1Ataligonjetsa dziko lonselo, Aisraele onse adasonkhana ku Silo, ndipo adamangako chihema chamsonkhano.
2Nthaŵi imeneyo nkuti mafuko asanu ndi aŵiri asanapatsidwe magawo ao a dzikolo.
3Motero Yoswa adafunsa Aisraele kuti, “Kodi mudzadikira mpaka liti kuti muloŵe m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakupatsani?
4Tandipatsani amuna atatu a fuko lililonse. Ameneŵa ndiŵatuma kuti akayendere dziko lonselo, ndipo alembe bwino magawo ake onse, kuti tithandizidwe poligaŵa. Atatero, abwererenso kuno kwa ine.
5Adzaligaŵe dzikolo magawo asanu ndi aŵiri. Yuda adzakhala m'dziko lake kumwera, ndipo Yosefe adzakhala m'dziko lake kumpoto.
6Mudzalembe mau ofotokoza za magawo asanu ndi aŵiriwo a dziko limenelo, ndi kudzandipatsa ine. Ineyo ndiye ndidzakuchitireni maere pamaso pa Chauta, Mulungu wathu.
7Alevi okha sadzalandira nao gawo la dzikolo, popeza kuti gawo lao ndi kutumikira Chauta pa unsembe. Fuko la Gadi ndi la Rubeni ndi theka la fuko la Manase adalandira kale dziko lao kuvuma kwa Yordani. Mose, mtumiki wa Chauta, ndiye adaŵapatsa.”
8Tsono anthuwo adapitadi kukalemba za dzikolo, Yoswa ataŵalangiza kuti, “Pitani, kaliyendereni dziko lonselo, ndipo mukalembe bwino za dzikolo. Tsono mutatero, mubwererenso kwa ine kuno. Ine ndidzakuchitirani maere pamaso pa Chauta konkuno ku Silo.”
9Pamenepo anthuwo adakaliyendera dziko lonselo, nalemba bwino m'buku za dzikolo. Adagaŵa dzikolo magawo asanu ndi aŵiri, ndipo adalembanso mndandanda wa midzi yonse. Atatero adabwerera kwa Yoswa ku zithando ku Silo kuja.
10Tsono Yoswa adachita maere, naŵapemphera nzeru kwa Chauta. Ndipo fuko lililonse la Aisraele adalipatsa gawo la dzikolo.
Dziko la Benjamini.11Mabanja a fuko la Benjamini adalandira dziko la pakati pa Yuda ndi Yosefe.
12Kumpoto malire ao adayambira ku mtsinje wa Yordani, nakwera chitunda cha kumpoto kwa Yeriko nabzola dziko lamapiri chakuzambwe, nakafika ku chipululu cha Betaveni.
13Tsono malirewo adaloza ku Luzi, ndi kutsata mbali ya phiri loti Luzi, (lotchedwanso Betele). Tsono adatsikira ku Ataroti-Adara, kubzola phiri lili kumwera kwa Betehoroni wakunsi.
14Ndipo malirewo adaloŵanso kwina, nalunjika kumwera kuchokera kuzambwe kwake kwa phiri limene limayang'anana ndi Betehoroni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati-Baala (wotchedwanso Kiriyati-Yeyarimu), mzinda wa fuko la Yuda. Ameneŵa ndiwo anali malire akuzambwe.
15Malire akumwera adayambira pamphepete penipeni pa Kiriyati-Yearimu, napita kuzambwe mpaka kukafika ku Akasupe a ku Nefutowa.
16Adatsikira m'mphepete mwa phiri limene limayang'anana ndi chigwa cha Benihinomu, cha kumpoto kwake kwa chigwa cha Arefaimu. Adapita chakumwera kubzola chigwa cha Hinomu, kumwera kwa chitunda cha Ayebusi, moyang'ana ku Enirogele.
17Tsono malire adakhota, naloŵa kumpoto ku Enisemesi ndi kubzola mpaka kukafika ku Geliloti, kuyang'anana ndi pokwerera pa Aduminu. Atatero malirewo adatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
18Adabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Betaraba, natsikira ku chigwa cha Yordani.
19Adapitiriranso kumpoto kwa chitunda cha Betehogila, ndipo adakathera chakumpoto ku mathiriro a mtsinje wa Yordani m'Nyanja Yakufa, kumwera kwake kwenikweni kwa Yordani.
20Mtsinje wa Yordani ndiye udachita malire kuvuma kwake. Ameneŵa ndiwo anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
21Mizinda ya mabanja a Benjamini inali Yeriko, Betehogila, Emekezizi,
22Betaraba, Zemaraimu, Betele,
23Avimu, Para, Ofura,
24Kefaramoni, Ofini ndi Geba. Yonse inalipo 12, pamodzi ndi midzi yake.
25Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti,
26Mizipa, Kefira, Moza,
27Rekemu, Iripele, Tarala,
28Zela, Haelefe, Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu), Gibea ndi Kiriyati-Yearimu. Yonse inalipo 14, pamodzi ndi midzi yake. Dziko limeneli ndilo limene mabanja a Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.