala nafe,
tidzamenya nkhondo molimba mtima,
pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.